Zilakolako zachinyamata: Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kuyesedwa ndi kuchimwa?

Zilakolako zachinyamata: Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kuyesedwa ndi kuchimwa?

Pali kusiyana kwakukulu. Ndipo n'kofunika kwambiri kudziwa kusiyana kwake.

11/17/20256 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Zilakolako zachinyamata: Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kuyesedwa ndi kuchimwa?

Thaŵani zilakolako zaunyamata!

Nkofunika kwambiri kuti timvetsetse kuti kuyesedwa sikofanana ndi kuchimwa. Makamaka pamene ndi za moyo wanu wa mmaganizo ndi zilakolako zaunyamata. Ndimachimwa ndigonja ku mayesero - osati ndisanagonje.

"Thawani zilakolako zaunyamata!" ndi zimene mtumwi Paulo akuuza mnyamata Timoteo. (2 Timoteyo 2:22.) Zilakolako zaunyamata zimakhuza mbali zambiri zosiyanasiyana m'moyo wa wachinyamata, koma kwenikweni zilakolako zimakula mphamvu kwambiri ku gawo la chilakolako chogonana. Chikhumbo chachibadwa chimenechi sichiri tchimo mwa icho chokha ndipo chiri m’dalitso umene Mulungu wapereka mkati mwa moyo wa pa banja, koma Baibulo limanenetsa bwino lomwe kuti kugonjera ku zilakolako zogonana zimenezi pamene suli pabanja ndi tchimo, ngakhale m'moyo wathu wa mmalingaliro. Koma chilakolako chimenechi ndi champhamvu kwambiri moti "kuthawa" nthawi zina kumangooneka ngati kosatheka.

Mzere wooneka bwino

Koma mu zimene timamva mthupi lathu, momwe timachitira,  ndi zilakolako zonyansa zomwe Baibulo limatcha "zilakolako zachinyamata", pali malire omveka bwino pakati pa kuyesedwa ndi kuchita tchimo. Ngati mukulimbana ndi kufuna kogonjetsa zilakolako ndi zimene mumamva mmatupi anu, ndiye kuti ndikofunikira kwambiri kuti mudziwe kuti kuyesedwa sikuli kofanana ndi kuchimwa.

Mwina mpaka pano, simunadziwe kusiyana pakati pa mayesero ndi uchimo. Anthu ambiri amaganiza kuti achimwa akayesedwa. Ndipo dziwani kuti mdyerekezi amapezerapo mwayi pa zimenezi. Adzakuimbani mlandu wochimwa nthawi iliyonse mukaona mnyamata kapena mtsikana wokongola. Iye akukuuzani kuti mwachimwa kale nthawi yomwe mumayang'ana chinachake kapena munthu wina, kapena nthawi yomwe lingaliro linabwera m'mutu mwanu. Iye akuyesa kuchotsa kulimbika kwanu kwa kumenya nkhondo yolimbana ndi zilakolako zaunyamata zimenezi! Pakuti ngati mukuganiza kuti "mwachimwa" kale, n'chifukwa chiyani mukufunabe kumenya nkhondo?

M'moyo wathu wonse tikhala tikukumana ndi mayesero. Koma mayeserowa amakhala tchimo pokhapokha ngati tagonjera ndi kuchita mayeserowo. Ndipo ngati timvetsetsa zimenezo, ndiye kuti tikuyenera kulimbana ndi mayesero ndikuwagonja, tikatero ndiye kuti tiyamba kukhala ndi moyo wogonjetsa.

"Ndipo Iye anapanga inu amoyo ..."

"Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolkwa,  dni zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi a maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire monganso otsalawo.  Aefeso 2:1-3.

Anakupatsani moyo; kumasulira kwina akuti, "Ndipo inu Iye anakupangani kukhala amoyo". Ichi ndi chisomo chochokera kwa Mulungu wosamala ndi wachikondi! Machimo anu samakhululukidwa kokha, komanso kukhala ndi moyo kumatanthauza kuti Mulungu Mwini wafikira ndi kukudziŵitsani za maitanidwe anu  akumwamba! Izi sizikutanthauza kuti chikhalidwe chanu chaumunthu chochimwa chachoka, kapena kuti zilakolako zanu zachibadwa zatha mpaka mutakwatira ayi. Koma tsopano mukudziŵa kuti machimo amene munamangidwa nawo onse amayamba monga mayesero. Ndipo mayesero ndi chinthu chimene mungathe kukana ndi kugonjetsa.

Pa Yakobo 1:14 pamati, "Koma timayesedwa pamene tikokedwa ndi kugwidwa ndi zilakolako zathu zoipa." Zimamveka zoopsa, si choncho? Kukokedwa kutali ndi kugwidwa pafupifupi kumamveka ngati mwachimwa kale. Koma ndi mayesero chabe, mukayang'ana zomwe zadzadza  muchikhalidwe chanu chaumunthu chokonda kuchita zoipa. Ndipo, chofunika kwambiri, ndi mwayi kwa inu woti mutha kugonjetsa!

Kodi mumadzilola kuwonera ndi kuŵerenga ndi kumvetsera chiyani?

Ngati mukufuna kusiya zilakolako zaunyamata, muyenera kuzitenga mosamala kwambiri, makamaka ngati ndi chinthu chomwe mukudziwa kuti mwakhala mukugonjera ku icho kwa nthawi yaitali.

Mukakhala wotembenuka moona mtima komanso ndi mtima wonse kwa Mulungu, muyenera kuganiziradi zimene mungalole kuti muzionera, kuwerenga ndi kumvetsera. Mwina mungafunse kuti, "Koma kodi ndilibe ufulu woonera zimene ndimakonda?" Yankho losavuta ndi lakuti: "Ayi!" Mukhoza kupeza mtendere m'dera lii la zilakolako zaunyamata ngati muutenga mosamala kwambiri, ndipo zimenezo zikutanthauza kuthawa zilakolakozi, ndikulimbana molimbika kuti musazigonjere!

Pakukhala wodzichepetsa mokwanira ndi kuima nji osatekeseka pa gawo limeneli,  simukumuonetsa Mulungu kokha kuti mukuzitenga mosamala kwambiri, koma kuti inunso mukudzipulumutsa ku mayesero ochuluka kwambiri!

kodi ndi liti pamene mayesero amakhala tchimo?

Choncho ngati simukuonera mafilimu odetsedwa, mwachitsanzo, mumapewa mayesero omwe angabwere chifukwa choonera mafilimu odzaza ndi chidetso. Koma bwanji ngati mwangozi muwona chinachake chodetsedwa, monga kutsatsa malonda kodetsedwa?

Yesu ananena momveka bwino kuti: "Ngati wina ayang'ana mkazi n'kufuna kugonana naye, m'maganizo mwake wachita kale tchimo limenelo ndi mkaziyo." Mateyu 5:27-28. Yesu sakunena kuti, "Aliyense amene akuona mkazi..." Kufuna kugonana ndi munthu wina ndi chisankho chomwe chimachitika, ngati mutayang'ana mkazi ndi cholinga chimenecho, ndiye kuti mwachimwa kale mumtima mwanu, ndipo ili ndi gawo loyamba lochitira mwakuthupi. Ngakhale ngati simufika mpaka pochita zimenezo mwakuthupi, kugonjera ku zilakolako zimenezi m'maganizo mwanu kukukulepheretsani kukhala wophunzira weniweni. Kuti mukhale wophunzira muyenera kukhala ndi mtima wosagawanika!

Koma kodi muyenera kuchitanji pamene muwona mwangozi chinthu chodetsedwa?

Mwachitsanzo, ngati mwangozi mukuona malonda odetsedwa, ndiye kuti muli ndi chisankho choti muchite! Ngati mumvera mawu a Yesu, ndikuyang’ana kumbali osafuna kuona kusatsidwa kwa malondawo, simunachimwe! Izi sizidzakhala zophweka, chifukwa zilakolako zanu kwenikweni zimafuna kuti mupitirize kuyang'ana.

Koma simuyenera kuchita nokha. Mulungu adzatumiza Mzimu Wake kuti akupatseni mphamvu kuti mugonjetse m'mayesero, kuti musapereke chilakolako chimenecho, monga momwe chalembedwera pa Agalatiya 5:17, "... kuti musachite zinthu zimene mukufuna."

Ndi kudzera m'mayesero a tsiku ndi tsiku ngati amenewa amene amatithandiza kumvetsa chifukwa chake Yesu anayenera kupemphera mosweka kwa Mulungu ndi mtima wonse, ndipo mudzapeza kuti mukuchita zomwezo. (Ahebri 5:7-8.) Mapemphero pakati pa "nkhondo" si nthawi zonse amakhala mawu oganiza mosamala. "Wokondedwa Mulungu, sindikufuna kuchimwa! Sindikufuna kuchimwa!" kungakhale kulira kotheratu kwa mtima wanu kumene mumabwereza kufikira mutazindikira kuti nkhondoyo yatha ndipo mayeserowo atha mphamvu yake. Koma ndi pemphero ndithu mogwirizana ndi mtima wa Mulungu!

Kunena kuti Ayi mukangoona kuti mukuyesedwa

Kunena mwamphamvu Ayi mukangozindikira kuti mukuyesedwa ndikofunikira kwambiri, kuopa kuti ikhoza kukula mosavuta ndikukhala tchimo "lachinsinsi" lomwe umalola kukula mumtima wanu.

Mukakhala tcheru kwambiri komanso kuopa Mulungu, m'pamenenso mudzachitapo kanthu mofulumira poyesedwa. Mudzakhala mmodzi wa iwo "amene nzeru zawo zimaphunzitsidwa ndi machitidwe kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa." Ahebri 5:14.

Koma anthu amene "amatsatira njira za dziko lino" kumbali ina, ali ndi "malingaliro awo ophunzitsidwa" mmene angaperekedi ku "zilakolako za thupi ndi za maganizo". (Aefeso 2:1-3.) Mukhoza kuona bwino zimenezi m'njira imene mwamuna kapena mkazi angatsatire munthu wokongola ndi maso ake. Mu mkhalidwe ngati uwu, inu monga wophunzira wa Yesu Khristu, muyenera kumenya nkhondo yolimbana ndi chidwi chodetsedwa chomwe mukuyesedwa ndikuchiphwanya mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Anthu amene amadziŵa za kufooka kwawo ndipo ali odzichepetsa mokwanira kupeŵa kudziika mmayesero osafunikira ali ndi mkhalidwe wolungama wa mumtima. Mulungu amapatsa anthu oterowo chisomo, osati kungoona kusiyana pakati pa mayesero ndi uchimo, komanso chisomo kuti apambane pa nkhondo yawo yolimbana ndi zilakolako zaunyamata – zilakolako zomwe ndi gwero la chisoni chachikulu ndi chimene anthu ambiri ali akapolo, kuyambira kalekale nthawi yawo yaunyamata

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhaniyi yachokera ku nkhani ya David Risa yomwe idasindikizidwa poyamba pa https://activechristianity.org/ ndipo yasinthidwa ndi chilolezo chogwiritsira ntchito pa webusaitiyi.