Moyo obisika
‘’Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khirisitu,funani zakumwamba.Kumene kuli Khirisitu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.Lingalirani zakumwamba osati zapadziko ai.Pakuti munafa,ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khirisitu mwa Mulungu.’’Akolose 3:1-3
Kukhala pamaso pa Mulungu mu moyo obisika ndi njira yokhayo imene ili ya mtengo wapatali m’moyo uno ndi kwamuyaya.Koma chikhalidwe cha ife anthu chimatiphunzitsa kuyambira tili ana kufuna kukondweretsa anthu,kufuna kukondedwa ndi anthu,kufuna kusangalatsa anthu komanso kufuna kuwoneka wabwino pamaso pa munthu wina aliyense.Umenewu ndi mzimu wa nthawi imene tikukhalamoyi.Koma Yesu ananena kuti zinthu zimene anthu amaganiza kuti ndi zofunika,Mulungu amadana nazo,(Luka 16:15). Zimabweretsa nkhawa zambiri, kudandaula komanso kusowa mtendre. Uwu ndi moyo wovuta kukhala. Ndipo izi zikhoza kukhala chimodzimodzi mu moyo wathu wachikhirisitu.
Musakhale okondweretsa anthu
Anthu amatha kugwiritsa ntchito luso lawo lachibadwidwe, kukondweretsa ena ndikudzipangira mbiri. Koma mphatso ndi maluso achibadwidwe amene Mulungu amatipatsa ayenera kugwiritsila nchito pomutumikila, ndipo m’njila imeneyi amatumikiranso ena chifukwa cha Iye.
Kudzikankhira wekha patsogolo pofuna kukondweretsa anthu sikubweretsa madalitso ochokera kwa Mulungu. Yesu anauza ophunzira ake kuti “inde” wawo akhale “inde” ndipo “ayi” akhale “ayi”. ( Mateyu 5:37 ). Tikakhala pamaso pa Mulungu sitiyenera kudzifotokoza tokha kapena kudzitsimikizira kuti ndife olondola. Tingolola kuti Mulungu asamalire zinthu zonse, monga mmene Yesu anachitira, chifukwa Mulungu amaŵeruzaa mwachilungamo. (1 Petulo 2:23.)
Yesu anati, Samalani! Mukamachita zinthu zabwino musamachita pa maso pa anthu kuti akuoneni. Mat:6:1 Ngati muchita zinthu zabwino kuti anthu akuoneni, mphotho yomwe mungalandire ndi ulemu wa dziko lapansi. Kodi inu mumakhumudwa mukapanda kulandira ulemu womwe you mumaufuna? Mumaona vuto ngati dzina lanu silinatchulidwe kapena anthu sanakuthokozeni? Ngati zinthu zili choncho, ndiye kuti inu mukusamalira za anthu osati za Mulungu.
Monga anthu timadzifananizira mosavuta ndi ena. Paulo analembera Akorinto kuti sayenera kudziona ngati iwo abwino, podzifananiza ndi wina ndi mnzake, chifukwa kumeneko ndi kupusa. ( 2 Akorinto 10:12 ) Izi sizimabweretsa chiyanjano ndi umodzi.
Bwanji osakhala pamaso pa Mulungu ndi kudziyerekeza tokha ndi Mawu a Mulungu ndi kukhala wochita Mawu? (Yakobe 1:21-25 .) Paulo anauza Timoteyo kuti azidziyang’anira n’kumayerekezera moyo wake ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, kuti adzipulumutse yekha ndi amene anamumva. (1 Timoteyo 4:16.)
Yesu analankhula mwamphamvu kwa alembi ndi Afarisi mu Yohane 5:44 kuti: “Mungakhulupirire bwanji? Umakonda kutamandidwa ndi anzako, ndipo sudera nkhawa za chitamando chimene Mulungu yekha angapereke!” Mulungu akufuna kuti tikhale ndi chikhulupiriro mwa Iye ndi kumvera Mau ake.Izi ndi zomwe zimabweretsa moyo ndi madalitso. Zimenezi sizingatheke ngati timafuna kusangalatsa anthu. Popanda chikhulupiriro ichi sikutheka kukondweretsa Mulungu. Mulungu amapereka mphotho kwa amene akufunadi kumpeza. ( Aheberi 11:6 )
Mzimu wa choonadi
Ngati mumangofuna kukondweretsa Mulungu, lekani kuyesa kukondweretsa anthu ndi kulola Mzimu kuti akuphunzitseni momwe mungakhalire pamaso pa Mulungu. Paulo anavomereza kuti panalibe chilichonse chabwino mu umunthu wake, ndipo pamene anafuna kuchita zabwino anapeza kuti choipa chinali pomwepo. (Aroma 7:18-24.)
Ngati tilola mzimu kuweruzadi zimene timachita ndi kulankhula, tidzaona kuti mkati mwathu muli njira zambiri zimene timakhalira pamaso pa anthu osati pamaso pa Mulungu. Kenako tingagwirizane ndi zimene Mzimu amatisonyeza, ndi kupempha Mulungu kuti atithandize kukhala omasuka ku zimenezo kuti mmalo mwake tikhale ndi moyo pamaso pake.
Davide analemba mu Salmo 131:1, “Yehova, mtima wanga sunyada; maso anganso sanyada. Sindimaganizira zinthu zapamwamba kwambiri. Sindidzidetsa nkhawa ndi zinthu zimene zili zofunika kwambiri kwa ine.” Anakhala wodekha ndi wokhutira. Ganizirani zosiya kukhala otanganidwa ndi nkhani za anthu ena ndikukhala opanda nkhawa zimene zimabwera chifukwa cha zimenezi. Yesu amatipatsa moyo wamtendere ndi wokhutitsidwa pa muyeso womwe adatiikira. ( Machitidwe 17:26 ).
Ndizokhudza kudzichepetsa ndekha pamaso pa Mulungu, ndi kuvomereza ndi kumvera choonadi chimene Mzimu amatiuza. Ngati tichita izi tsiku ndi tsiku, tidzalandira zambiri za zipatso za Mzimu, ndipo utumiki wathu kwa ena udzakhala woyera. Tikatero tidzatha kuthandiza anthu moyenera. Mwa kukhala pamaso pa Mulungu kokha, tidzakhaladi achimwemwe ndi odalitsika m’zonse zimene timachita.