Kodi ukufuna kumasulidwa kwa Satana oimba mlandu?

Kodi ukufuna kumasulidwa kwa Satana oimba mlandu?

Ndizotheka kumasulidwa kwa Oimba mlandu kuchokera koyambirira kwa moyo wako wa chikhristu.

8/19/202610 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Kodi ukufuna kumasulidwa kwa Satana oimba mlandu?

Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti, “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.” Chibvumbulutso 12:10

Anthu ambiri ali ophyinjika ndi Satana woneneza abale.  Koma moyo wathu wa chikhristu sukuyenera kulabadira za woneneza abaleyu. Sakuyenera kukhala ndi malo aliwonse mumtima kapena mmalingaliro a wokhulupirira aliyense.

Osamvera konse woneneza abaleyu

Satana amagwira ntchito munjira zosiyanasiyana.  Amakonda kulimbana nafe kudzera m’malingaliro ndipo amabweretsa maganizo ofowoketsa ndi opanda chiyembekezo. Timadziwa kuti tikangolakwitsa, amabwera msanga ndi kunena kuti “ Taona walakwitsanso kawiri.  Palibe chiyembekezo apa, wakhala ukuyesetsa kambirimbiri.” Munthawi zoterezi kodi tingachite chiyani?

Chinthu chabwino kwambiri choyenera kuchita ndi woneneza abale ndi kusamvera zomwe akunena. Zikhoza kukhala zoona kuti walakwitsa ndipo wachita chinthu chopusa, koma tsono wonenezayo amakuuza kuti ulibe chiyembekezo. Ndipo ukamumvera wonenezayo, umachotsedwa chifupi ndi Mulungu ndipo umakhala ofowoketsedwa ndi opanda chiyembekezo.  Koma Mzimu wa Mulungu sungakupange zoterezi ayi.  Mzimu wa Khristu nthawi zonse umabwera ndi chiyembekezo ndi chilimbikitso.  

Chomwe chingatithandize ife ndi mau a Mulungu.  Tikuyenera kukhulupirira mau a Mulungu ngakhale kuti zomwe tikumva mthupi lathu zikusiyana. Anthu ambiri sakudziwa mau a Mulungu bwino lomwe, ndiye sakudziwa kuti mau a Mulungu ananena momveka bwino  ku Afilipi 1:6 kuti: “…..Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.” Ndipo tikawerenga izi, palibenso chokaikitsa chilichonse pa mathero athu.

Zimatenga nthawi kuti ukule

Ifetu titakhala kuti tadzadzidwa ndi umulungu wonse kamodzi ndi kamodzi, tikhoza kukhala odzitamandira ndi odzikuza mwachangu.  Mmalo mwake Mulungu anakonza ndondomeko ya chipulumutso chathu mwangwiro, ndipo zimatenga nthawi kuti tikule.

Mwinatu mwagwa, pa chinachake chimene chakhala chikuchitika mobwerezabwereza m’mbuyomu, ndipo ndi dera limene mukulidziwa bwino; ndipo mwina mukugwira nalobe ntchito ndipo mwagwanso.  Ndipo apa Woneneza abale uja amabwera ndi kukuuza kuti “Waona wagwanso.” Ndipo izi ndi zoona palibenso kukana chifukwa zachitika. Kodi nanga amabwera ndi bodza lotani? Amabwera ndi ili “ Waona tsopano, palibe chiyembekezo, izi sizithekapo apa, zikhoza kuwathekera ena osati iweyo.”

Mzimu Woyera amationetsera zimene zatigwetsa, zofanana ndithu, koma pali kusiyana kwakukulu ndi mmene Oneneza abale amachitira- Mzimu Woyera amakhala odzala ndi chiyembekezo cha chigonjetso. “Pita chitsogolo ndipo phunzira ku zolakwika zako zomwe wachita kumbuyoku.  Ukhale maso kuti zisadzachitikenso ulendo wina.”  Ndipo Iye amakuuza kuti, “Ine ndidzakhala nawe, Ine ndidzakupempherera, Ine ndimakhala kuno kumwamba kukupempherera iweyo.”  Tikuyenera kulumikizana ndi dziko la muyaya losaoneka kudzera mmalingaliro ndi mitima yathu.

Ngati uyamba kukumana ndi nyengo zako za tsiku ndi tsiku opanda chiyembekezo ichi mu mtima wako, ukhoza kukhala opanda chiyembekezo, ndipo ichi ndi chifukwa chimene ambiri akodwa mu msampha wa Onenezayo.  Amayang’ana nyengo zawo za tsiku ndi tsiku ndi mu nthawi imene anachita zolakwika, ndipo iwo sakhulupirira za kukhululukidwa kwa machimo, ndiye amakhala opanda chiyembekezo.

Akhistu onse amagwirizana kuti tinalandira chikhululukiro chomwe sitimayenera konse. Ndi chinthu chimene chiinapatsidwa kwa ife.  Koma zimakhala zovuta kuvomereza za mphatsoyi.   

Mwa ichi yankhula mau a chikhulupiriro kwa iwe mwini. Tonse timaona mkhalidwe wathu oipa, ndipo timadziwa pamene tinachimwa kumbuyoku ndi pamene tinagwa, timazidziwa pamene timafowoka, ndipo izi ndi zimene Wonenezayo amayesetsa kugwiritsa ntchito polimbana nafe.

Khulupirira zomwe zalembedwa mu Mau a Mulungu

Koma Mau a Mulungu ndi amphamvu kwambiri kuposa mau a Onenezayo. Timawerenga za Yesu kuti anatifera pamene ife tinali ochimwa, chifukwa Iye anatikonda ndipo akufuna kutipulumutsa ife. Tsopano ali kumwamba kutipempherera ife, Iye ndiye wotilankhula wa chipulumutso chathu.  Tikuyenera kumenya nkhondo kuti tikhulupirire izi.

Yesu, mu chikondi, ubwino ndi kukoma mtima kwake, anaganiza zobwera pa dziko lino lapansi kudzabwezera Satana kotheratu, ndipo zotsatira zake ndi zimene tikuziona pa Chibvumbulutso 12:10: “Kenaka ndinamva mau ofuwula kumwamba akunena kuti, Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.”

Ndipo tsopano zalembedwanso za ife pa vesi 11, “Abale athu anamugonjetsa ndi magazi a Mwana Wankhosa ndiponso ndi mawu a umboni wawo. Iwo anadzipereka kwathunthu, moti sanakonde miyoyo yawo.”

Ndipo tsono ikubwera vesi 12 kenanso, imenenso ndiyofunika kwambiri, “Choncho kondwerani inu dziko lakumwamba ndi onse okhala kumeneko! Koma tsoka dziko lapansi ndi nyanja chifukwa Mdierekezi wagwetsedwa kwa inu! Iye wadzadzidwa ndi ukali chifukwa akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa.”

.Ndiye Satana Onenezayo salinso kumwamba ayi, ndipo izi zikutanthauza chiyani? Izi zikutanthauza kuti ngati ine, monga kwalembedwa ku Akolose 3: 1-2, ndaikidwa mmalo akumwamba ndi Mulungu ndipo ndikufunafuna za kumwamba, ngati ndiika masomphenya anga ndi chidwi changa ndi maganizo anga pa zinthu za kumwamba, ndiye kuti Satana alibenso kuthekera kofikira maganizo anga ndi moyo wanga.  Ndi pokhapokha pamene ndayamba kufunafuna zinthu zapansi pano, zimene zimandipangitsa kupezeka mu ulamuliro wa Satana.

Mwa ichi, ndagwiritsitsa chiganizo changa chofuna kutumikira Mulungu. Ndili ndi chidwi cha zinthu za kumwamba ndipo izi ndizimene ndigwiritsitse kwathunthu.  Uyu ndiye nangula wanga ndipo ndikachita izi, pamenepo ndi pomwe ndikhoza kugonjetsa Onenezayo. Iye akhala akuyesetsa kwa nthawi yaitali, koma akuyenera kudziwa kuti nthawi zonse pamene abwera kwa ine, ndidzamenyetsa chitseko kumaso kwake. Ndipo iye amaphwanyidwa.  Satana ndi Oneneza, ndipo tili ndi lonjezo lakuti iye adzaphwanyidwa pansi pa mapazi athu ( Aroma 16:20).  Izi sizikuyenera kutenga nthawi yaitali.  Ine ndili kumwamba ndi Khristu, ndaukitsidwa ndi Iye, ndiye tsopano ndiyenera kufunafuna zinthu za kumwamba.  Ichi ndiye chida chomwe ndili nacho polimbana ndi Satana.  

Kuneneza ena

 Chinthu chimodzi ndi chakuti ndikhoza kulolera kunenezedwa, koma Onenezayo amabweranso ndi zoneneza motsutsana ndi anthu ena.  Ndiye mzimu wonenezawu wabweretsa mavuto ambiri pa dziko lapansi. Ndiye ichi ndi chinthu chimene tiyenera kuchidziwa bwino.

 Tikudziwa kuti ngati Satana amaphwanyidwa pansi pa mapazi athu, monga kwalembedwa ku Aroma 16:20, izi sizichitika ndi mphamvu zanga kapena ndi chifuniro changa cholimba kuti ndikuphwanya Satana.  Izi zimachitika kaamba ka chisomo ndi chifundo cha Mulungu.  Ndipo ndizoyenera kuti inenso ndichitire chifundo ena.

. Yesu akutichenjeza kolimba kuti tisaweruze ena, komanso Atumwi akutilangiza kuti tisalowere zochitika za anthu ena. Ngati ndikhala otanganidwa ndi za ena, posakhalitsa ndizayamba kuwaneneza.  Koma ngati ndinapanga chiganizo chokhazikika kuti Onenezayo alibe mphamvu pa ine, ndiye kuti sindidzanenezanso ena.

 Ngati tifunafuna zinthu zakumwamba, ndiye kuti ndikuyenera kuphunzira momwe Mulungu amaonera zinthu. Mulungu analenga anthu onse,- Iye amawakonda ndipo akufuna kuti apulumutsidwe.  Ndikuyenera kukhala mumzimu omwewo, ndi mtima omwewo.

 Paulo akulemba ku Aroma 8:33, “Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa.” Taganizirani ichi, ndi chinthu chopusa kuneneza munthu amene Khristu amamupempherera.  Iye sawaneneza, Iye ali ndi chiyembekezo chonse ndi chikhulupiriro pa iwo. Ndiye kupempherera anthu komaso kuwaneneza siziyendera limodzi.

  Ngati ukuyesedwa kuneneza wina, ungoyamba kuwapempherera iwo.  Zimenezi zimafewetsa mtima wako ndi kubweretsa chiyembekezo ndi chikhulupiriro pa za tsogolo lowala pa aliyense amene Yesu anamufera.  Ndipo apatu ndi aliyense wa ife.

Kukhala ndi mtima otere zimasintha chilichonse.  Moyo wathu wonse umakatembenuzika.  Onenezayo amabwera kuti aphe ndi kuononga.  Amayesetsa kuti atibere maubale athu abwino.  Koma Khristu mmalo mwake amabwera ndi moyo ndi kuwala komanso ndi tsogolo ndi chiyanjano.    

Panga chiganizo mwa chikhulupiriro kufuna kukhala ophunzira

 Munthu aliyense, wamng’ono kapena wamkulu, amene wapanga chisankho chokhala ndi moyo wa Yesu amakhala ophunzira wake wa Yesu.  Ophunzira ndi iye amene amaphunzira, amene sadziwa kanthu kumayambiriro koma akufuna kuphunzira. Ndiye izi zimapereka chiyembekezo ukapanga chiganizo chotere. Ndipo sizitenga nthawi yaitali pamene umayamba kuona chipambano.  

Siziyenera kutenga nthawi yaitali kuti Satana aphwanyidwe pansi pa mapazi athu (Aroma 16:20), ichi ndi chisankho chomwe ndiyenera kupanga mwa chikhulupiriro mu mau a Mulungu, ndipo izi zikhoza kuchitika ku mayambiriro a moyo wanga wa chikhristu.  Kumayambiriro a moyo wathu wa chikhristu, Onenezayu akuyenera kutsekeredwa kunja.  Ndilibe kanthu kalikonse ka Satana.  Tsopano bwana wanga ndi Yesu, ndipo ndi Iye amene ndimutumikira, Iye ndi amene anandifera ndipo ili ndi tsogolo langa tsopano.  Ndachoka mu m’mdima ndili m’kuwala: ndachoka mu mphamvu ya Satana ndili kwa Mulungu (Machitidwe a Atumwi 26:18).  Ndipo izi zimachitika mu kanthawi chabe pamene ndapanga chiganizo ndi kutembenukira kwa Yesu, mpulumutsi wanga ndi bwana wanga.  

Ku Ahebri 10:22 kwalembedwa za chitsimikizo cha chikhulupiriro monga chikhulupiriro chenicheni.  Palibe kukayika konse.  Pamene tiwerenga ma umboni a a makalata a ophunzira oyamba, amadziwa kuti iwo anali oyipitsitsa.  Koma mkatikati mwa chisautso chawo, chikhulupirirochi chinalipobe kufikira kumalekezero.  Ifetu titenge iwo ngati zitsanzo zathu. Satana analibe mphamvu pa iwo. Zimene Yesu anawalonjeza, zinachitikadi.

Mau akunena pa Afilipi 1:6 kuti Mulungu amene anayamba ntchito yabwino mwa ife akayitsirizitsa.  Ndipo mwa aliyense amene ali ndi kulakalaka kotere kofuna kukhala ophunzira oona, Iye wayamba ntchito yotere. Iye wayamba ntchitoyi poyika kulakalaka kotere ndipo akayitsirizitsa.

Khala kalata ya chikhulupiriro

Ndikhoza kukhala kalata ya chikhulupiriro kwa onse ondizungulira mkatikati mwa nyengo zanga zovuta. Ndikudziwa zomwe zikuchitika m’kati mwanga, ndikudziwa nkhondo zomwe ndikulimbana nazo, koma zimenezi sizomwe anthu akuona, anthu akuyenera kuona mzimu wa chikhulupiriro ndi kugonjetsa, chiyanjano ndi Mulungu, chiyanjano ndi Yesu. Ine ndine ophunzira.  

Ku Ahebri 2:11 timawerenga kuti Yesu sachita manyazi kutitchula ife abale ndi alongo ake. Mwa ichi ndikhoza kuima ndi kulankhula kuti, “Ine ndine mchimwene kapena mlongo wake; Iye sachita nane manyazi ndipo inenso sindichita naye manyazi,” ndipo kuwala kumatuluka mwa ine. Kodi oneneza ali kuti mu ichi? Kodi kusakhulupirira kuli kuti? Ndipo ine ndikhoza kukhala thandizo kwa onse ondizungulira, kuntchito, m’banja langa, kwa achichepere omwe ndili nawo limodzi, kuti akhoza kundiona ngati mzati wa chikhulupiriro, ndikupeza chiyembekezo cha mtsogolo kudzera mwa ine.

Werenga mau a Mulungu ndi kuwakhulupirira

Werenga mau a Mulungu ndi kuwakhulupirira. Palibe chikayiko chilichonse pa mau a Mulungu pa zotsatira za moyo wako. Yamba ukadali wa chichepere, mvetsera mau a Mulungu, werenga mau a Mulungu, ndipo usamvere maganizo ako ndi zomwe umazimva mthupi lako. Izi sizikuuza zoona. Koma mau a Mulungu adzakhalapo kwa muyaya. Choncho gwiritsa ntchito mau a Mulungu monga chida mdzanja lako munyengo zako za tsiku ndi tsiku ndipo udzapambana.   

Udzaphwanya Satana pansi pa mapazi ako.  Iye alibe ufulu ndi kuthekera kokuneneza pamene ufunafuna zinthu zakumwamba.  Iye sakhalanso kumwamba ayi.  Mulungu anamutulutsa pamene Yesu anabwerera. Zonse zalipiridwa kale, ndipo zonse zili m’chimake chenicheni kuchokera kwa Mulungu, choncho khulupirira izi.

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi ikuchokera pa podcast ya Harald Kronstad, Eunice Ng ndi Mvan der Staal yomwe inatsindikizidwa pa https://activechristianity.org/ ndipo ikugwitsidwa ntchito pa website iyi ndi chilolezo