Izi zimangotenga kanthawi kochepetsetsa kuposa theka ya mphindi ...

Izi zimangotenga kanthawi kochepetsetsa kuposa theka ya mphindi ...

Mphamvu yaikulu ya kukhala oyamika ingasinthe mkhalidwe kotheratu.

2/18/20253 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Izi zimangotenga kanthawi kochepetsetsa kuposa theka ya mphindi ...

Kumayambiriro kwa ukwati wathu, tinakhala ndi banja lina loopa Mulungu kwa miyezi ingapo. Banjali linali ndi ana angapo ndipo linalibe ndalama zambiri. Nyumba ndi mipando zinali zakale, anawo anali kusewera paliponse ndikupanga chisokonezo, ankasunga ziweto zingapo ndipo nthawi zonse pakhomopo pankaoneka kuti pali alendo. 

Tsiku lina ndinali kumwa tiyi ndi Amayi, ndipoanandiuza kuti, "Ife timakhala ngati mafumu ..." 

Tsiku limenelo anandisonyeza chinsinsi chachikulu: kukhala oyamika ndi njira yopambana ya kaganizidwe ndi kakhalidwe koyeyenera.  Apatu pali chinthu: chofunika:  pamene tidziphunzitsa tokha kukhala oyamika zingasinthe miyoyo yathu mukanthawi kochepetsetsa kuposa theka la mphindi. 

Koma kwenikweni, motani? 

Kuyamika kuyenera kukhala maziko a moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, ndipo pali zifukwa zabwino zochitira  izi. 

Chifukwa chimodzi n'chakuti zimakhudza anthu amene timawazungulira. Tinali ndi mlendo posachedwapa ndipo tinakonzekera kumupatsa tsiku labwino. Koma zinthu sizinayende mmene tinkayembekezera. Ndisanamve chisoni kuti tsikulo silinayende bwino monga momwe tinakonzera, njira imene mlendo wathu anachitira inatenga malo. Chilichonse chinali "changwiro" kwa iye - anali wokondwa ndi zonse; iye anaseka pamene zinthu zinalakwika ndipo anali kulankhula nafe mosangalala m'kuchuluka kwa magalimoto munseu. Kuyamika kwake kunandisangalatsa ndipo kunali chitsanzo kwa ine cha mmene timakhalira wina ndi mnzake, ndi mmene kuyamika kungasinthire mkhalidwe kaamba ka ubwino. 

Ndipo kuyamika kumatisinthanso. Panali nthaŵi imene ndinagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kuweruza zimene mwamuna wanga anali kuchita ndi kunena, m'malo mwa kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kudziweruza. Izi nthawi zina zimapangitsa kuti tiziimba mlandu wina ndi mnzake, ndipo ndikukumbukira tsiku lina adanena chinachake chomwe chinandipweteka ndipo ndinakhumudwa. Ndinaima pawindo ndikumuyang'ana akupita kuntchito ndipo mwadzidzidzi ndinaganiza kuti: Iye ndi munthu wabwino, kwenikweni. Ndipo ndinaganiza zoika kukhumudwa kwanga kumbali imodzi ndikumupempherera - kuti akafike kuntchito bwinobwino, kuti tsiku lake liyende bwino, kuti amve mawu a Mzimu mu zonse zomwe adachita, ndikuti ndikhoza kuchita mbali yanga kuti ndipange khomo lathu kukhala lamtendere. 

Pamene ndinali kumupempherera, ndinayamba kumuyamikira kwambiri, ndipo kukhumudwa kwanga kunaoneka kukhala kochepa ndi kopusa. Kusintha kuchoka pakukhumudwa kukhala woyamikira kunatenga masekondi asanu koma kunasinthiratu tsiku langa ndi momwe ndinkawonera moyo. Ndinayamba kusiya kumuweruza. 

Koma kodi nchiyani kwenikweni chimene chimachitika m'masekondi asanu ofunika kwambiri amenewo? 

Pali nthawi yomwe Mulungu amatsegula maso anga ndikuwona momwe ine ndekha ndiliri kwenikweni, ndipo izi zimandipatsa njala yofuna kusintha kakhalidwe kanga. Chisankho chomwe ndikhoza kuchita  mu masekondi amenewo ndi chimene chinene  ngati ndikugwiritsa ntchito mwayi wosinthidwa ndi mphamvu ya Mzimu, kapena ngati ndikuyenda kuchoka pawindo ndikutsimikizabe kuti mwamuna wanga ndiwolakwa ... 

"Choncho tonsefe amene tachotsa chophimba chimenecho tikhoza kuona ndi kuonetsa ulemerero wa Ambuye. Ndipo Yehova—amene ali Mzimu—amatichititsa kukhala ngati iye kwambiri pamene tikusinthidwa kukhala chifaniziro chake chaulemerero." 2 Akorinto 3:18. 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhaniyi yachokera ku nkhani ya Maggie Pope yomwe idasindikizidwa poyamba pa https://activechristianity.org/ ndipo yasinthidwa ndi chilolezo chogwiritsira ntchito pa webusaitiyi.