Udziweruze wekha

Udziweruze wekha

Mulungu amatsutsana ndi udzikuza koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa. Kudziweruza wekha ndi kudzichepetsa wekha ndi chinthu chachikulu kwambiri choyenera kuchita mu moyo uno!

8/19/20269 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Udziweruze wekha

Chilichonse- kuphatikizapo ndi nkhani ya chipulumutso- zimagwira ntchito malinga ndi malamulo. Monga kulili malamulo a zonse kuthupi, kulinso malamulo a uzimu.   

Lamulo lofunika kwambiri pa nkhani ya chipulumutso- kuchokera panthawi imene tinayamba kufikira pa nthawi yoti takhala angwiro- ndi lamulo la kudzichepetsa. Izi zalembedwa mofanana pa 1 Petro 5:5 ndi Yakobo 4:6: “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.” 

Chipulumutso sikungobwera kwa Yesu ndi kukhululukidwa machimo athu kokha ayi, koma kuti pang’ono ndi pang’ono tikupulumutsidwanso ku zizolowezi zathu zonse zoipa ndi kuyamba kulandira mochulukira zipatso za Mzimu m’moyo wathu.  

Lamulo la kudzichepetsa 

Mbali yoyamba ya lamulo la kudzichepetsa limati: “Mulungu amapereka chisomo kwa odzichepetsa.” Ndiye pali mbali yotsutsana nayo : “Mulungu amatsutsanandi odzikuza.” Odzikuza ndi iwo amene amadzimva ndi odziona kuti iwo ndi anzeru.  Ngati suli odzichepetsa komabe kumapempherera chisomo, Mulungu sangamve pemphero lako, chifukwa amatsutsana nawe.  

Sungadzale mbatata ndi kumayembekezera kuti ukolola nkhuyu, zilibe kanthu kuti ukufununitsitsa motani, koma sizingatheke.  Chimodzimodzi, kuti ndizosatheka kulandira chisomo pamene suli odzichepetsa. 

Mau a mphamvu kwambiri omwe tili nawo okamba za kudzichepetsa ndi mau a Yesu: “……ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.” Luka 14:11.  Ine ndimaonjezera, “kaya akufuna kapena ayi.”  Mulungu amakonda anthu oterewa.  Ngakhale atakhala osapemphera kuti akwezedwe, iwo adzakwezedwabe. Umu ndi momwe lili lamulo limeneli.  

Ukadzichepetsa wekha, anthu uposa amaganiza kuti ndiwe chitsiru ndipo anthu anzeru amaganiza kuti ndiwe wa nzeru, koma zilibe kanthu zimene ena akuganiza; iweyo udzakwezedwabe basi. Mukulankhula kwina, kukhala ndi mantha ofuna kudzichepetsa wekha, ndi kumaopa pamene ukudziwa kuti ukufunika kutero, ndikuyamba kuganiza kuti ndi chinthu chosafunika kutero, kunena zoona kumbali ya uzimu ndi chinthu choipitsitsa. 

Muyeso wa pamwamba ndi muyeso wotsikirako wa kudzichepetsa 

Kudziikira wekha kumbuyo ndi chinthu chopusa, ndipo zimatanthauza kukana chipulumutso.  Nthawi zonse tiyenera kufunafuna zabwino kwambiri, ndipo tifunefune za muyeso wapamwamba, zimene ndi kudziweruza tokha ndi kudzichepetsa ku zofuna zathu. Ichi ndi chapatali kwambiri, cha ulemerero oposa, chopindulitsa koposa ndi choyenera kuchita mu nyengo zathu nthawi zonse pa moyo wathu.   

That is what you should love to do and use every opportunity to do it. To humble yourself means you do it of your own will and not just because other people think that you should do it. This alone is first-class. But God is so gracious and merciful, and therefore it can also go well even when it is second-class. Izi ndi zimene ukuyenera kukonda kuchita ndi kugwiritsa mwai uliwonse kuchita zoterezi.  Kukhala odzichepetsa zimatanthauza kuti ukuchita mwa kufuna kwako osati chifukwa choti anthu akuganiza kuti ukuyenera kuchita.  Kuchita motere ndi kwapamwamba zedi.  Koma Mulungu ndi wa chisomo ndi wachifundo, zikhoza kuyendanso bwino ngati uchita motsikirako muyeso.  

Muyeso wotsikirako ukulumikizana ndi kunyazitsidwa.  Ichi ndi chimene Mulungu mwini amachita.  Izi sizikutanthauza kuti munthu akhoza kupulumutsidwa mu njira yotere, koma pali kuthekera. Komabe, pali choti chichitike kuti munthu apezeke kuti wapulumutsidwa kudzera mukunyazitsidwa, ichi ndi chakuti ukhale kuti wavomereza kotheratu kudutsa munyengo yovutayi osati ndi pakamwa pokha koma kuchokera mu m’mtima, ndipo iwenso udzakwezedwa.   

Pali anthu ambiri amene amachimwira anzawo tsiku ndi tsiku ndipo safuna kuvomereza kalikonse- safunsanso chikhululukiro, ndipo sapepesa.  Kwa iwo amaona kuti akungoyenera kudziikira kumbuyo mwa njira iliyonse.  Komatu ukamachita zoterezi, umakhala ukugwira ntchito yolimbana ndi chipulumutso chako chomwe.  

Udziweruze wekha 

Njira yokhayo yakupulumuka ndi pamene ukuvomereza za zinthu mmene zili mwa iwe.  Kulibenso njira ina ayi. Ukuyenera kudzichepetsa wekha; ndipo ukuyenera kuvomereza za mmene zinthu zili mwa iweyo; ukuyenera kudziweruza wekha osati kuweruza ena ayi.  

 Tili ndi mau ofunikira kotheratu okhudza zimenezi pa 1 Akorinto 11: 31-32, “Koma tikamadziyesa tokha sitikaweruzidwanso.  Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.”  

Ndizosavuta.  Ngati udziweruza wekha, iwe sukaweruzidwa.  Sipakhala chifukwa chochitira izi.  Koma ngati sitichita izi, Mulungu ndi wachifundo ndipo Iye amaweruza ndi cholinga chotipatsa mwai wina.  Koma ngati sitivomera chiweruzo chake, kunyazitsidwa kotereku, ndiye kuti adzatitsutsa pamodzi ndi dziko lapansi  

Sungathe kudzichepetsa kotheratu 

Ndiye funso lalikulu kwambiri ndi lakuti ukwanitsa kuvomereza chiweruzocho. Ngati sutero, ndiye kuti utsutsidwa pamodzi ndi dziko lapansi!  Ukhoza kuwerenga zomwe umakonda, koma izi zikutero.  Kulibe chinthu chakuti unadzichepetsa wekha koposa muyeso; koma kulipo kusadzichepetsa mokwanira.  Palibe munthu amene anadzichepetsa moposa muyeso.   

Pamene zinthu sizikuyenda malinga ndi momwe amayembekezera, yankho limakhala limodzi: Vuto ndi kusoweka kwakukulu kwa kuopa Mulungu.  Anthu satenga Mau a Mulungu ndi chidwi chachikulu, koma mauwa akusowekera chidwi chachikulu. 

 Ine ndikufunireni kupambana kwakukulu ndi mafuno abwino a tsogolo la ulemerero ndi chipulumutso chenicheni! Ndi Mulungu yekha amene amapereka chisomo cha izi.  Iye amakonda kupereka chisomo cha zimenezi. Izi ndi zimene Iye akufuna pa wina aliyense kuposa chilichonse.  

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi inatanthauziridwa kuchokera mu Norwegian, ndipo poyamba inaonekera pa mutu oti “Dziweruzeni nokha kuti musaweruzidwe” mu bukhu la “Elias Aslaksen mauthenga ake omaliza” omwe anatsindikidwa mu 1989.  Nkhaniyi ikugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo pa webiste ino.