Kodi mawu oti kumva zowawa m’thupi amatanthauza chiyani?

Kodi mawu oti kumva zowawa m’thupi amatanthauza chiyani?

Mtumwi Petro akulemba kuti, “….iye amene wamva zowawa mthupi lake walekana nawo uchimo.” Koma timamvetsetsa zimene mawuwa amatanthauza mu moyo wathu wa tsiku ndi tsiku?

8/19/202611 mphindi

Written by ActiveChristianity

Kodi mawu oti kumva zowawa m’thupi amatanthauza chiyani?

“Popeza kuti Khristu anamva zowawa m’thupi lake, mukhale nawonso mtima womwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa m’thupi lake walekana nawo uchimo.  Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu.” 1 Petro 4:1-2.     

Kuchokera mu ndime izi, zinthu zitatu zikumveka bwino: 

Kuti ife eni tikuyenera kumva zowawa m’thupi lathu kuti tileke kuchimwa - sikuti anali Khristu yekha amene anamva zowawa kaamba ka ife. 

Kuti ndi njira yokhayo yomva zowawa m’thupi kuti tileke kuchimwa. 

Kuti ndizotheka ndithu kuleka kuchimwa ndi kuyamba kuchita chifuniro cha Mulungu 

Khristu anamva zowawa m’thupi lake 

Pamene Petro analemba kuti “Khristu anamva zowawa m’thupi lake,” samanena zowawa za Khristu monga mwa thupi.  Apa ndi chachidziwikire kuti zowawa zakuthupi pazokha sizingathe  kuthandiza munthu kuti aleke kuchimwa. Izi tikhoza kuziona kuchokera ku zitsanzo zochuluka pa dziko lapansi komanso kuchokera mu mbiri yake.  

Ayi, Khristu anamva zowawa m’thupi lake pamene anabwera pa dziko lapansi ngati munthu, wokhala nalo thupi ndi mwazi monga ife, ndipo anayesedwa mu zinthu zonse monga tilili ife, ndipo Iye sanachimwe! (Afilipi 2:7; Ahebri 2:14; Ahebri 4:15) Ndipo pamene anabadwa, Iye anabadwa ndi umunthu monga ife. Kuchokera mu umunthu wa mwazi ndi thupi Iye anakhala omvera mpaka imfa. (Afilipi 2:8) Ndipo Iye anaphunzira kukhala omvera kuchokera mu zowawa zomwe anakumana nazo, monga timawerenga ku Ahebri 5:8. 

Tikuona zowawa zimenezi pamene Iye anafuulira kwa Atate ake mofuula ndi molira misozi, pamene thukuta lake linagwa monga madontho a magazi, molimbika anamenya nkhondo kuonetsetsa kuti asachimwe mu mayesero omwe amakumana nawo. (Luka 22:41-44; Ahebri 5:7)  Mu zonsezi, Iye chokhumba chake chinali, “Atate…osati chifuniro changa, koma Chanu, chichitike.” 

 Panali nkhondo yaikulu mkati mwake pakumva zowawa zomwe zimachitika mwa Yesu kuti chifuniro cha Mulungu chichitike, osati cha Iye mwini.  Izi ndi zimene mawu amatanthauza pamene akuti Iye anamva zowawa m’thupi lake- kumva zowawa uku sikunali monga mwa thupi, kunali kumva zowawa kochitika mkati mwake pamene anamenya nkhondo kuti asagonjere ku mayesero.  Ndipo zotsatira zake zinali zoti anagonjetsa chifuniro chake, kuti chifuniro cha Atate ake chichitike padziko pano monga chilili kumwamba. (Mateyu 6:10)  

Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa m’malemba.’ ’’ Ahebri 10:7 

Ifenso tikuyenera kumva zowawa m’thupi lathu 

 Tsopano ndi nthawi yathu yakuti timve zowawa m’thupi lathu, kuti tileke kuchimwa.  Yesu nayenso ananena izi poyera pamene amalongosola za iye amene akhoza kukhala ophunzira wake, omutsatira Iye: “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku n’kumanditsata Ine.  Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa.” Luka 9:23-24   

 Timadza mu kumva zowawa za mkati mwathu pamene tikuyesedwa monga Yesu kuti “osati mwa kufuna kwanga, koma kufuna kwanu kuchitike.” Pamenepo ndi pomwe timakapeza kuti thupi lathu, umunthu wathu woipa sufuna kulekana nazo zilakolako ndi zikhumbitso mophweka. (Yakobo 1:14; Agalatiya 5:24). Ndiye, monga Yesu, tikuyenera kulirira thandizo.  Tikuyeneranso kuphunzira kumvera kudzera mu zinthu zomwe timva nazo zowawa ( zomwe timva nazo zowawa m’thupi lathu)  

 Koma chinthu choposa ndi chakuti, chifukwa Yesu anakumana nazo (ndipo Iye sanachimwe), Iye amadziwa ndi kumvetsetsa mayesero ndi zowawa zomwe tikumana nazo. Ndipo chifukwa cha ichi Iye akhoza kutithandiza pamene tikuyesedwa. (Ahebri 2:17-18) “Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.” Ahebri 4:16 

Thandizo lomwe timapeza ndi lakuti Mzimu Woyera amatipatsa mphamvu zakupereka chifuniro chathu ndi kusenza mtanda, zimene mwachidule zimatanthauza kunena kuti “Ayi” kawirikawiri ku chifuniro chathu; ku zilakolako ndi zikhumbitso za m’thupi mwathu, mu m’khalidwe wathu wokonda kuchita zoipa. Pamene tidzikaniza tokha kuzikhumbitso zotere, zimawawa.  Izi ndi zimene zimatanthauza kumva zowawa m’thupi lathu.  Koma pamene tichita izi mukhulupirika, pamene tidzikaniza tokha kugonjera mayesero osataya mtima ndipo osagonja, pang’ono ndi pang’ono timakayamba kuleka kuchimwa mu dera limenelo. 

Zotsatira za kumva zowawa m’thupi 

Chotsatira cha ulemerero pa kumva zowawa m’thupi ndi chimene chalembedwa ku mapeto a ndime. Sitikhalanso ndi moyo potsatira zilakolako ndi zikhumbitso koma timakhala malinga ndi chifuniro cha Mulungu. Sitichitanso zomwe thupi lathu lifuna, zomwe umunthu wathu woipa ufuna, koma timakayenda mu Mzimu.  Ndipo Mzimuyo amakationetsa zimene Mulungu akufuna pa ife, zimene zimatanthauza kulandira chipatso cha Mzimu monga mkhalidwe wathu.  Timayamba kukula mu chikondi, chimwemwe, mtendere, chifatso, kukomamtima, chifundo, kukhulupirika, kudekha, kudziletsa. (Agalatiya 5:16-25) 

 Timakaleka kuchimwa ndipo timalandira m’khalidwe wa Yesu! (2 Petro1:4). Timakakhala ophunzira ake a Yesu, ndipo timamutsatira Iye. Ndipo zikatere, Iye amafuna kuti tikhale abale ake! (2 Petro 1:4) 

Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mu njira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeretsedwa onse ndi a banja limodzi. N’chifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake.” Ahebri 2:10-11 

Kaamba ka lonjezo ndi chiyembekezo cha chimwemwe ichi tikhoza kunena limodzi ndi Atumwi: “Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya  umene ndi wopambana kwambiri.  Motero sitiyang’ana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka.  Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene  sizioneka ndi zamuyaya.” 2 Akorinto 4:17-18 

Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa m’malo aMulungu ndi olowa m’malo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.  Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife.” Aroma 8:17-18 

Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani.  Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera.” 1 Petro 4:12-13 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi inatsindikizidwa pa https://activechristianity.org/ ndipo yakhazikitsa ndi chilolezo kuti igwire ntchito pa tsamba ili.