Posachedwapa, ndazindikira momwe nthawi zambiri ndingadziwone ngati wabwino pang'ono kuposa anthu ena omwe mwina sangakhale anzeru monga momwe ine ndili, kuchita chinthu mosiyana kapena osawona zinthu momwe ndimaziwonera. Anthu ena akhoza kudziyerekezera ndi anthu ena ndi kukhala ndi vuto la kudziyang’anira pansi - kumene amadziona okha kuti ndi osayenera podziyerekeza ndi omwe ali nawo. Koma ndazindikira mwa ine ndekha kuti ndikadziyerekezera ndi ena, nthawi zambiri ndimatha kukhala ndi vuto la kudzimva ndi kuziona kuti ndine woposa - ndikuganiza kuti ndine wabwino kuposa anthu omwe andizungulira.
Kupikisana ndi ena "amene ali ndi zonse"
Ndachiona chiimenechi ngakhale mu zinthu zazing'ono m'moyo wanga. Mwachitsanzo, sindigwirizana ndi mafashoni. Ngakhale kuti ndimakonda kukhala ndi zovala zatsopano, sizofunika kwambiri kwa ine ndipo kotero nthawi zambiri ndimakonda kuvala zovala zomwe zingakhale mu mafashoni zaka zingapo zapitazo. Koma pali ena omwe nthawi zambiri amakhala ndi zinthu zatsopano, ali ndi nyumba yaikulu kapena galimoto yabwino.
Kuyang'ana anthu amene ali ndi zambiri kuposa ine kungandichititse kudzimva wotsika kapena wachisoni. Kuyesa kuyendera limodzi nawo kungandichititse kupsinjika maganizo ndi kuda nkhawa komanso kukhala ndi zofuna, komanso kukhala wosasangalala chifukwa cholephera kupikisana ndi amayi awa omwe "ali ndi zonse".
Koma ndikumvanso mbali ina ya izo, yomwe ndi kukhala odzimva ndi oziona kuposa ena. Ena mwa malingaliro omwe amabwera ndi, "Kodi padziko lapansi ali ndi nthawi yotani pa zimenezo?," kapena "Ine sindimasala, chifukwa ndimatha kumavala chinthu chomwecho mobwerezabwereza ku tchalitchi," kapena "Kodi akufuna awoneke ngat ndani potumiza zimenezi pa Instagram?" Mndandanda umapitirirabe.
Zotsatira za nsanje
Kudzudzula ena, ngakhale kudzera m'maganizo mwanga, n'chimodzimodzi ndi kuganiza kuti ndine wabwino kuposa enawo. Ngakhale kuti ndimazazindikira pambuyo pake kuti malingaliro amenewa nthawi zambiri amakhala chifukwa chakuti ndili ndi nsanje. Ndipo nkofunika kuwona ndi kuvomereza zimenezi kwa ine ndekha. Ndakumana nazo kuti malingaliro awa a nsanje ali ngati matenda opatsirana, kuyambitsa chisokonezo m'moyo wanga chomwe chimafalikiranso ku miyoyo ya anthu omwe ndili nawo pafupi kwambiri.
Zalembedwa pa Yakobo 3:16, "Kumene kuli nsanje ndi dyera, padzakhala chisokonezo ndi mtundu uliwonse wa zoipa." Nsanje imandipangitsa kuyerekezera zimene ndili nazo ndi munthu wina ndipo mwachinsinsi ndimalakalaka ndikanakhala ndi zimene anali nazo, kapena ngakhale kulakalaka kuti ndikhale ndi kanthu kena kabwino kuposa iwo kotero kuti andichitire nsanje.
Ngakhale kuti ndizosokonekera, ndimaona kuti ngati ndilibe zimene munthu wina ali nazo, zisandichititse kumuyang’anira pansi uyo amene ali nazo. Ndikhoza kuganiza kuti, "N'chifukwa chiyani akanawononga ndalama pa zimenezo?" pamene kwenikweni, ndikanakhala ndi ndalamazo, ndikanakonda kugula chinthu chomwecho. Monga momwe zalembedwera m'Mawu a Mulungu, nsanje imapanga chisokonezo (kusakhazikika), ndipo imamangidwa ndi chinthu chilichonse choipa.
Kusunga mtima wanga woyera
"Koposa zonse, tetezani mtima wanu, pakuti zonse zimene mumachita zimachokera ku izo." Miyambo 4:23. Zinthu zomwe ndimalola mumtima mwanga ndi maganizo anga zingayambitse mtendere ndi chikondi, kapena malingaliro ambiri osakhazikika, osakondwa ndi nkhawa. Mwa kuchita Mawu a Mulungu, ndi kusankha mwadala kutsutsana ndi malingaliro oipa ameneŵa, ndingasunge mtima wanga kukhala woyera. Ndiyeno sindisonkhezeredwanso ndi kulamulidwa ndi mmene ndimaonera zinthu, malingaliro, ndi zimene ndimazimva mthupi mwanga, ndipo ndimatha kuona ena m'njira yabwino ndi yodalitsika.
"Musachite chilichonse pofuna kudzikonda, koma modzichepetsa muziganizira kuti ena ndi abwino kuposa inuyo." Afilipi 2:3.
Ngati ndichita monga momwe ndimeyi imanenera, zidzandipulumutsa kuti ndisatenge maganizo anga apamwamba ndi kuyang’anira pansi ena. M'malo momayang'ana nthawi zonse kunja, zomwe ena ali nazo ndi kuchita, ndikuweruza malinga ndi zinthu zimenezo, ndikhoza kukhala ndi mtima wabwino komanso wotseguka. Ndikhoza kuphunzira kudalitsa ena ndi kuwapangitsa kukhala abwino monga momwe ndingathere kwa iwo.