Nzeru ndizo kufunafuna chifuniro cha Mulungu
Pamene Mose amalemba Salimo 90 amaganizira momwe moyo ulili waufupi ndi momwe nthawi imathera (vesi 4-9). Ndipo Iye akuti: “Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.” Masalimo 90:12. Mukutanthauzira kwina akunena kuti: “Tiphunzitseni kugwiritsa ntchito nthawi yathu yonse tili nayo mwa nzeru.”
Paulo akunenanso chimodzimodzi ku Aefeso 5:15-17: “Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite.” Kufunafuna chifuniro cha Mulungu ndiye chinthu cha nzeru choposa chimene tiyenera kuchita pamene tili pa dziko pano, ndipo tidzapeza mtima wa nzeru ngati tichita izi.
Yesu amafunafuna nzeru imeneyi moyo wake onse pamene anali padziko pano. “N’chifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati, “simunafune nsembe kapena zopereka, koma thupi munandikonzera. Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo. Tsono Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa m’Malemba.’ ’’ Ahebri 10:5-7
Yesu anaperekanso umboni wake: “Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pandekha. Ine ndimaweruza molinga ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.” Yohane 5:30. Maganizo ake anali otanganidwa nthawi zonse kuchita chifuniro cha Atate Ake.
Kodi moyo wathu timaukhala motani?
Makalata onse mu Chipangano cha Tsopano alembedwa kuti atithandize okhulupirira kupeza chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, Yohane akunena ku 1 Yohane 2:15-17: “Musakonde dziko lapansi ndi chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. Pakuti zonse za m’dziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso athu amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.”
Petro nayenso akulemba kuti: “Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire m’mapazi ake. Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza. Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. M’malo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.” 1 Petro 2:21-23. Izi ndi zina zambiri zolimbikitsa zinalembedwa kuti zitithandize kudziwa chifuniro cha Mulungu paife aliyense payekha.
Pamene tasankha kukhala masiku athu padziko pano munjira iyi, tidzakhala ndi mphotho yaikulu mumoyo wamuyaya. Pamene Paulo, amene anakhala mumoyo wotere zaka zambiri, atadziwa kuti mapeto a moyo wake ali pafupi, iye anati: “Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.” 2Timoteo 4:7-8
Tiyeni tikhale anzeru tsiku lililonse, kufunafuna ndi mtima wathu onse kuchita chifuniro cha Mulungu.