Yesu anali ofatsa ndi odzichepetsa mumtima, koma anathamangitsa amalonda mu kachisi ndi changu ndi ukali wolungama. Zimatanthauza chiyani kukhala ofatsa?
Yesu anati, “Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Mateyu 5:5
Mawu akuti “kufatsa” akhoza kuoneka ngati olakwika. Anthu akhoza kuganiza kuti pokhala ofatsa zikutanthauza kuti ena akhoza kumakuchitira zoipa, kapena kumakhala munthu wamantha osafuna kulankhula pamene ukuchitiridwa zoipa.
Koma Yesu ananena Yekha za Iye mwini kuti ali ofatsa ndi odzichepetsa mtima (Mateyu 11:29), koma ife tikudziwa kuti Iye analankhula motsutsana ndi Afarisi, anagubuduza matebulo a anthu amalonda mu kachisi, ndipo samachita mantha kulankhula choonadi. Mwa ichi sitingalankhule kuti Yesu anali wamantha pofuna kulankhula. Ngati tifuna kulandira dziko lapansi, nkofunika kuphunzira kumvetsa bwino tanthauzo lenileni la kukhala ofatsa.
Munkhani yotsatirayi, Elias Aslaksen akutionetsera kusiyana kwakukulu pakati pa kukhala ofatsa, ndi kukhala wamantha- komanso kuti chifukwa chiyani chinachi ndi chabwino, ndipo chinacho ndi choipa.
Kukhala ofatsa ndi kukhala wamantha ndi zotsutsana
Kukhala ofatsa zisamasokonezedwe ndi kukhala wamantha kulankhula pa zoipa. Mzimu wamantha ndiwotsutana ndi mzimu ofatsa. Kukhala chete kochokera mu kufatsa kumachokera mu kudalira Ambuye, koma kukhala chete kochokera kumanyazi ndi mantha zimachokera kukusadalira Iye.
Tisamaganize kuti munthu ofatsa nthawi zonse amakhala wachete. Amakhala chete pamene akuyenera kukhala chete- monga pamene akunyozedwa, pamene ena aphya mtima, pamene ena akulankhula zonyoza zosiyansiyana, pamene ena akumenya nkhondo kuti apindulepo, etc. Koma sakhala chete pamene akufuulira kwa Mulungu kupempha thandizo usiku ndi usana, kapena pamene akuyenera kukweza mawu ake ngati lipenga kuuza anthu a Mulungu za machimo awo (Yesaya 58:1); kapena pamene akuyenera kuteteza choonadi cha uthenga wabwino, kapena kulanditsa nkhosa mkamwa mwa mkango.
Mkhalidwe wa Umulungu uli ndi mbali ziwiri. Umakhala chete pamene ukuyenera kukhala chete, komanso umatha kukalipa monga mphenzi ndi ziphaliwali pamene ukuyenera kutero. Mkhalidwe wathu wa umunthu ilinso ndi mbali ziwiri. Umakafuula pamene ukuyenera kukhala chete, ndipo umakakhala chete ndi mantha pamene ukuyenera kufuula moyenera.
Kukhala ofatsa kumakutengera ku chipulumutso
“Koma Mose anali munthu wofatsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi.” Numeri 12:3. Koma iye ataona mwana wang’ombe ndi kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mmanja mwake, ndi kuyiphwanya. (Eksodo 32:19)
Ndipo Yesu, amene atiuza kuti tiphunzire kukhala ofatsa kuchokera kwa Iye, anali wodzala ndi changu ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi kuwatulutsa m’kachisi ndi chikwapu. (Yohane 2:13-17) Aliyense sakuyenera kukhala ofatsa pa nyengo ngati izi. Tikhale otsimikizika kuti chifatso chimapezeka mwa anthu auzimu; koma munyengo ngati izo, makhalidwe ena a umulungu amayenera kuonekera kwambiri chikukwa akuyenera kutero.
Timawerenga ku Yakobo 1:21 kuti tiwalandire ndi chifatso mau omwe anadzalidwa mwa ife. Pamene mau atiweruza ndi kutikonza, pamene asiyanitsa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizana fundo ndi mafuta (Ahebri 4;12), pamene atiphwanya ndi kutipeputsa, pamene ativula ndi kutiika pa mbalambanda- pamenepo ndi pofunikira kwambiri kukhala chete ndi kufatsa ndi kuvomereza kuti Mawuwo ndi oona. Ndipo tikuyenera kukhala chete osati kulimbana ndi kupereka mayankho, kudziteteza ndi kupeza zifukwa zozitetezera. Tikachita izi tidzapitirira kuyenda pa njira ya moyo ndipo moyo wathu udzapitirira kupulumutsidwa mwa ndondomeko.