Zilakolako zathu zimatinamiza

Zilakolako zathu zimatinamiza

Ife tonse tili ndi zilakolako zoipa mu thupi lathu zimene zimatichititsa kuchita uchimo. Kodi tingapulumutsidwe bwanji ku vuto limeneli?

11/17/20253 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Zilakolako zathu zimatinamiza

“Zikhumbokhumbo Zomwe Zimatisocheretsa"

 MtumwiPaulo anatifotokoza kuti ndife anthu amene timanamizidwa mosavuta  ndi ‘’zilakolako zachinyengo’’. ‘’… kuti muvule kunena za makhalidwe oyamba munthu wakale wovunda potsata zilakolako zachinyengo" Aefeso 4:22. Makhalidwe achinyengo ndiwo amene amatisocheretsa. Izi zikutanthauza kuti makhalidwewa amandinyenga ndi kundinamiza.

Pa 2 Petro 1:4. Petro akulankhula za kuthaŵa “chivundi chimene chili m’dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zauchimo.” Ichi ndi chowonadi chomwe anthu ambiri sachidziwa. Mavuto onse, kusakondwa konse, kupsinjika konse  kusowa mtendere konse, makangano onse zimachokera pofuna kutsatira zilakolako zauchimo. “Zichokera kuti nkhondo,zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu? Yakobo 4:1.

‘’Koma Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero mu msampha ndi m'zilakolako zambiri ndi zopweteka zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitaiko 1 Timoteo 6:9.Tchimo limatichititsa ife kukhala opusa ndipo zotsatira zake limationonga.

Kodi Ine ndimakhulupirira chiyani

Ndime za Baibulo zotsatirazi zikusonyeza bwino lomwe kuti tiyenera kusankha pakati pa zilakolako zathu zauchimo ndi chifuniro cha Mulungu:

‘’Kuti nthawi yotsalita simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsats zilakolako za anthu,koma chifuniro Cha Mulungu.1Petro 4:2.

‘Ndipo dziko lapansi likupita ndi zilakolako zake, koma iye amene achita chifunilo cha Mulungu akhala ku nthawi zonse 1 Yohane 2:17 

Ku Atesalonika, Paulo adawalembera kuti Mulungu adawasankha "Kuti alandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi" 2 Atesalonika 2:13. Popanda chikhulupiriro m'cboonadi palibe chipulumutso ndipo sitingayeretsedwe. Kodi nanga choonadi tikuchiwrengachi nchiyani?

Yakobo analemba kuti ‘’Munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo.’’ Yakobo 1:14. Chotero ndiyenera kuona ndi kuvomereza kuti pali zilakolako zauchimo mu umunthu wanga zimene zimayesa kundikokera kutali ndi kundinyengerera kuti ndichite chinthu chimene sichili bwino kwa ine. Ngati ndilola kuti ndinyengedwe ndi uchimo mu umunthu wanga, ndiye kuti ndimakhulupirira bodza. Ndikhoza kupeza chipulumutso, ndipo ndingathe kukhala woyera ngati ndikhulupirira choonadi - osati bodza.

Kukonzekera nkhondo mwanzeru

Pa 2 Atesalonika 2:13 timawerenga kuti timapulumutsidwa mwa chikhulupiriro m’choonadi. Choncho ndikayesedwa, ndimayenera kudziweruza kuti: “Chinthu chimene ndikuyesedwa nacho  panopa chikundiuza kuti ndikachipeza kapena kuchichita chindipatsa chisangalalo" Koma ili ndi bodza! Zoona zake n’zakuti m’malo mondithandiza, uchimo udzandiwononga. Zoterezi zimandichotsera chimwemwe changa chonse. Zimandipusitsa ndi kundipatsa maganizo oipa. Mwa njira ina ndikuyenera kutsutsana ndi zomwe zikhumbo zanga zoipa zikuyesera kundiuza.

Zilakolako zathu zimatinamiza! Tangoganizani mmene zingakhalire zomvetsa chisoni ndikaganizira za moyo wanga n’kuona kuti ndanamizidwa!

Paulo ananena ku Agalatiya 5:24 "Koma Iwo a Khirisitu Yesu anapachika pamtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zake ndi zolakalaka zake’’ Ichi ndicho chikhulupiriro, pomwe ndimasankha mokhazikika komanso kutha kuzindikira kuti zilakolako zanga zauchimo ndi zabodza. Chifukwa chake, ndikhoza kunena kuti Ayi ku bodza! Ayi kukunyengedwa! Ayi ku zomwe zingandipweteka ine! Sindidzamveranso bodza, koma chowonadi chokha!

Izi ndi zinthu zanzeru zotithandiza kumenya nkhondo ndikutitsogolera kugonjetsa zoipa ndikukula mu zabwino.

Nkhaniyi idachokera ku nkhani ya Øyvind Johnsen yomwe idasindikizidwa koyamba pa https://activechristianity.org/ ndipo idasinthidwa ndi chilolezo kuti igwiritsidwe ntchito patsamba lino.

Tumizani