Pamene mzimu wa chikhulupiriro unalowa mumtima mwanga, maganizo anga pa moyo asintha n'kuyamba kuwona zinthu moyenera
Moyo wa Chikirisitu Wochitachita
Kodi muli ndi chiyembekezo cha moyo wosatha? Kodi mungakhale ndi moyo umene umatsogolera ku moyo wosatha m'nthaŵi yanu pano padziko lapansi?
Kodi mumakhulupiriradi ubwino ndi mphamvu za Mulungu? Kapena kodi mukuganiza kuti Mulungu ndi wofooka ngati inuyo?
Tonse tikudziwa kuti nthawi imene tili padziko lapansi ndi yochepa. Kodi tidzakhala titapindula chiyani panthaŵiyo?
Pali nkhondo yoti timenye, nkhondo yolimbana ndi uchimo, umene ulu muzu wa mazunzo onse.
Ndi mwa chikhulupiriro mwa Mulungu kuti tifika ku tsogolo limene Iye watikonzera.
Ndaona kuti Mulungu wathu ndi wamkulu kwambiri, komanso kuti m'Mawu a Mulungu muli machiritso ndi thandizo lalikulu bwanji.