“Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achimfumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikireza ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitananikuti mutuluke mu mdima ndi kulowa m'kuunikakwake kodabwitsa. Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.” 1 Petro 2:9-10.
Mdima: Munthu amene sanabadwenso mwatsopano
“Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.” Genesis 1:1-2.
Dziko lapansi linalibe mawonekedwe ndipo linali lopanda kanthu, ndipo panali mdima wandiweyani. Munthu amene sanabadwenso mwatsopano alinso chonchi. “Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake. Maganizo awo ndi odetsedwa, ndipo ali osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo komanso chifukwa cha kuwuma mtima kwawo. Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha ku zilakolako zonyansa, ndi dyera lochita mtundu uliwonse wa zoyipa.” Aefeso 4:17-19
“Monga kwalembedwa: ‘Palibe munthu wolungama, inde, palibe ndi mmodzi yemwe; palibe ndi m'modzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu. Onse apatukira kumbali, onse pamodzi asanduka opandapake. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino, palibe ngakhale mmodzi.’” Aroma 3:10-12.
Apa tikuona kufunika kwa chipulumutso chozama. Kodi Mulungu anachita chiyani pachiyambi ndi dziko lapansi lopanda kanthu komanso lamdima?
Mawu a Mulungu amabweretsa kuwala ndi kutentha kuti zinthu zikule
“Pamenepo Mulungu anati, ‘Kuwale,’ ndipo kunawaladi. Mulungu anaona kuti kuwalako kunali kwabwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.” Genesis 1:3-4.
Mulungu atachita izi, dziko lapansi silinalinso lopanda kanthu. Kuwala kwa Mulungu kunaperekanso kutentha. Timawerenganso mu Genesis 1:12, “Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake, ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.”
Mulungu amachitanso chimodzimodzi ndi munthu amene amakhala mumdima komanso ali wosowa. Davide amachitira umboni momveka bwino za zimenezi mu Salmo 40:1-3, “Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga. Ananditulutsa m’dzenje la chitayiko, m’thope ndi m'chithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pathanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba. Iye anaika nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.”
Paulo atapita ku Damasiko, anali mumdima waukulu, koma ali panjira kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira. (Machitidwe 9:3.) Pambuyo pake anakhala Paulo watsopano, ndipo anati, “N'chifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.” 2 Akorinto 5:17. Kenako munthu wakale wachisoni, wodzaza ndi kudzudzula, kuneneza, kukhumudwa, nsanje, zofuna, ndi zina zotero, wapita. “Yehova ndiye wachita zimenezi ndipo n'zodabwitsa pamaso pathu.” Salimo 118:23.
Zotsatira za kuunika kodabwitsa kwa Mulungu
Pali anthu ambiri amene angachitire umboni kuti akumana ndi kubadwa kwatsopano kumeneku. Maso a mitima yawo anatsegulidwa, ndipo amatha kuona bwino chiyembekezo cha kuitana kwake, chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima, ndi ukulu woposa wa mphamvu yake kwa ife amene timakhulupirira (Aefeso 1:18-19). Mphamvu imeneyi imatithandiza kugonjetsa uchimo wonse ndi kudzionera tokha kuti chiyembekezo chokhala ndi chikhalidwe chaumulungu sichikhumudwitsa (Aroma 5:5).
Kuunika kwa Mulungu kumaperekanso kutentha m’mitima mwathu, kuti miyoyo yathu ikhale yodzaza ndi chipatso cha Mzimu Woyera (Agalatiya 5:22).
“Pakuti Mulungu amene anati, ‘Kuwala kuunike kuchokera mu mdima,’ Iyeyo ndiye anawunikira m’mitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuwoneka pankhope pa Yesu Khristu.” 2 Akorinto 4:6.
Makhalidwe abwino a Khristu akamawala kudzera mwa ife, zimakondweretsa kwambiri Mulungu, mnzathu wapabanja, ana athu, ndiponso abale ndi alongo athu mwa Khristu. Tiyeni tiyendedi m’kuunika, kuti magazi a Yesu atitsuke ndi kutichotsera machimo onse amene timaona m’kuunika (1 Yohane 1:7). Tikamayenda m’kuunika, timakana uchimo mpaka uchimo utagonjetsedwa mwa imfa. Ndipo palibe kuyeretsedwa kozama kuposa imfa.
“Popeza kuti Khristu anamva zowawa m’thupi lake, mukhale nawonso mtima womwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa m’thupi walekana nawo uchimo. 1 Petro 4:1.
Atamandike Mulungu amene anatiitana kuti tituluke mumdima ndi kulowa m’kuunika kwake kodabwitsa!