“Wodala ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.” Mateyu 5:8
Anthu wodala amakhala anthu osangalala. Ndipo iwo amene ali oyera mtima amakhala osangalala chifukwa salola choipa kulowa mu mtima mwawo chomwe chingawapangitse kukhala osasangalala.
M’malo mokhala ndi mtima wadzala ndi zonyansa, kusayamika, kusakhulupirira ndi zokayikira zoipa za ena, iwo amakhala ndi maganizo oyera ndi abwino, maganizo oyamika ndi maganizo wolingalira momwe akhoza kudalitsira ena. Saloleranso maganizo aliwonse odzikonda, azonyansa, wokayikira ndi wodandaula kuti alowe mwa iwo.
Kodi ndikhoza kupeza mtima woyera bwanji ndi kuwusunga motero?
Ukhoza kulankhula ndi anthu okwana 100 ndipo onse akhoza kunena kuti akufuna kukhala osangalala. Koma si onse omwe akhoza kukhala okonzeka kuchita zoyenera kuti asunge mitima yawo kukhala yoyera. Kupeza mtima woyera ndi kuwusunga izi sizichitika pazokha. Kupeza mtima woyera ndikuyenera kukonza zinthu mu moyo wanga pamaso pa Mulungu ndi anthu. Koma chiyero sichilekeza pomwepo.
Kwalembedwa ku Masalimo 119:9: “Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.” Mawu a Mulungu amandiuza momwe ndikhoza kusungira mtima wanga kukhala oyera m’moyo wanga wonse. Sizovuta kuyamba kukhala woyera mtima. Koyambirira, ungotenga vesi imodzi ndikuyamba kuyichita, monga vesi ya ku 1 Atesalonika 5:18, “Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.”
Tangoganizani momwe ndikhoza kukhala osangalala mu mwezi umodzi wokha ngati ndikhala oyamika mu zonse. Nanga pakutha pa chaka kenako zaka 10? Tangoganizani kumapeto a moyo wautali woukhala ndi mtima woyera wodzala ndi chiyamiko, pamene ndayamba kupanga zisankho zoyenera pamene ndili wachinyamata!
Munyengo iliyonse ndikuyenera kupanga zisankho za momwe ndikhoza kuwaonera anthu, zomwe ndimachita panthawi yomwe sindikugwira ntchito, ndi maganizo amene ndimawalola kulowa mumtima mwanga. Mawu a Mulungu amatsogolera moyo wanga ndipo amandithandiza kupanga zisankho zoyenera mu nyengo zanga zonse.
Mapeto a moyo wokhalidwa mu kuyera mtima
Davide anati ku Masalimo 23:6, “Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m’Nyumba ya Yehova kwamuyaya.” Umu ndi mmene moyo umaonekera ukawukhala mu kuyera mtima. Zikatero umangokhala wosangalalirabe.
Sikokhako kuti zokoma ndi chikondi chosasinthika zizanditsata masiku onse a moyo wanga, koma ndidzalandiranso chimwemwe chosatha ndi kudalitsika pamodzi ndi Yesu ndi oyera mtima onse. Uwu ndiye moyo woyenera kuwukhala - moyo wosakhala ndi choipa chilichonse mumtima wanga ndipo wopanda kunong’oneza bongo!