Chaka chatsopano mu dzanja la Mulungu

Chaka chatsopano mu dzanja la Mulungu

Nkhani iyi inalembedwa mu chaka chatsopano cha 1957, koma ndiyofunikiranso kwambiri lero monga inalili nthawi imeneyo.

8/19/20267 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Chaka chatsopano mu dzanja la Mulungu

Chisamaliro cha Mulungu ndi chitsogozo changwiro 

Kachikenanso, tikulowa mu chaka chatsopano, ndi chisomo chatsopano ndi mwayi watsopano.  Mulungu akudziwa kale bwino zonse zomwe chaka chatsopanochi chibweretse mwatsatanetsane, ndipo ichi ndi chitonthozo chomwe tili nacho kwa ife amene timakhulupirira.  Iye amayang’anira zonse zochitika pa dziko pano, ndipo Iye amang’anira moyo wa wina aliyense wa ife.  Mwa ichi tikhoza kuyang’ana ku tsogolo lathu wodzala ndi mpumulo, chimwemwe, ndi chiyamiko mu nyengo zathu zonse, ndi chikhulupiriro komanso kulimbika mtima mwa Iye.  Iye amatikonda ndipo akufuna kutikonzekeretsa za moyo wamuyaya kudzera munyengo zonse zomwe akuzilola pa njira yathu. 

Koma anthu amene amangofuna kukhala moyo wabwino pa dziko pano adzakhala moyo wosakondwa pamene zinthu zawo siziyenda monga momwe amafunira kapena pamene sakumvetsa momwe zinthu zikuyendera. Timawerenga ku 1 Timoteo 5:6 kuti iwo imene amakhala moyo wokwaniritsa zilakolako zawo ndi akufa ngakhale ali moyo.  Mulungu amayesetsa kuwadzutsa anthu oterewa ku tulo ta imfa iti chifukwa amawakonda ndipo akufuna kuti apulumutsidwe.  

Pamene Mulungu atsutsana ndi odzikweza mu njira zawo zonse, amakhala ndi cholinga chakuti ngati nkotheka athe kuwona ndi kuvomereza choonadi komanso modzichepetsa afunefune chipulumutso, pakutero adzadalitsika. Werengani Jobu 33  

Makolo amatha kuganiza kuti Mulungu ndi owuma mtima pamene m’modzi wa ana awo, amene amamukonda kwambiri, watengedwa kwa iwo.  Komatu uwu ndi ubwinonso wa Mulungu.  Mwachitsanzo, ndi kwabwino kuti watengedwa kupita kumudzi kwa Mulungu akadali wang’ono, wosaonongedwa ndi uchimo, koposa kukhala moyo ngati wochimwa kwa zaka zambiri ndi kukhala otayika kwa muyaya.   

Chitsime cha Moyo 

Pamene tikhala moyo wongofuna kusangalatsa anthu ndi womangidwa ku zinthu zooneka ndi maso, tidzakhala osowa mpumulo ndi wodzala ndi madandaulo a mtundu uliwonse.  Koma pamene ife, kudzera mwa Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro cha moyo, tamasulidwa ku izi zonse ku moyo wathu wam’malingaliro, tidzafika ku ufulu waulemerero wa chimwemwe ndi mpumulo.  Sipadzakhalanso chilichonse chomwe chidzasokoneza mpumulo wathu wa mkati, ndipo chimwemwe chathu chidzachokera mkati osati kunja.  Chitsime cha moyo chotere sichidzaphwa.  

Koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu.  Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” Yohane 4:14 

 Tiyeni tikumane ndi tsogolo lathu ndi chitsimechi mkati mwathu chimene chidzatitsogolera ife ku moyo wopambana ndi wodalitsika mwa Mulungu.   Pamene zaka zikupita, matupi athu amakhala akukula ndi kufowoka, koma ndi chinthu chodalitsika kuona kuti mzimu wathu mkati mwathu ukusandulika tsiku ndi tsiku ndipo moyo wathu wamkati ukukula tsiku ndi tsiku ngati tikhala okhulupirika ku malamulo a Mulungu. (2 Akorinto 4:16-18) 

Israeli ndi mkwatulo 

Pali zinthu zambiri zimene zidzachitike padziko pano m’masiku otsiriza.  Masiku ano, pali mpungwepungwe wa ndale, ndipo anthu akudabwa kuti kutsogoloku kubwera zotani.  Zochitikazi zikukhudza Israeli, koma palibe mphamvu imene ikhoza kutchinga Ayuda kumanga dziko lawo.  Dziko laling’ono ili ndi chozizwa ku dziko lapansi ndipo lidzapitirira kutero ndi mphamvu yaikulu.  Aliyense amene afuna kuwononga Aisraeli adzachititsidwa manyazi.  

 Koma chimene chili chachikulu ndi chofunika koposa zina zonse zomwe zikuchitika ndi kukonzekeretsedwa kwa mkwatibwi za kudza kwa Khristu.  Wodala ndi iwo amene akutengapo mbali pa kukonzekeretsedwaku ndi iwo amene adzakwatulidwa.   

 Tiyeni tionetsetse kuti tili pakati pa anthu amene Mulungu anawaitana ndi kuwasankha, pakukula mu zipatso za Mzimu.  “Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.” Werenga 2 Petro 1:10-11.  

Ngati tili owopa Mulungu tili ndi tsogolo lowala kutsogolo kwathu.  Tikumwa pa chitsime, tikweze mitu yathu pamwamba ndi kuchita malamulo a Mulungu, kukhulupirira ndi kudalira mwa Iye amene anatiyitana.  Iye ndi wamphamvu zonse kutipatsa ife chigonjetso pa uchimo wonse ndi kutipereka ife angwiro ndi opanda cholakwa pamaso pake pakudza Iye. (Akolose 1:22) 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi ikuchokera pa nkhani ya Aksel J. Smith yomwe poyamba inatsindikizidwa pa mutu oti “Chaka chatsopano” mu Skjulte Skatter” (Hidden Treasures) mu January 1957.  Yatanthauziridwa kuchokera ku Norwegian ndipo ikugwiritsidwa ntchito ndi chilolezo pa website iyi.