Anthu ambiri amakayikira. Ndiye n'chifukwa chiyani Mulungu sandipangitsa kukhulupirira mosavuta? N'chifukwa chiyani Iye samangolankhula kuchokera ku mitambo ndi kudziwonetsa yekha kwa ine?
Kukayikira kumabwera mu mawonekedwe osiyansiyana. "Kodi Mulungu amafunadi kuti ndichite chiyani ndi moyo wanga?" "N'chifukwa chiyani Iye amalola matenda ndi ngozi kuchitika?" ndi "N'chifukwa chiyani Ine ndimaona ngati ali kutali kwambiri?"
N'chifukwa chiyani kukhulupirira n'kovuta?
Mulungu ndi wodabwitsa. Analenga chilengedwe chonse. Analenganso munthu aliyense mwachikondi. Mphamvu zake n'zosatha. Koma maganizo anga ndi amene amachititsa kuti kukhulupirira Mulungu kukhale kovuta kwambiri. Njira ndi malingaliro a Mulungu sangamvetsetsedwe ndi maganizo anga aumunthu.
Mulungu samandisankhira, Iye amandilola ndekha kusankha ngati ndikufuna kumukhulupirira Iye kapena ayi. Iye amandipatsa ufulu kusankha kukhulupirira Iye ndi kukonda Iye pachikondi chomwe amandionetsera.
Mulungu amafuna kukhala pafupi nane ndipo amafuna kuti ndikhale ngati Iye. (2 Petro 1:4.) Zonse zimene Mulungu ali ndi zomwe amachita ndi zabwino (Salmo 119:68), koma chifukwa cha uchimo, pali mtunda waukulu pakati pa Mulungu ndi ine, zomwe zimandipangitsa kukhala wovuta kukhulupirira kuti ndikhoza kukhala ngati Iye. Mulungu akufuna kundipatsa chigonjetso pa tchimo langa, limene liri magwero a kupanda chimwemwe konse ndi kuvutika, ndipo pamapeto pake Iye akufuna kumasula dziko lonse lapansi ku uchimo.
Mu zonse zimene Mulungu amalola kuti zichitike, Iye akuyesetsa kutibweretsa pafupi ndi Iye, kudzera mu nyengo yomwe ikuwoneka yopanda pake kapena ngakhale yomvetsa chisoni.
N'chifukwa chiyani ndiyenera kukhulupirira Mulungu?
Mulungu ali ndi dongosolo lenileni komanso tsogolo labwino kwa munthu aliyense amene amakhulupirira Iye, mosasamala kanthu kuti ndine ndani kapena kuti ndimachokera kuti. Ndipotu, Mulungu wapereka kuthekera kuti aliyense, kulikonse, angakhulupirire mwa Iye ndi kumudziwa Iye payekha.
Zolinga za Mulungu n'zazikulu kwambiri kuposa zimene ndingaganize. Monga mbali ya dongosolo lake, Iye anatumiza Mwana Wake, Yesu, kukakhala padziko lapansi, ndipo Iye anampatsa Mzimu Wake Woyera. Yesu anali ndi chilengedwe monga ine, koma mwa kumvera Mzimu wa Mulungu nthaŵi zonse, Iye sanachimwepo. Tsopano n'zotheka kuti ndipeze thandizo lomwelo kuchokera kwa Mzimu Woyera kuti ndisiye kuchimwa. Mwa kukhulupirira Mulungu ndi kumvera Mzimu Wake, ndikhoza kumasulidwa ku mtolo wolemera wa kulephera kusiya kuchimwa, ku "kuchimwa ndi kupempha chikhululukiro" mobwerezabwereza.
Ndikufuna mzimu woyera wa Mulungu kukhulupirira ndi kumvetsa zimene Mulungu, m'chikondi Chake, wandikonzera. Mulungu ndi Bwenzi limene limandipatsa mphamvu zochita zimene sizingatheke pandekha.
Kodi ndimakhulupirira bwanji?
Kukhulupirira ndi chisankho chimene ndimapanga, sikumverera. Ndipo ndiyenera kuchitapo kanthu. Njira yoyamba ndiyo kupempha Mulungu kuti andikhululukire ndi kundipatsa chikhumbo chenicheni cha kuleka kuchita zinthu zimene ndikudziŵa kuti nzochimwa ndi zoipa.
Ndikufuna Mzimu Woyera wa Mulungu kuti ndikhale ndi mphamvu zosiya kuchita zinthu zauchimo. Kuti ndilandire Mzimu Wake, ndiyenera kupemphera kwa Iye ndi kuwerenga mawu a Mulungu, ndi kuyamba kuchita zinthu zimene ndimawerenga. Ndiyenera kumvera zimene ndimawerenga m'Baibulo. Mulungu amapereka Mzimu Wake kwa iwo amene amamumvera (Machitidwe 5:32).
M'Baibulo muli nkhani ya mneneri, Eliya, amene anapemphera kwa Mulungu ndi kuyembekezera yankho. Choyamba, chivomezi chinadza ndipo kenaka moto, koma Mulungu sanayankhe Eliya mwa izi. Pambuyo pake Mulungu analankhula ndi mawu a kamphepo kayaziyazi (1 Mafumu 19:12.) Lero Mulungu akulankhula nafe kudzera mwa Mzimu Wake m'njira yabata monga momwe anachitira kwa Eliya.
Kuti ndimve Mzimu wa Mulungu tsiku lililonse ndikuyenera kukhala ndi chidwi kuposa zomwe zili pa Tsamba lamchezo, zomwe anzanga akuganiza za ine, ndi ntchito yanga. Ndiyenera kukonda Mulungu ndipo ndikufuna kukhala ngati Iye. Ndiyenera kukhala ndi chidwi ndi zomwe Iye akunena.
Ndikalandira Mzimu Wake, ndimayamba kulandira "zikumbutso" zabata mmalingaliroa anga. Ndimakumbutsidwa za zinthu zimene ndingachite bwino, ndipo potero mapemphero anga akuyankhidwa.
Mwinamwake ndikadzuka ndikumva kukhala woipa. Mzimu umandikumbutsa kuti kukwiya ndi kunyinyirikaa ndi tchimo. Ndimapempha thandizo kwa Mulungu kuti ndisakwiye. Mothandizidwa ndi Mzimu Wake, ndimatha kusankha kuti ndisakwiye ngakhale kuti mwina ndimamva choncho.
Mwina ndimapempherera munthu amene ndimamuganizira. Ndimakumana nawo tsiku lomwelo ndikupeza mwayi wonena chinachake chabwino kwa iwo. Ndikakhala ndi Mzimu Wake, ndimalandira mayankho a mapemphero anga ndipo ndimaona Mulungu m'zochitika za tsiku ndi tsiku.
Nthawi zina tikhoza kumamva ngati Mulungu ali kutali nafe i, koma Iye nthawi zonse amakhala nafe pafupi. (Machitidwe 17:24-27; Salmo 139:7-10.) Ndikhoza kupemphera ndi kukhulupirira Mulungu mwachidaliro kuti andithandize ngakhale kuti sindikumva kukhala wodzala ndi chikhulupiriro. (Masalimo 145:18.)
Mwina sindingaone mayankho pa mapemphero anga mofulumira monga momwe ndikufunira koma adzabwera! Kutsika kwa madzi m'kupita kwa nthaŵi kungaseme mwala wolimba, osati mwa mphamvu y koma mwa kusaima. Yesu amatha kupulumutsa kwathunthu anthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iye. (Ahebri 7:25.)
Mulungu salankhula nane kuchokera ku mitambo mwachindunji. Iye akufuna ine ndisankhe kukhulupirira Mwa Iye ndi KUCHITA chinachake kuchokera kumbali yanga. Pamene ine kusankha kukhulupirira ndi kumvera Mulungu ndiye tsogolo langa ndi lowala ndi lodzala ndi malonjezo ake!