Kudziyang’anila pansi ndi kudzimva, kapena kudziona kuti ndiwe oipitsitsa kapenanso wabwino kwambiri kuposa ena, zakhala chiyambi cha zovuta za mitundumitundu m'dzikoli kuyambira pachiyambi cha nthawi. (Yakobo 3:16.) Kugonjetsa zovuta zimenezi kungakhale kovuta, koma m'mawu a Mulungu timapeza njira zothetsera vutolo!
Kodi nchifukwa chiyani kudziyang’anira pansi kuli koopsa kwambiri? Ndi chifukwa chakuti umamangidwa ndi zomwe anthu amaganiza. Sukhala ndi ufulu wokhala chimene ulia, ndipo sukhala ndi kulimba mtima kulikonse kochita zinthu zimene Mulungu wakupatsa kuti uchite. Umatuluka mu ufulu umene uli mwa Khristu. Ndipo kudzimva kotereku kumakupangitsa kuona ena ngati opanda pake chifukwa umawaonera pansi m'maso mwako.
Mwachidziwikire umu si mmene Mulungu akufunira.
Kugonjetsa kudziyang’anira pansi ndi kudzimva kukhala opambana
Kuti tigonjetse kudziyang’anira pansi ndi kudzimv kukhala oposa ena, tiyenera kudziwa kumene zimachokera.
Tielman Slabbert posachedwapa walankhula zambiri za nkhaniyi. Onse odziyang’anira pansi ndi odzimva kuti ndi oposa ena, zonsezi zimachokera ku maonedwe a zinthu zomwe umazitenga kukhala “zoposa“ kwambiri pa moyo wako. Mwina umamva kuti ukusowa chinachake chomwe ukuganiza kuti ndi choposa, kapena ukuganiza kuti ndiwe wabwino chifukwa uli ndi chinachake "choposa". Izi zikhoza kumveka ngati zosavuta, koma zikupereka kumvetsetsa kwabwino.
N'chifukwa chiyani ukhoza kudziyang’anira wekha pansi kwa munthu wina? Chifukwa maona ngati iwo ndi ochenjera kwambiri kapena ooneka bwino; umaona kuti ndalama zawo zimawapatsa mwayi, kapena kuti mphatso zawo ndi maluso awo mwanjira inayake zimawapangitsa kukhala abwino kuposa iweyo. Ndiponso njira ina ndi iyi: ngati umazikhulupirira kuti ndiwe wopambana kwambiri kapena umachokera ku chikhalidwe chabwino, kuti njira zanu zochitira zinthu ndi zolondola kwambiri, ndi zina zotero, ndiye kuti umadzimva kuti ndiwe wabwino kuposa ena. Zingakhale zovuta kuvomereza zimenezi, koma ngati udziyang'ana mosamala, mudzapeza kuti ndi zoona.
Koma zoona zake n'zakuti zinthu zimenezi ndi "zoposa" chabe pamaso pa anthu. Izi kwenikweni sizitanthauza kanthu pamaso pa Mulungu – zinthu zimene simudzapeza konse m'Baibulo. Chikhalidwe ndi miyambo ya momwe timakhalira zinatipusitsa kufika poti tinayamba kuona zimenezi zinthu zazikulu, ndipo taphunzitsidwa kukhulupirira zimenezo, kuposa mmene timakhulupirira mawu a Mulungu.
Dziko lapansi limatenga zinthu zina kukhala zofunika kwambiri monga ndalama, kukongola, maphunziro, Udindo waukulu. Koma Yesu anati, "... chimene chimalemekezedwa kwambiri [chosiririka] pakati pa anthu ndicho chonyansa [choipa choopsa] pamaso pa Mulungu." —Luka 16:15. Choncho Mulungu amadana ndi zinthu zimenezi. Zimenezi zimatithandiza kwambiri kuona zinthu m'njira yoyenera. Zinthu zimenezi sizipatsa munthu phindu lowonjezera kuchokera ku lingaliro la Mulungu; kwenikweni ndizosiyana, Iye amadana nazo pamene "mumasirira" zinthu izi ndikuyang'ana anthu omwe ali nazo, kapena kuyang'anira pansi kwa anthu omwe alibe! Mulungu ali ndi njira yosiyana kotheratu yoyezera zinthu zofunika.
Kodi chimene chili cha phindu kwa Mulungu ndi chiyani?
Muyenera kungoyang'ana mawu Ake kuti mudziwe zomwe Mulungu amaganiza kuti ndi zazikulu. Mwachitsanzo, Agalatiya 5, Paulo analemba za chipatso cha Mzimu. "Koma chipatso cha Mzimu ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa, kudziletsa. Motsutsana ndi zimenezo palibe lamulo." Agalatiya 5:22-23. Ndipo pa 1 Akorinto 13:13: "Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zimenezi ndi chikondi." Ndipo: "Iye wakusonyezani inu, munthu, chabwino; ndipo Kodi Ambuye amafuna chiyani kwa inu koma kuchita mwachilungamo, kukonda chifundo, ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wanu?" Mika 6:8. Kupeza nthaŵi yoŵerenga mawu a Mulungu kumatsegula maso anu ku zinthu zimene zili ndi phindu lenileni losatha.
Ndiye umaonanso mofulumira kwambiri kumene kusowa kwako kuli. Kunena zoona, mkhalidwe wathu wokonda kuchita zoipa omwe tinabadwa nawo ndi osiyana ndi mawu a Mulungu. Koma kwalembedwanso kumeneko kuti "Ndingathe kuchita zinthu zonse kudzera mwa Khristu chifukwa Iye amandipatsa mphamvu," ndi kuti "Iye amene wayamba ntchito yabwino mwa inu adzamaliza." Chotero ngati mukufunadi zipatso za Mzimu zimenezi, pamenepo Mulungu adzakusonyezani njira yozipezera. (Afilipi 4:13; Afilipi 1:6.)
Pamene wayamba kuona mkhalidwe wako wokonda kuchita zoipa kuti sufanana ndi mawu a Mulungu, ndiye kuti uwu ndi Mzimu umene wayamba kugwira ntchito mwa inu, akulankhula nanu za "kusandulika kwa moyo". Kusandulika kwa moyo ndiye njira imene mkhalidwe wathu wokonda kuchita zoipa umasinthidwe kukhala wa umulungu. Pamenepo muyenera kukhala wodzichepetsa ndi kuvomereza choonadi ndi kugwirizana ndi zimene Mzimu akukuwonetsani. Kudzichepetsa kumeneku sikudzimva kukhala wopanda pake kapena wopanda chiyembekezo, koma m'malo mwake, ndiko kuti ndinu wofunitsitsa kumvera chitsogozo Chake ndi wofunitsitsa kukana chifuniro chanu kotero kuti chifuniro Chake chichitike kupyolera mwa inu! Mwachitsanzo, pamene mudzikaniza kupanga nsanje, mumaphunzira kuyamikira m'malo mwake. Zimagwira ntchito mofanana m'madera onse. Mungasinthe kuchoka pa kukhala wodzala ndi nkhaŵa ndi kusakhulupirira kukhala ndi chikhulupiriro chonse ndi kudalira pa Mulungu. Kuchokera pa kukhala wodzala ndi kunyada ndi kudzitama, kukhala wodzichepetsa ndi wokoma mtima. Imeneyi ndi ntchito "yosanduliza moyo" imene Mulungu amachita mwa inu pamene muli wofunitsitsa ndi womvera. (Afilipi 2:13.)
Kuona anthu mmene Mulungu amaonera
Mukatero mudzaphunzira kuona anthu mmene Mulungu amawaonera. Palibenso kuyang'anira pansi anthu chifukwa mukuganiza kuti ndinu abwino kuposa iwo, kapena kuyang'ana kwa anthu chifukwa mukuganiza kuti ndinu ofunika pang'ono kuposa iwo. Mumaphunzira kuwayang'ana ndi chikondi, kuleza mtima, kukoma mtima, ndi zina zotero. Mulungu anapanga aliyense, komanso inuyo, kukhala ngati Iye mwini! Simungathe kuyang'anira pansi pa zomwe Mulungu analenga kuti zikhale ngati Iye mwini! Pamenepo, mukayamba kudziyang'ana nokha malinga ndi mmene Mulungu amakuonera! Mumayamba kuona kukula kwa kufunika kwako kwa Iye.
"Ngati pamenepo munaukitsidwa ndi Khristu, funani zinthu zimene zili zakumwamba, kumene kuli Khristu, atakhala kudzanja lamanja la Mulungu. Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu za padziko lapansi." Akolose 3:1-2.
Mavesi amenewa kwenikweni ndi mfungulo. Ngati malingaliro anu ali mu "zinthu zakumwamba", ndiye kuti zinthu zonse zomwe anthu amaganiza kuti ndi "zazikulu" zikuwonetsedwa ngati zopanda pake poyerekeza ndi ulemerero wopeza zomwe zili ndi phindu losatha. Pamenepo simuchitira nsanje ena kapena kuchita mantha, ndipo simukhumudwitsa aliyense. Chifukwa mukudziwa kuti Mulungu wakuikani m'moyo uno ndi makhalidwe woyenera, maluso, ndi makhalidwe omwe angakuthandizeni kukhala "chilengedwe chatsopano", kumene chikhalidwe chanu chaumunthu chimasinthidwa pang’ono ndi pang’ono kukhala chikhalidwe chaumulungu, kumene muli ndi zipatso za Mzimu. Ndipo simukusowa zambiri kuposa zimenezo.
"Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, kudzera mwamtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi. Pakuti kay mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano.Agalatiya 6:14-15.