Ndinkadana ndi umunthu wanga komanso mmene ndinkachitira zinthu ndi anthu ena. Ndinkadana ndi zimene ndinkachita komanso kunena. Ndinkafuna kudalitsa ena; ndinkafuna kukhala munthu wosonyeza kuti kukhala Mkhristu n’kwabwino. Koma sindinathe chifukwa ndinalibe kudzidalira; sindinkaganiza kuti ndinali wabwino mokwanira. Zimenezi zinandilepheretsa kuchita kapena kunena zinthu zimene Mulungu ankagwira ntchito mwa ine kuti ndizichite kapena kunena.
Popanda kuzindikira, ndinali kunena kuti, “Sindigwirizana ndi Mulungu, amene analenga zinthu zonse komanso amene anandilenga.” Anandilenga ndendende mmene ndilili, ndi umunthu wanga, mphatso zanga, ndiponso maonekedwe anga; ndipo kwenikweni ndinali kunena kuti Iye anandilenga molakwika. Nditazindikira zimenezi, ndinaona kuti kunali tchimo kukhala ndi maganizo odziona ngati wosafunika ndiponso olakwika pa mmene Mulungu anandilengera. Kunali kusayamika ndiponso kusakhulupirira kuti Mulungu anali ndi dongosolo langwiro pa moyo wanga, monga mmene anandilengera.
Ndinawerenga m’Mawu a Mulungu za chipatso cha Mzimu, za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziletsa, ndipo ndinadziwa kuti zimenezi n’zimene ndinkafunadi pa moyo wanga.
Chida m'manja mwa Mulungu
Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kudziona mmene Iye amandionera. Ndi thandizo Lake, ndinayamba nkhondo ya mumtima yolimbana ndi kusayamika kumeneku kumene kunali mwa ine—uchimo umenewu, chifukwa kusayamika chifukwa cha mmene Mulungu anandilengera ndi uchimo. Inde, Mulungu sanangochotsa maganizo oipa onsewa okhudza ine. Koma maganizo amenewo akabuka, Iye ankandipatsa mphamvu zolimbana nawo.
Ndinagwiritsitsa vesi la 1 Akorinto 6:20: “Ndinu ochita kugulidwa. N'cifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.” Nthawi iliyonse pamene ndinkayesedwa kuti ndiziganiza zinthu zoipa ndi kudziona ngati wopanda pake, ndinkati, “Ayi. Mulungu anandigula pamtengo wapatali. Anaona kuti ndili ndi mtengo wapatali.” Kudziona ngati wosafunika kunandipangitsa kukhala wosachitapo kanthu. Maganizo oipa amenewa sanali oona, ndipo ankandiletsa kulemekeza Mulungu ndi thupi langa komanso mzimu wanga, zimene zili za Mulungu.
Kuchimwa kumabweretsa kusakhazikika ndi mavuto. Ine ndekha ndinakumana nazo zimenezo. Koma ndikagonjetsa uchimo, ndimatha kukhala pa mtendere ndi kukhala ndi chimwemwe m’moyo wanga. Ndikakhala ndi moyo wogonjetsa uchimo, ndimatha kukhala chida m’manja mwa Mulungu (Aroma 6:13), ndipo Iye angandiphunzitse ndi kundigwiritsa ntchito monga momwe akufunira.