Ndinali ndi mayeso omwe ndinayenera kuwakonzekera komanso ndinali ndi zovala zambiri zomwe ndinayenera kuchapa. Ndimafuna kutenga ang’ono anga kukagula zinthu ku sitolo komanso ndinayenera kukathandiza mnzanga amene anali ndi mwana wongobadwa kumene, koma ndinalibe nthawi.
M’malo mokhala pamodzi ndi abale, ndinali ndili kunyumba ndi zovala zochuluka komanso mabuku ambiri. “Ndilibe nthawi yoti ndikhoza kuchita chilichonse chabwino,” ndinaganiza motere. Koma mwadzidzidzi ndinazindikira kuti sindili okondwa kaamba ka nyengo zanga. Ndipo vesi inadza mumtima wanga: “Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye, osati ya anthu.” Akolose 3:23
“Kodi ndikhoza kugwira ntchito yochapa zovala zanga monga ndichitira Ambuye?” Ndinadzifunsa ndekha. “Kodi ndikhoza kugwira ntchito zanga za ku kusukulu monga ndichitira Ambuye?” Ndinadziwa kuti yankho ndi “Inde” chifukwa chilichonse ndingachite zikutanthauza kuti chilichonse ndingachite ndithu. Mmalo modandaula ndi kudzimvera chisoni pamene ndikuchapa zovala, ndikhoza kumapempherera wina wake, kulingalira za mau a Mulungu, kapenanso kuimba nyimbo yondilimbikitsa. M’malo mogwira ntchito ya maphunziro anga monyinyirika, ndikhoza kugwira monga ndingathere ndi kukhala oyamika kuti ndili ndi mwai wa maphunziro.
Izi ndi zinthu zimene ndikhoza kumachita tsiku ndi tsiku kuonetsa chikondi changa pa Mulungu. Zinthu izi ndi “zobisika” m’malingaliro anga. Izi sizingandibweretsere kuyamikiridwa kapena ulemu kuchokera kwa ena, koma zindibweretsera madalitso a Mulungu pa moyo wanga!
Pamene ndikuchapa zovala, Mau a Mulungu akhoza kundidzala ine ndi chimwemwe ndi kundimasula ku moyo wosakhutitsidwa.
Aefeso 6:17-18: “Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mau a Mulungu. Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, m’mitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.”
Ndikapemphera kwa Mulungu kupempha thandizo malinga ndi nyengo zanga, Iye amandipatsa Mau Ake chomwe ndi chida chogonjetsera malingaliro odandaula. Pakuvala Mau a Mulungu monga chida, ndikhoza kukonda ndi kutumikira Mulungu paliponse pamene ndili, ndi chilichonse ndikuchita, ndikhoza kuchita ndi mtima wanga onse monga ndichitira Mulungu!