“Ine sindipempherera iwo okhawa, komanso amene adzakhulupirira Ine chifukwa cha uthenga wawo. Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga ife tili amodzi. Ine ndikhala mwa iwo, ndi Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe munandikondera.” Yohane 17:20-23.
Kodi Mulungu ndi Yesu ndi amodzi bwanji?
Tili ndi maitanidwe akulu ndi opatulika oti tikhale amodzi monga Atate ndi Mwana alili amodzi. Ngati tikufuna kukhala amodzi monga Iwo, tiyenera kutsatira Mwana panjira yopapatiza yopita ku moyo.
“Pakuti Ine ndinatsika kuchokera Kumwamba, osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine.” Yohane 6:38.
“Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chikhulupiriro chosatha kwa onse omvera Iye.” Ahebri 5:8-9.
Apa tikuona mmene Atate ndi Mwana anakhalira amodzi. Yesu anabadwira m’banja la anthu ndipo anakhala Mwana wa Munthu (1 Timoteo 2:5). Monga Mwana wa Munthu, monga munthu, Iye anaphunzira kumvera. Zinali zovuta kwa Iye, koma anaphunzira kudzera m’masautso. Ndipo mu Yesaya 53 timawerenga za masautso ena amene anadutsamo pophunzira kumvera.
“Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa. Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa. Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye..” Yesaya 53:10.
Yesu anapemphera kuti, “Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna Ine!” Luka 22:42. “Chifuniro changa” chimenechi chinali chifuniro cha mtundu wonse wa anthu, chifuniro cha Yesu monga Mwana wa Munthu. Chifuniro chimenechi chinayenera kuphwanyidwa kuti chifuniro cha Ambuye chikwaniritsidwe kudzera mwa Iye, ndipo apa Yesu anayenera kudzipereka nsembe. Anatsatira njira imeneyi mwa kufuna kwake. Anasankha kuchita zimenezi! Iyi inali njira yatsopano ndi yamoyo imene Iye anatsegulira ife kuti timutsatire (Ahebri 10:20). Iyi inali njira imene chifuniro cha munthu chinaphwanyidwa ndipo chidzalo chonse cha umulungu chinakhala m’thupi la munthu (Akolose 1:19; Akolose 2:9).
Talandira malonjezo akulu ndi amtengo wapatali kudzera m’chidziwitso cha Iye, kuti ifenso tigawane nawo chikhalidwe cha Mulungu (2 Petro 1:3-4).
Kodi tingakhale bwanji amodzi monga momwe Atate ndi Mwana alili amodzi?
Lero, tili ndi mwayi womwewo umene Yesu anali nawo ngati ifenso tili okonzeka kukhala nsembe. Yesu anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa aliyense amene amamumvera (Ahebri 5:9). Mwanjira imeneyi timakhala amodzi, monga Atate ndi Mwana alili amodzi.
Izi n’zofunika kwambiri moti Paulo akunena kuti chifukwa cha zimenezi analandira chisomo ndi utumwi kuti atsogolere anthu a mitundu yonse kuti akhale omvera ku chikhulupiriro (Aroma 1:5). Koma n’zosatheka kuphunzira kumvera popanda kukhala wokonzeka kuphwanyidwa, popanda kukhala wokonzeka kukumana ndi zowawa.
Pali anthu ambiri amene amayesetsa kuti magulu osiyanasiyana achipembedzo akhale amodzi, koma n’zachabechabe. Atsogoleri amadziona ngati akuluakulu, ali ndi maganizo awoawo olimba, ndipo mamembala amene amasankha mbali amachitanso chimodzimodzi. N’chifukwa chake nthawi zonse pamakhala mikangano ndi mkwiyo mkati mwa magulu osiyanasiyana achipembedzo komanso pakati pawo. Safuna kuphwanyidwa. Ambiri a iwo amalankhula za chikondi ndi kuwerenga 1 Akorinto 13, koma simungapeze chikondi chimenechi ngati simuli wokonzeka kuphwanyidwa, komanso ngati simusiya kunyada kwanu ndi maganizo anu olimba.
Tingawerengenso zimene chikondi sichichita: Sichichita nsanje, sichidzikuza, sichifunafuna zake zokha, sichikhala ndi mkwiyo, sichiganizira zoipa, ndi zina zotero. Anthu amene safuna kuphwanyidwa amakhala ndi mkwiyo, amafunafuna zawo, ndipo amadzikuza. Anthu oterewa sangagwirizane. Nthawi zonse amaoneka kuti ali ndi chifukwa chokhumudwira, m’malo motenga mtanda wawo, kudzikana okha, ndi kudzitsutsa chifukwa cha kudzikonda kwawo ndi kuuma mtima kwawo.
Timawerenganso zimene chikondi chimachitadi: Chimaleza mtima; chimakondwera ndi choonadi ndipo chimapirira zonse; chimakhulupirira zonse, chimayembekezera zonse, ndiponso chimanyamula zonse (1 Akorinto 13:4-7; Akolose 3:12-14). Ena akakhala ovuta komanso oumitsa khosi, anthu ambiri amanena kuti: “Sindingalole zimenezo. Payenera kukhala malire pa zimene munthu ayenera kupirira.” M’malo molola kuti agonjetsedwe, amaumitsa mtima ndi kudziteteza, komanso kuteteza ufulu ndi maganizo awo. M’malo mokhululuka monga mmene Yesu anatikhululukira, amachita zoipa ndi kulankhula zoipa za m’bale kapena mlongo wawo.
Mwina simukonda munthu wina, koma ngakhale mukupitiriza kumuchitira ulemu ndi kumwetulira, mumakhala patali naye. Simukufuna kukhala naye pa chiyanjano cha mu Mzimu. Kunyada kwanu sikungalolere munthu winayo kukhala mmene alili. Simukufuna kuti kunyada kwanu kuphwanyidwe kuti mulandire chikondi chimene chimapirira zinthu zonse ndi kuyembekezera zinthu zonse. Ndithudi, simukufuna kukangana naye, choncho mumakhala naye patali mwaulemu. Koma zimenezi si kukhala amodzi monga Atate ndi Mwana alili amodzi.
Kukwaniritsidwa kwa pemphero la Yesu la umodzi wa Akhristu
Odala ali iwo amene amvetsetsa mmene Mwana alili mmodzi ndi Atate, ndipo akufuna kutsatira Mwanayo pa njira yatsopanoyi yamoyo. Pemphero la Yesu likukwaniritsidwa m’miyoyo yawo, ndipo nthawi zonse amakhala limodzi mu ulemerero. Amayenda m’kuunika monga Iye alili m’kuunika, ndipo magazi a Yesu amawayeretsa ku uchimo wonse. Amayanjana wina ndi mnzake (1 Yohane 1:7).
Tithokoze Mulungu chifukwa cha chipulumutso chaulemerero chimenechi, ndiponso chifukwa chakuti tingathe kutenga nawo mbali tikakhala ofunitsitsa kukhala nsembe, komanso kuti anthu ambiri athe kutenga nawo mbali. Mu chiyanjano chimenechi cha m’kuunika, Satana sangathe kulowamo.