Mwayi kwa onse
Mulungu anakonda dziko lapansi ndipo anapereka Mwana wake kuti apulumutse aliyense wokhulupirira mwa Iye—popanda choletsa, popanda kufunika kokwaniritsa zofunikira zinazake, ndiponso mosakondera aliyense (Yohane 3:16; Aefeso 2:4–9). Zimenezi zimapatsa anthu onse, mosasamala kanthu za mtundu, chikhalidwe, kapena kuti ndi wamkazi kapena wamwamuna, mwayi waukulu!
Yesu atapita kumwamba, Iye anati, “Pitani kwa anthu a mitundu yonse ndipo muwapange ophunzira anga...” Mateyu 28:18–20. Mwa kuyankhula kwina, aliyense, mosasamala kanthu zakuti ndi wamkazi kapena wamwamuna, mtundu, chikhalidwe kapena dziko limene amachokera. Zonse zimadalira ngati mukufuna kutero, monga Yesu anafotokozera pa Mateyu 16:24 kuti, “Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.’”
Izi ndi zimene Paulo ankafuna kuchita, ndipo tingawerenge umboni wake waumwini pa Agalatiya 2:20: *“Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m’thupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.”*
Kupachikidwa pamodzi ndi Khristu kumatanthauza kumvera kuitana kwathu kwakumwamba. “Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe kapena wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.” Akolose 3:11.
Paulo, amene anali mtumwi kwa Amitundu, akutiuza kuti timutsatire monga mmene iyenso anatsatira Khristu. (1 Akorinto 11:1). Sananene kuti zimenezi n’zosiyana malinga ndi mtundu, kaya munthu ndi mwamuna kapena mkazi, kapena chikhalidwe chake; koma ananena momveka bwino kuti amuna ndi akazi onse ali ndi mwayi wofanana wotsatira Khristu ndi kutenga nawo mbali mu imfa ya Khristu ndi moyo wa Khristu! “Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa kuchokera kwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.” 1 Akorinto 11:11–12.
Khristu ndiye chofunika kwambiri ndipo Iye amakhala mwa ife tonse
“Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera m'chikhulupiriro mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munalumukizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu. Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbeu ya Abrahamu, ndi olowam'malo molingana ndi lonjezo.” Agalatiya 3:26–29
Mpingo ungakule kokha ngati pali umodzi umenewu mwa Khristu! Pasakhale tsankho la mtundu uliwonse, kuphatikizapo tsankho chifukwa cha banja kapena chikhalidwe chimene mumachokera. Tonse ndife ziwalo za wina ndi mnzake, ndipo tonse tayitanidwa kuti tikule mwa Khristu, amene ndiye mutu wa thupi (Aefeso 4:15–16). Sitiyenera kulamulira anthu; koma tiyenera kugwira ntchito limodzi ndi ena kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro chimenechi asangalale pogawana nawo moyo wa Khristu (2 Akorinto 1:24).
Ndicho chifukwa chake Mulungu “Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe.” Aefeso 4:11–12
Tiyeni titumikirane ndi chisomo chimene Mulungu amapereka, mosasamala kanthu za zimene ena amachita komanso popanda kuyembekezera kubwezeredwa chilichonse (1 Petro 4:10–11). Mwayi wotumikira m’thupi la Khristu ndi wopanda malire chifukwa cha chisomo cha Mulungu pa moyo wathu, pakuti Iye amapereka mphatso zosiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyana, monga momwe Iye wasankhira (1 Akorinto 12:11). Choncho, n’kofunika kwambiri kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu, osati kuchita zinthu pofuna kukondweretsa anthu kapena kufunafuna ulemu wawo m’moyo wathu kapena muutumiki wathu (Yohane 5:41).
Umodzi mwa Khristu
Njira yokhayo imene tonse tingakhalire amodzi ndiyo kukhala ndi chiyanjano ndi Atate ndi Mwana wake, Yesu Khristu. Kuyenda m’kuunika kokha n’kumene kungagwirizanitse amuna ndi akazi, anthu a mafuko ndi zikhalidwe zosiyanasiyana, m’thupi limodzi limeneli, limene Khristu ndiye mutu wake (1 Yohane 1).
“Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale m'modzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa, pothetsa m'thupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nkupanga mtendere ndi kuyanjanitsa onse awiriwa m'thupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo. Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi. Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.
“Kotero kuti inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso ndi a m'banja la Mulungu. Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pangodya. Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala nyumba yoyera mwa Ambuye. Ndipo mwa Iye, inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake."Aefeso 2:14–22.
Mu mpingo, membala aliyense ayenera kukhala womasuka kukula kufikira Khristu, amene ndiye mutu. Palibe amene ayenera kulamulira wina aliyense! Palibe amene ayenera kudyera mnzake masuku pamutu—chifukwa zimenezi zimawononga ntchito ya Mulungu yokhudza miyoyo! (2 Akorinto 7:1–2).
Tikukumana ndi nthawi zovuta; tikutha kuona zimenezi m’dziko lotizungulira, mmene mphamvu zauzimu za zoipa zikulamulira. Ana athu akukumana ndi makhalidwe osalemekeza Mulungu kwambiri kusukulu masiku ano kuposa zaka zingapo zapitazo. Mpingo uyenera kukhala malo otetezeka pakati pa zonse, mmene ana ndi achinyamata angakule bwino pamodzi ndi anthu amene akufuna kutsatira Khristu ndi kukhala abusa abwino a nkhosa! (Yohane 10:1–18).
Werengani 1 Akorinto 9. Chitani zonse chifukwa cha uthenga wabwino; yesetsani kupindula anthu ambiri momwe mungathere! Kenako mudzaika maganizo anu pa kusonyeza imfa ya Khristu ndi moyo Wake munyengo zanu (2 Akorinto 4:10–11). Iyi ndiyo njira yokhayo imene mungatsatirire chitsanzo cha Paulo monga mtumiki wa onse!
Mulungu adalitse mpingo wake ndi kutipatsa tonsefe chisomo chomvetsetsa ntchito yathu, yomwe ndi kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa ndi okhulupirira, mosasamala kanthu za mtundu, kapena kuti wamkazi kapena wamwamuna, kapena chikhalidwe chawo!