Ukhoza kumenya nkhondo yolimbana ndi kufooketsedwa motani

Ukhoza kumenya nkhondo yolimbana ndi kufooketsedwa motani

Ndi mavesi amenewa monga zida, sitikuyenera kulolera kugonjetsedwa ndi kufooketsedwa

8/19/202612 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Ukhoza kumenya nkhondo yolimbana ndi kufooketsedwa motani

Kufooketsedwa ndi chinthu chimene timakumana nacho pa moyo wathu wa chikhristu. Ndi “mdani” amene amachedwetsa kukula kwathu ndipo amaba mtendere, chiyembekezo ndi chimwemwe. Uyu ndi mdani amenenso tikhoza kumugonjetsa ngati timvetsetsa ndi kuchita zomwe zalembedwa M’mau a Mulungu. Pali mavesi mu Baibulo amene akhoza kutithandiza kugonjetsa kufooketsedwa- tikungosowekera kuwakhulupirira!    

Tangoganizani kuti pali msilikali amene waitanidwa kukamenya nkhondo ndipo akukonzekera, ndiye maganizo a kukaika, mantha ndi kusadziwa kuti nkhondoyo ikayenda bwanji zamufikira.  “Ine sindine msilikali wabwino ndi oyenera. Ndilibe zondiyenereza.  Ine ndagonjetsedwa kale ndipo ndikuona kuti sizikandiyendera bwino. Palibe amene amasamala za ine. Zotsatira za nkhondoyi sizofunikira kwenikweni.  Nsembeyi ndi yaikulu koposa. Adani ndi ambiri ndipo gulu lawo lankhondo ndi la mphamvu.” 

Pakhoza kukhala njira ziwiri: 

Msilikaliyu akupitirira kukhala ndi maganizo oterewa. Kulimbika mtima kwake kukuyamba kuchepa. “Ine sindine woyenera,” ndipo akuvomereza za izi. “Ineyo sizindithera bwino,” akukhulupirira zimenezi.  “Nkhondo imeneyi tikagonjetsedwa ndithu.”  Sakulabadira zoti anyamule zida zake. Kukaika ndi mantha zamufoola ziwalo zake. Alibe kulimbika ndi mphamvu kuyamba kumenya nkhondo. 

kapena 

Msilikali wakonzekera bwino ndipo akudziwa zoyenera kuchita. Wanyamula lupanga lake (Aefeso 6:17). “Ndili ndi wamkulu wa nkhondo amene ndi wabwino, ndipo ndimamukhulupirira. Iye amandiyang’anira ndipo akandithandiza pa nkhondo imeneyi.” Iye wanyamula chishango chake (Aefeso 6:16).  “Mkulu wanga wankhondo anagonjetsa kale mdani ameneyu, ndipo ine ndichita chimodzimodzi.  Nkhondoyi ndiyofunikira kwambiri ndipo mphotho yake ndi yaikulu.  Ine ndipambana pa nkhondo imeneyi.” 

Mavesi a m’Baibulo ogonjetsera kufooketsedwa- zida zomwe ukuzisowa kuti ugwiritse ntchito 

Zimatengera kugwira ntchito, kutsimikizika ndi kulimbika kuti ukagonjetse kufooketsedwa.  Khala msilikali wabwino ndipo uzingokhulupirira liwu la chiyembekezo.  Limba mtima! Khala wamphamvu! Ika kulimbika mtima kwako pa Yesu, amene ali mkulu wathu wankhondo amene anagonjetsa muzinthu zonse ndipo akutisonyeza momwe ifenso tikhoza kugonjetsera. 

Dzikonzekeretse wekha ndi zida izi mu Mau a Mulungu amene ali odzala ndi choonadi ndi chikhulupiriro. 

Kodi ukadali olemedwa ndi machimo ako akale?  

Ukapempha chikhululukiro moona mtima, Mulungu amatayira machimo ako munyanja yakuya kwambiri, monga momwe mavesi m’Baibulo akunenera. Ngati Mulungu watayira kutali machimo ako, iwenso ukhoza kuchita chimodzimodzi! 

 Mika 7:19: “Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.” 

 1Yohane 1:9: “Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika  ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.”  

Afilipi 3:13: “ Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nkuyiwala za m’mbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili m’tsogolo mwanga.” 

Kodi wagwa mu uchimo? 

Lapa, limba mtima ndipo pitiriza kuyesetsabe kuchita zabwino.  Usalole mtima okayika ndi maganizo ochokera kwa Satana okuuza kuti supambana.  Yesu satopa nafe ndipo amatipempherera kwa Atate amene amatikonda ife mwangwiro.  Mavesi awa a m’Baibulo akutsimikizira za izi: 

Miyambo 24:16: “Paja munthu wolungama akagwa kasanu n’kawiri amadzukiriranso. Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.” 

1 Yohane2:1 “Inu ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate,  Yesu Khristu, Wolungamayo.” 

Aroma 8:33-34 “Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha?  Ndi Mulungu amene amalungamitsa. Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali ku dzanja la manja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.” 

1 Petro 2:20 “Kodi pali choti akuyamukireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira , mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu.” 

 Yakobo 4:7 “Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.” 

Umakhulupirira ndani? 

Satana amabwera ndi mau ofooketsa, okuimba mlandu, ndi maganizo opotoka ndi cholinga choti abe, aphe ndi kuononga chiyembekezo ndi chikhulupiriro chako.  Mulungu amabwera ndi chilimbikitso, thandizo, chitonthozo, chikhulupiriro ndi chiyembekezo. 

Yeremia 29:11 “Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa ayi.  Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za m’tsogolo.” 

2 Timoteo 1:7 “Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.” 

Kodi njirayi ikuoneka yovuta kwambiri ndipo zotsatira zake zikuchedwa? 

Osataya mtima! Ukusowekera chikhulupiriro ndi kudekha kuti ukafikire moyo ogonjetsa.  Pamene ukuyesedwa ndi kofooketsedwa, lolera mavesi awa a m’Baibulo akulimbikitse. 

 Ahebri 10:23 “Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.” 

2 Timoteyo 2:3: “Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu.”  

 Ahebri 10:35-36: “Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.  N’kofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza.”  

Ahebri 12:3: “Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafooke ndi kutaya mtima.” 

Kodi ukumvetsera, kuonera kapena kuwerenga zinthu zomwe zikukuchotsera chiyembekezo? 

Aefeso 5:11: “Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma m’malo mwake muzitsutse.”  

Yeremiya 2:13: “Popeza anthu anga achita machimo awiri: Andisiya Ine kasupe wa madzi a moyo, ndi kukadzikumbira zitsime zawo, zitsime zong’aluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.” 

Kodi ukutenga nthawi yako kulimbikitsa chikhulupiriro chako? 

Aefeso 6:13: “Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loipa kwambiri lifika, mudzathe kuima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzaimabe mwamphamvu.” 

Aroma 10:17: “Motero chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.” 

 Yuda 1:20: “Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.” 

Ahebri 12:12: “N’chifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu agowoka.” 

Kodi mwakumanapo ndi chidzudzulo cha Mulungu pa moyo wanu? 

Mulungu amakusamalirani kwambiri ndipo akufuna kukupulumutsani ku uchimo ndi kukupatsani ulemelero wa chipatso cha Mzimu. Pamene Iye akukudzudzula chimenecho ndi chizindikiro cha chikondi chake pa iwe.  

Ahebri 12:5-6: “…Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula. Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.” 

1 Petro5:6-7: “Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wa mphamvu, kuti panthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.” 

Kodi maganizo opotoka akukupangitsa kuona mdima ndi kusaona moyenera?  

Malingaliro athu akhoza kukhala osakhazikika, koma Mau a Mulungu ali ngati Nthanthwe loona. Mzimu wako ukhoza kuima pamwamba pa kufooketsedwa kuli konse ngakhale kuti m’malingaliro ako uli ofooka. 

Masalimo 61:2: “Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimaitana Inu ndimaitana pomwe mtima wanga ukufowoka: tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ine. 

 1 Yohane 3:20: “Nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa.  Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.” 

Yesaya 40:31 : “Koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.” 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi inakhazikika pa nkhani yomwe analemba ndi Martha Evangelisti imene analimbikitsika kuchokera mu nkhani yomwe mutu wake ndi “Kufooketsedwa” yomwe inalembedwa ndi Elias Aslaksen (imene poyamba inasindikizidwa mu Norwegian ndi Stiftelsen Skjulte Skatters Forlag) ndi BCC Urbana Bible study. Inatsindikizidwa pa https://activechristianity.org/ ndipo yatengedwa ndi chilolezo kuti igwiritsidwe ntchito pa website ino.