Samueli: Tingamve bwanji mawu a Mulungu

Samueli: Tingamve bwanji mawu a Mulungu

Mulungu anapeza m’tima woyera mwa Samueli

10/7/20234 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Samueli: Tingamve bwanji mawu a Mulungu

Wansembe wamkulu Eli anali atakalamba kale pamene Samueli ,m’nyamata wamng’ono , anapita kukakhala ndi kutumikira naye mu kachisi. Ana a Eli ndi amene amayenera kulandilra udindo okhala wansembe wamkulu Eli akamwalira, koma iwo analibe chidwi chopembedza Mulungu. Wawo unali uchimo ndipo iwo samawonetsa ulemu ku malamulo a Mulungu,ndipo Eli analibe mphamvu komanso kufuna kuwalanga anawo chifukwa cha machimo awo. (1 Samueli 2:12-17). Zotsatira zake, Mulungu samayankhulana ndi Eli ngati m’mene amayankhulirana ndi anthu ena monga Mose. 

Samueli atabwera kudzakhala kukachisi, Mulungu ankamuyang’anitsitsa. Mayi ake a Samueli analonjeza kuti adzabweretsa Samueli kukachisi kuti azitumikira Mulungu kuyambira ali mwana. Mulungu anakumbukira zimenezi ndipo ankangoyembekezera nthawi yoyenera kuti alankhule ndi Samueli m’njira imene sakanatha kuchita ndi Eli ndi ana ake. 

Mulungu anapeza mtima woyera mwa Samueli 

Kodi n’chiyani chinachititsa mnyamatayu kukhala wapadera kwambiri moti Mulungu anafuna kulankhula naye? Zalembedwa kuti Ambuye sanalankhule kawirikawiri kwa anthu m’masiku amenewo, ndipo panalibe masomphenya ambiri. (1 Samueli 3:1) Mulungu anachenjeza Eli kuti banja lake lidzawonongedwa, ndipo anati: “Ndasankha munthu wina kuti akhale wansembe wanga, amene adzakhala wokhulupirika ndi kundimvera. Nthawi zonse ndidzalola banja lake kukhala ansembe ndi kuthandiza mfumu yanga yosankhidwa.” (1 Samueli 2:35) Iye amafunafuna munthu wamtima woyera ndipo anupeza mwa Samueli. 

Pamene Mulungu anamuitana usiku wina, Samueli anaganiza kuti anali Eli. Anali atazolowera kumvera, choncho anadzuka nthawi yomweyo. Izi zinachitika katatu, ndipo Eli anazindikira kuti Mulungu ankafuna kulankhula ndi mnyamatayo. Choncho anauza Samueli kuti atamvanso mawuwo ayenera kuyankha kuti: “Lankhulani Yehova, ine mtumiki wanu ndikumvetsera.” (1 Samueli 3) 

Nthawi zambiri ndimaganizira za Samuel ndi yankho lake losavuta. Ndinalingalira za kufunika kokhala maso ndi kumvetsera pamene Mulungu akuyesera kulankhula nane. M’nthawi ya Samueli, Mulungu analankhula ndi aneneri ndi ansembe, ndipo iwo anapita kukalankhula ndi anthu. Koma tsopano Mulungu akhoza kulankhula nafe mwachindunji kudzera mwa Mzimu wake Woyera. 

Malamulo ndi nzeru za Mulungu zimapezeka m’Baibulo. Mwachitsanzo, palemba la Yohane 14:21  akuti: “Iwo amene akudziwa malamulo anga ndi kuwasunga, ndi amene amandikonda, ndipo Atate wanga adzakonda amene amandikonda. Ndidzawakonda ndipo ndidzadzisonyeza kwa iwo.” Choncho, ngati nditadziwa Mawu a Mulungu ndikuwatsatira, ndidzalandira Mzimu Woyera. Ndiye, ngati ndipitiriza kukhala wokhulupirika, ndidzaphunzira kumva mawu amenewa mumtima mwanga mowonjezereka ndipo anganditsogolere pa moyo wanga wa tsiku ndi tsiku. 

Ubale wa pamtima ndi Mulungu 

Pamene Mulungu analankhula ndi Samueli kwa nthawi yoyamba, anali ndi nchito yofunika kwambili yakuti Samueli aichite—kuyesa kusonyeza kukhulupirika kwake. Zinalembedwa kuti Samueli ankaopa kuuza Eli zimene Mulungu ananena. (1 Samueli 3:15) Koma Eli anafuna kumva zimenezo, choncho Samueli anamuuza kuti: “Mulungu anali wokonzeka kukwaniritsa lonjezo lake kwa Eli ndi ana ake, ndipo anaika Samueli m’malo mwa Eli monga mneneri wa anthu a mtundu wake. 

Samueli anali ndi mtima woyera, koma Mulungu anafunika kumuyesa pa nthawiyi. Zilinso chimodzimodzi kwa ife. Mulungu amatitumizira ntchito zosonyeza kukhulupirika kwathu. Zitha kuoneka ngati zovuta - mwina Mulungu amafuna kuti tiuze wina zoona, monga Samueli, ngakhale titadziwa kuti winayo sangafune kumva. Koma ngati ndikufuna kutsimikizira kuti ndimakonda Mulungu kuposa china chilichonse, ndiyenera kumvera nthawi yomweyo Mulungu akamalankhula mu mtima mwanga. Ndikamvera mwachangu, zotsatira zake zimakhala zabwino. 

Malo a m’Baibulo amene mneneri Samueli amatchulidwa akusonyeza kuti iye anakhalabe ndi mtima woyera kwa moyo wake wonse, ndipo chifukwa cha zimenezi nthawi zonse ankamva mawu a Mulungu. Pamene ankapempherera anthu, Mulungu ankamvetsera nthawi zonse. 

Ndi uchimo umene umatilekanitsa ndi Mulungu. (Yakobo 4:6) “Mulungu amatsutsana ndi odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” Ngati sitilolera kudzichepetsa pansi pa chifuniro cha Mulungu, kumvera Iye ndi kuwononga mphamvu ya uchimo m’miyoyo yathu, tidzaona kuti tadulidwa ku chisomo cha Mulungu, monga momwe anachitira Eli. Koma ngati tisunga mtima wathu woyera, tingakhalenso paubwenzi wapamtima ndi Mulungu, pamene angalankhule nafe, monga anachitira ndi Samueli. Tikatero tingakhalenso antchito anzake, monga mmene mneneri Samueli analili m’nthawi yake! 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhaniyi idachokera ku nkhani ya Heather Crawford yomwe idasindikizidwa koyamba pa https://activechristianity.org/ ndipo yasinthidwa ndi chilolezo kuti igwiritsidwe ntchito patsamba lino.