Kugonjetsa tchimo: Cholinga cha Mulungu kwa ife!
Baibulo limalonjeza momveka bwino ophunzira onse okhulupirika a Yesu kuti adzagonjetsa uchimo. Mulungu amafuna kuti tisiye uchimo kotheratu. Ngakhale kuti uthenga wabwino ndi womveka bwino, nthawi zambiri umamvedwa molakwika kapena kapena kuunyalanyaza kumene. M'munsimu muli mavesi ochepa omveka bwino omwe amatsimikizira popanda kukayikira kuti chifuniro cha Mulungu kwa ife ndi chiyani - ndipo ndikuti tchimo lisakhalanso ndi mphamvu iliyonse pa ife!
Mateyu 5:48:
"Muyenera kukhala wangwiro-monga Atate wanu wakumwamba ali wangwiro."
Aroma 6:12-14:
"N;chifukwa chake, musaloletchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. Musapereke ziwalo za thupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo za zamakhalidwe oyipa. Mmalo mwake mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo za thupi lanu ngati zipangizo za chilungamo, Tchimo silizakhalanso ndi mphamvu pa inu, chikukwa malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo."
Aroma 8:12-13:
"Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe la uchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa za thupi, mudzakhala ndi moyo.”
1 Akorinto 15:34:
"Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi."
2 Akorinto 2:14:
"Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambanano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino."
Akolose 3:5:
“Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano."
Ahebri 2:17-18:
"Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala ofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wa chifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu. Popeza iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwa."
Ahebri 4:15-16:
"Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo cha zofooka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa m’njira zonse monga ife, koma sanachimwe. Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando wa ufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni."
1 Petro 2:21-22:
"Munaitanidwa kudzachita zimenezi, chikukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire m’mapazi ake. Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza'"
1 Petro 4:1-2:
"Popeza kuti Khristu anamva zowawa mthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mthupi lake walekana nawo uchimo. Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulung.u"
2 Petro 1:10 :
"N’chifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi simudzagwa konse."
1 Yohane 3:3:
"Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera."
1 Yohane 3:6-7:
"Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa. Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi olungama, monga Khristu ali wolungama."
Chivumbulutso 3:21:
"Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambanandi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu."