Mwinamwake mwakumana ndi kuti zinthu nthawi zambiri zayenda moipa - mwagwera mu uchimo mobwerezabwereza ndipo zikuwoneka ngati palibe kupita patsogolo. Mwayesa zonse, koma palibe chomwe chimagwira ntchito. Mukamva mawu a Mulungu akulankhulidwa mwamphamvu komanso odzaza ndi Mzimu Woyera, mumapezanso chiyembekezo, koma chiyembekezo chanu chimatha mwamsanga mutabwerera m'moyo wanu wa tsiku ndi tsiku.
Ndipotu, zinthu zakhala zikuyenda mmwamba ndi pansi ngati izi kwa nthawi yayitali kwambiri, kotero mwayamba kuganiza kuti mwina zidzangopitiriza mofanana kwa moyo wanu wonse. Zokumana nazo zanu zonse zimakuuzani kuti sizidzapambana konse kwa inu kuleka kuchimwa!
Mukufuna chikhulupiriro
Chifukwa chake mufunikira chikhulupiriro!
Chikhulupiriro chimatsutsana ndi kumvetsetsa kwathu kwaumunthu. Ku malingaliro athu aumunthu, chikhulupiriro sichiri "chanzeru" konse. Ndicho chifukwa chake ndi chikhulupiriro. Chikhulupiriro chimatanthauza kugwirisungira Mawu a Mulungu ndi malonjezo Ake! Mofanana ndi mawu a pa Afilipi 1:6 pamene timawerenga kuti: "Ndipo ndikutsimikiza kuti Mulungu, amene anayamba ntchito yabwino mkati mwa inu, adzapitiriza ntchito yake kufikira itatha pa tsiku limene Khristu Yesu adzabweranso." Chikhulupiriro chimatanthauza kukhala wogontha ndi wakhungu ku malingaliro onse a kusakhulupirira. Chikhulupiriro ndi khoma lalitali pakati pa zochitika zakale ndi lero.
Mwinamwake mwayesa kale kupeza chikhulupiriro chakuti mudzatha kugonjetsa uchimo wonse, ndipo mwinamwake mwataya chikhulupiriro chimenecho kachiŵirinso. Koma muyenera kuyesa mobwerezabwereza! Kuti mupeze chikhulupiriro muyenera kupempha Mulungu ndipo kenako muyenera kusankha kukhulupirira zimene Iye akunena m'Mawu Ake. Pamenepo muyenera kugwiritsitsa chikhulupiriro chimenechi tsiku lililonse. Iwalani zomwe zili kumbuyo, ndikulimbana kuti mugonjetse. Gwirani chikhulupiriro! Yembekeza! Tsiku ndi tsiku, ndipo musadandaule za mawa!
Ngati mugwiritsitsa zimenezi, tsiku lidzafika posachedwapa pamene muyang'ana kumbuyo ndi kupeza kuti mukukhala ndi moyo wogonjetsa ndi kuti kwakhala kosavuta ndi kwachibadwa kugonjetsa tsiku lililonse.
Palibe chifukwa chosiya
Koma bwanji ngati pambuyo pake muli ndi tsiku loipa ndi kugwanso? Kodi zonse zili zopanda chiyembekezo tsopano? Kodi zonse zakhala zopanda pake? Kodi tsopano mwabwereranso kukakhala m'uchimo? Kodi tsopano muli ndi chifukwa cholefulidwa ndi kusiya?
Ayi! Khulupirirani kuti Mulungu adzakhululukira machimo anu! Musakhale pansi kwa kamphindi kamodzi, koma kudumphanso, kukhulupirira zimene Mulungu walonjeza, ndi kuzigwira! Pa 2 Timoteyo 1:7 panalembedwa kuti Mulungu sanatipatse mzimu wolefula, choncho simuyenera kukhala mumzimu umenewo! Gwiritsani ntchito kugwa kwanu ngati chifukwa chodana ndi tchimo ngakhale kwambiri - kuti mukhale okonzeka bwino nthawi yotsatira! N'kwachibadwa kwambiri kugwa kwa munthu amene akuphunzira kuyenda, koma siziyenera kukhala choncho!
Nkofunika kwambiri kuti musataye mtima! Zidzapambana!