Zimene zimachitika m’maganizo mwanu zimadzaonekera nthawi zonse m’zimene mumanena kapena kuchita, mwanjira ina kapena ina. Munganene kuti maganizo anu ndiwo moyo wanu. Koma nthawi zina maganizo amenewo angakhale odzaza ndi malingaliro ndi zithunzi zosafunika. Ndiye tingakhale bwanji ndi moyo wa maganizo oopa Mulungu komanso wachimwemwe?
Ikani Mawu a Mulungu m’maganizo mwanu
Ndikofunika kwambiri kuti maganizo athu azikhazikika m’Mawu a Mulungu, komanso kuti Mulungu atiululire Mawu ake. Tiyenera kuyeretsa maganizo athu amkati, ndipo zimenezi zingatheke kudzera m’Mawu a Mulungu okha. “Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana fundo ndi mafuta a m’mafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za m'mitima.” Aheberi 4:12. Mawuwo amaweruza ndi kulekanitsa maganizo athu.
Mu Malaki 3:2 kwalembedwa kuti: “Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ng'anjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa.” Tikuzindikira kuti tifunikira sopo wamphamvu ndi moto woyeretsa m’maganizo athu, kuti maganizo athu akhale okondweretsa Mulungu. Uchimo nthawi zambiri umayambira pa zimene zikuchitika m’maganizo mwathu, choncho timafunikira Mawu a Mulungu kuti ayeretse maganizo athu. Ndipo tiyenera kumamatira ku Mawu ake.
Anthu ambiri amavutika kwambiri ndi maganizo awo, ngakhale atalandira chikhulupiriro. Izi zili choncho chifukwa m’mbuyomu ankakhala ndi maganizo ambiri oipa, onyansa komanso osayera. Maganizo amenewa amabweranso kwa iwo ndipo amawabweretsera masautso aakulu. Koma kuti muwathetse, muyenera kugwiritsitsa mawu a Mulungu!
Paulo akunena pa 1 Atesalonika 2:13: “Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.” Choncho, Mawu a Mulungu ndi amphamvu kwambiri. Ndikawalandira monga ochokera kwa Mulungu, osati monga mawu a anthu, Mawuwo amayamba kugwira ntchito mwamphamvu mwa ine. Kenako moyo wanga wakale wa maganizo umatsukidwa, moti ndimalandira maganizo atsopano—moyo watsopano wa maganizo wogwirizana ndi Mawu a Mulungu.
Maganizo atsopano kudzera mu mphamvu ya Mawu!
Ngati mukuona kuti zimakuvutani pa moyo wanu wamaganizo, ndiye kuti muyenera kuika chiyembekezo chanu mwa Mulungu ndi kukhulupirira Mulungu, mawu a Mulungu, ndiponso moto wa Mulungu! Moto umene uli m’mawu a Mulungu udzawotcha zithunzi zonse zoipa zimenezi m’maganizo mwanu. Kenako mudzalandira zithunzi zatsopano ndi zokongola kuti zilowe m’malo mwake. Zithunzi zabwino. Mulungu adzakukumbutsani za anthu amene mungawapempherere. Mudzakhala ndi anthu amene amakubweretserani chisangalalo mukamawakumbukira mumtima mwanu. Ndi zina zotero. Mudzazindikira kuti mawuwo akukhala amoyo mumzimu mwanu. Kenako mudzayamba kukhala ndi malingaliro atsopano—moyo watsopano wamaganizo.
Zalembedwa mu 1 Yohane 3:9: “Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbeu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.” Apa tikuona mphamvu yayikulu imene ili m’Mawu a Mulungu. Mawu ndi mbewu, ndipo mukadzaza moyo wanu ndi Mawu amenewo, amakhala amoyo mwa inu mukayesedwa.
Mwachitsanzo, mawu onena za kuleza mtima. Mawu amenewo akakhala amoyo mwa inu pamene mukuyesedwa kukhala wosaleza mtima, simudzakhala wosaleza mtima. Mungathe kugonjetsa mayeserowo mwa mphamvu ya mawu amene ali mwa inu! Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yotereyi. Muyenera kutembenukira kwa Mulungu ndi Mawu ake m’maganizo mwanu, ndipo mudzaona kuti mudzakhala ndi moyo watsopano wa maganizo; mudzakhala ndi maganizo atsopano! Ndipo maganizo oipawa ndi ovutawa adzakankhidwira kutali kwambiri.
Mavesi angapo othandiza:
“Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola, ndi zinthu zosiririka.” Afilipi 4:8.
“Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima m'njira ya anthu oyipa, kapena kukhala m'magulu a anthu onyoza. Koma chikondwerero chake chili m'malamulo a Yehova ndipo m'malamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. Iye alingati mtengo wodzalidwa m'mbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake munthawi yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.” Masalimo 1:1-3.
“Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musandilole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu. Ndasunga mawu anu mumtima mwanga kuti ndisakuchimwireni!” Salmo 119:9-11.
“Mawu anu ndi nyali ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.” Masalimo 119:105.