Kukhala moyo wa chiyero ndi wopembedza Mulungu ndi njira yokhayo yokhala ndi ufulu weniweni ndi chimwemwe, ndipo komalizira kulandira ulemerero waukulu kwambiri pamene Yesu abweranso. Ndipo iwo amene ayembekezera za Tsiku lalikulu ili akhoza kulifulumizitsa pakuyesetsa kukhala moyo wa chiyero ndi wabwino.
“Popeza kuti zinthu zonse zidzaonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wa chiyero ndi opembedza Mulungu pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale opanda chilema…N’chifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zinthu zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa.” 2 Petro 3:11-12,14,17
Tsopano ndi kofunikira kwambiri kulimbikitsana wina ndi mnzake za kukhala moyo wa chiyero ndi opembedza Mulungu. Ichi ndi chipulumutso chokhacho chomwe tili nacho. Anthu ambiri amafuna kupanga zonse zomwe akhoza, koma safuna kukhala moyo wa chiyero ndi opembedza Mulungu, zotsatira zake adzaonongeka.
Konda zomwe Iye amakonda ndipo dana ndi zimene Iye amadana nazo
Kuopa Mulungu, kapena kukhala moyo wa chiyero zimatanthauza kukhala kutali ndi uchimo ndi chodetsa. Ndi chikondi cha Khristu chokha chimene chikhoza kutisiyanitsa kotheratu ku uchimo, ndipo mu chikondi ichi ndi mmene sitidzachititsidwa manyazi pakudza Kwake. Ngati ife timukonda Iye, ndiye kuti tidzadana ndi zimene Iye amadana nazo ndi kukonda zimene Iye amakonda. Wina aliyense asakayikire izi pamene awerenga Baibulo.
Timoteo anatsatira chiphunzitso cha Paulo ndi moyo wake ndipo analimbikitsikidwa kuziphunzitsa yekha kukhala opembedza Mulungu. Ifenso tiyenera kutsatira zitsanzo za moyo wa Yesu ndi Atumwi komanso miyoyo ya oyera mtima ena ndi anthu owopa Mulungu- osati kuphunzira monga mwa thupi, koma kutsata iwo mu mzimu ndi choonadi.
Kodi moyo opembedza Mulungu umatanthauza chiyani?
Kodi moyo opembedza Mulungu zimatanthauza chiyani, kapena kuopa Mulungu? “Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.” Miyambo 8:13. Kukhala moyo wopembedza Mulungu ndiko kuyanjana ndi Ambuye ndi kudana ndi zimene Iye adana nazo.
Moyo opembedza Mulungu, kapena kuopa Mulungu, zimatipangitsa ife kukhala okhazikika ndi osasunthika kuti tisatenge mbali munjira za anthu oyipa ndi kutaya chitetezo chathu cha chikhulupiriro chokhazikika. Munthawi yathu ino, kusalungama ndi komwe kukulamulira dziko lapansi kuposa kale. Anthu akunamizidwa ndipo iwonso akunamiza anzawo. Chilichonse chikulunjika ku chionongeko ndi kusamvera. Anthu akufunafuna ufulu umene sunakhalepo ndipo mmalo moti akhale omasuka, akukhala okodwa mu chionongeko ndi zokhumudwitsa, ndipo mapeto ake a zoipa zonse ndi kudza kwa Okana Khristu, osamvera uja.
“Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, ‘Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.’ ’’ Ahebri 13:5
Zikuoneka kuti padzafika nthawi ya kulemera Yesu asanabwerenso. Anthu adzamanga ndi kudzala, kudya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa kufikira tsiku lakudza kwa Yesu. Kukonda ndalama kumapangitsa anthu kukhala akhungu ku chuma choona ndi chamuyaya. Munthawi ya Nowa, komanso m’masiku a Loti, anthu anasocheretsedwa ndi zinthu za padziko, ndipo anawonongeka. Analipo owerengeka okha omwe anapulumutsidwa. Tiyeni tikhale odzipereka kwathunthu ndi owerengeka omwe akufunafuna kukhala moyo wa chiyero ndi opembedza Mulungu. Tikatero sitidzachititsidwa manyazi pamene Yesu abweranso.