“Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anaitanidwa monga mwa cholinga chake.” Aroma 8:28.
Mau akuti “chilichonse.” Apa zikuonekeratu kuti zikutanthauza kuti chilichonse chimene chimachitika mu moyo wathu chimatibweretsera ubwino pamene ife tikonda Mulungu. Apatu palibenso kuchotsera pa lamulo la moyo ili, kuti mwina pa nyengo zovutitsitsa kwambiri kapena lamuloli siligwira ntchito. Ayi, palibenso kuchotsera ku lamulo ili ngati ife tikonda Mulungu.
Ine ndapeza chitonthozo chachikulu mu Mau a Mulungu awa kudzera mu nyengo zowawa ndi mayesero zomwe ndakumana nazo. Nthawi zambiri ndimadziveka ndekha mau awa ndi kudzilimbitsa ndekha mu nyengo zanga zovuta, kuti tikagonjetse nkhawa ndi kudandaula mu moyo wanga.
Kuyesedwa
Nthawi ina yake ndinalephera kulowa m’kalasi kuti ndiphunzire, ndipo mayeso anangotsala mwezi umodzi kuti ndilembe. Ndinayesedwa kwambiri kukudandaula. Ndimadziwa ndekha kuti sindinali okonzekera bwino. Ndimakumbukira nditakhala muchipinda changa, osadziwa choti ndichite. Ndinadzimvera ndekha chisoni chifukwa sindimaona njira yopulumukirapo.
Ndinalibe chimwemwe, mtendere kapena mpumulo. Ndinayesetsa kuwerenga koma zimakanika. Izi zimandipangitsa kukhala odandaula koposa. Ndinakodwa kwambiri mukusautsika kotere kwa masiku angapo.
Ndiye tsiku lina ndinali kunyumba kwa mnzanga, ndipo ndinaona vesi yochokera ku Luka 12:31 itakolekedwa pakhoma: “Koma funafunani ufumu wake; ndipo mudzapatsidwa zonsezi.” Anali ngati kuwala komwe kunawalitsidwa kwa ine. Chinadziwika tsopano kuti ine sindimafunafuna poyamba zinthu zakumwamba, ndisanafune zinthu zapadziko pano. Ndinalolera ndekha kukhala odandaula kaamba ka maphunziro anga, ndipo ichi chinandibera chimwemwe ndi mtendere wanga.
Zoti tichite
Nditazindikira ichi, ndinadziwa kuti ndikuyenera kuchitapo kanthu ndi kufunafuna Ufumu wa Mulungu pamwamba pa zonse. Ndipo tsopano ndinaona kuti Mulungu anandipatsa zonse zomwe ndimadzisowa! Sikuti zinali zoti ndinazindikira zonse za ntchito ya kusukulu, kapena kuti ndinakhoza bwino popanda kulimbikira. Koma ndinali ndi mtendere ndipo ndinakwanitsa kukhala wachindunji pamaphunziro anga.
Ndi chinthu chachilungamo kuchita moyenera ntchito ya kusukulu ndi ntchito zina zonse, koma ukuyenera kudziyang’anira wekha kuti zinthu izi zisakubere mtendere ndi chimwemwe zako.
Kuda nkhawa ndi kudandaula
Chilichonse mu moyo uno chikhoza kukhala chotidetsa nkhawa ndi kutidandaulitsa, ndipo izi zimene zimatipangitsa kutaya chimwemwe ndi mtendere wathu. Komatu uwu simoyo umene Mulungu watiyitanira kuti tkaukhale. Maganizo olemera akudandaula ndi kuda nkhawa amachokera kwa Satana ndipo tikuyenera kuwathamangitsa ndikukhala kutali ndi mitima yathu ngati tifuna kutsata Yesu.
Tikuyenera kuyang’ana ganizo lililonse lomwe likudza m’mutu mwathu ndi kuona komwe likuchokera. Ganizo la nsanje, mwachitsanzo, limapangitsa kukhala osowa mtendere. Umu ndi mmene timadziwira kuti likuchokera kwa Satana ndipo likufuna kutenga mtendere wathu. Pamene ganizo lotere labwera, imeneyo ndiye nthawi yoyenera kulirira kwa Mulungu, ndi kumupempha kuti awononge ganizo lotere lisanakule msinkhu. (Ahebri 4:16). N’kofunikira kwambiri kugonjetsa ganizo lotere pamene tazindikira kuti ndi loipa, ngati sititero likhoza kusokoneza kaganizidwe, kaonedwe ndi moyo wam’malingaliro wathu.
Mwa kulankhula kwina, tikuyenera kusankha kuchita chifuniro cha Mulungu osati chathu. Ili ndilo tanthauzo la kukonda Mulungu mochitachita monga mau anena ku Aroma 8:28. Zikatere, sitisamala za zotsatira za nyengoyo, koma zimakatha potichitira ubwino - zimakatisendeza chifupi ndi cholinga cha Mulungu cha paife padziko pano.
Chikondi cha pa Mulungu
Vesi iyi ya ku Luka 12:31 ndi thandizo kwa iwo amene ali ndi chikondi choyaka moto cha pa Mulungu ndipo akufunitsitsa kugonjetsa uchimo. Cholinga cha Iye pa ife padziko pano ndi chakuti tikafanane ndi Yesu. (Aroma 8:29). Izi zikutanthauza kuti tikalandire m’pumulo, mtendere ndi chimwemwe chochuluka, koma izi zikatheka ngati ife tinena kuti AYI kumaganizo aliwonse wodandaula ndi kudera nkhawa.
Zinthu zambiri zimatha kumaoneka ngati zovuta, ndipo zimaoneka kuti pali zifukwa zokwanira zoti tikakhale wodandaula ndi woda nkhawa. Koma Mulungu sanatiyitane ife kuti tikakhale anthu aulesi omangoyembekezera Mulungu kuti atipatse zosowa zathu zonse ife titangokhala osachitapo kanthu. Izi sizowona ayi; tikuyenera kufunafuna ufumu Wake pamwamba pa zonse ndi kumukonda Iye ndi chilungamo Chake, ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa ife ndipo zonse zidzatichitira ubwino.
Ndikuyamika Mulungu kaamba ka lonjezo ili ndi choonadi, ndipo ndikulimbikitsa aliyense wowerenga izi kuti ukayesere mu moyo wako. Mulungu ali woona ku Mau Ake!