"Iwo anapereka ana awo aamuna ndi aakazi monga nsembe kwa mafano a Kanani." —Salimo 106:37. Izi zalembedwa ngati chenjezo kwa ife, kuti tisachite chimodzimodzi.
Fano lotchedwa 'Ukulu wa Dziko'
Pali fano lotchedwa: Ukulu wa Dziko. Uyu ndi mulungu amene amalambiridwa ndi pafupifupi aliyense, ponse paŵiri ndi akudziko ndi achipembedzo, olemera ndi osauka. Pafupifupi Akristu onse amayang'ana chimene chiri chachikulu, ndipo amafuna kuti ana awo akhale ophunzira kwambiri kotero kuti akhale aakulu m'dziko, ngakhale pa mtengo wa chikhulupiriro chawo Chachikristu. Ndipo pamene aperekedwa nsembe ku fano limeneli, makolo awo samawabweza.
Abrahamu anapereka mwana wake mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, koma lerolino anthu akupereka ana awo mogwirizana ndi chifuniro chawo, malinga ndi zimene anthu amayang'ana ndi kusirira. Ana a Isiraeli anapereka nsembe ana awo aamuna ndi aakazi kwa mafano (Salmo 106:37), ndipo chinthu chomwecho chachitidwa m'mibadwo yonse. Anthu ndi ofunitsitsa kuchita zonse kuti ana awo akhale aakulu m'dzikoli. Koma Yesu anati: "Ufumu wanga suli wa dziko lino."
Ukulu wa kudziwa Khristu Yesu
Kuti akhale aakulu, ayenera kudzaza ubongo wawo ndi chidziŵitso cha dziko, ndipo kaamba ka ichi chirichonse chaperekedwa nsembe pa guwa la nsembe la fanolo. Koma Paulo akuti, "Zinthu zimenezo zinali zofunika kwa ine, koma tsopano ndikuganiza kuti zilibe kanthu chifukwa cha Khristu. Osati zinthu zimenezo zokha, koma ndikuganiza kuti zinthu zonse zilibe kanthu poyerekeza ndi ukulu wa kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga. Chifukwa cha iye, ndataya zinthu zonsezo, ndipo tsopano ndikudziwa kuti ndi zinyalala zopanda pake. Zimenezi zimandilola kukhala ndi Khristu komanso kukhala wake." Afilipi 3:7-8.
Ngakhale m'misonkhano yambiri yachipembedzo, munthu angakhale m'busa yekha pambuyo pophunzira kwa nthawi yaitali. Koma ngati tidziŵa Mulungu, timalankhula mawu a Mulungu popanda kufunikira madipuloma apadziko lapansi. Koma anzeru a m'dzikoli amachedwa kwambiri kuphunzira kudziwa Mulungu mwa chikhulupiriro. Chidziŵitso chawo chimamamatira kwa iwo, ndipo nthaŵi zonse akuyerekezera nzeru za dziko (zimene ziri chinyengo chopanda pake) ndi nzeru ya Mulungu, imene idzavumbulidwa m'nthaŵi yake kulamulira olamulira ndi maulamuliro onse.
Tiyeni tipereke nsembe ana athu aamuna ndi aakazi kwa Ambuye, pakuti ichi ndi umulungu weniweni. Tiyeni tiwaphunzitse zimene Mulungu amaona kuti n'zazikulu kuti amusangalatse. Tiyeni tiwapereke kwa Iye amene ali Mutu pa olamulira onse ndi mphamvu, ndiye tidzawabwezeretsa mpaka kalekale.
Pempherani kuti Mulungu atsegule diso kuti muthe kuona
Pempherani kwa Mulungu kuti atsegule diso kuti muthe kuwona, chifukwa ngati mutayang'ana pepala lililonse lachipembedzo (zilibe kanthu kwenikweni kuti ndi liti), mudzawona kuti amasirira ukulu wa dziko, ngakhale kuti sakunena pomwepo. Atsogoleri a misonkhano yachipembedzo nthaŵi zonse akuuziridwa ndi ukulu wa dziko ndipo anthu akuufuna motero. Kwa iwo Mulungu ayenera kukhala wogwirizana ndi dziko. Ziribe kanthu momwe anthu oopa Mulungu omwe ali otsika ndi osauka angakhalire, ngakhale kuti chidziwitso chawo cha Mulungu ndi chachikulu kwambiri, amawonekabe ngati otsika kuposa ena.
Koma pamaso pa Mulungu iwo ali oyenera kutumikira monga "ansembe" pamaso pa Mulungu. Ezekieli 44. Iwo ali odzala ndi mantha ndi chikondi cha Mulungu, ndipo amakonda anthu Ake oyera. Iwo sanaperekedwe nsembe kwa mafano, koma aperekedwa nsembe kwa Mulungu wamoyo kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, ndipo adzakhala ndi moyo kosatha. Koma amene amalambira mafano adzatayika kosatha.
"Ana aang'ono, dzisungireni nokha ku mafano." 1 Yohane 5:21.