N’zotheka kukhala omasulidwa ku uchimo m’moyo uno! Yesu akufuna kuti ophunzira ake akhale ndi moyo wogonjetsa uchimo (Aroma 5:17).
Ufulu ku uchimo kwa amene agonjetsa!
Yesu akufuna kuti tikhale ngati Iye (Aroma 8:29). Aliyense amene amaona ulemerero wa Ambuye amasandulika kukhala chifaniziro chomwecho (2 Akorinto 3:18). Ulemerero wa Yesu ndi moyo wake—moyo wogonjetsa uchimo. Moyo wogonjetsa, umene timalamulira uchimo! Tikamaona ulemerero umenewu ndi kusinthidwa kuti tikhale ngati Iye, timakhala atumiki ndi mizati m’kachisi wa Mulungu.
“Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu Watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.” Chivumbulutso 3:12.
Iye amene wagonjetsa, iye amene wapambana! Yesu akufunafuna anthu ogonjetsa pamene akulembera angelo a mipingo isanu ndi iwiri ya ku Asia Minor. Malonjezo ndi a anthu amene amapambana ndi kumasulidwa ku uchimo. Mphamvu yokhala ndi moyo wogonjetsa imachokera kwa Mzimu Woyera, ndipo Mulungu amapereka Mzimu umenewu kwa aliyense amene amamumvera (Machitidwe a Atumwi 5:32).
Kumasuka ku uchimo ndi chipulumutso chozama kwambiri
Kodi timamasuka bwanji ku uchimo? Ngati timvera zimene Mzimu Woyera amalankhula mumtima mwathu, timalandira mphamvu yonena kuti Ayi ku zilakolako zoipa ndi zikhumbo za uchimo m’thupi mwathu. Yesu anatipatsa mwayi wokhala ndi moyo wogonjetsa uchimo. Moyo umenewu unali wofunika kwambiri kwa Paulo moti anafuula kuti, “Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? Ayi, m’njira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitiriza bwanji kukhalabe m’menemo?” Aroma 6:1-2.
Anthu ambiri amaona chipulumutso ngati chikhululukiro cha machimo okha. Koma chipulumutso chimene chimalalikidwa kudzera mu uthenga wabwino chimapita mozama kwambiri kuposa mmene anthu ambiri amamvetsetsera chipulumutso.
“Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mukondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.” 1 Petro 1:8-9
“*Pakuti pamene Davide anatsiriza kutumikira Mulungu mu m’bado wake, anamwalira, iye anayikidwa m’manda pamodzi ndi makolo ake ndipo thupi lake linawola. Koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa sanawole ayi. N'chifukwa chake, abale anga, dziwani kuti mwa Yesu chikhululukiro cha machimo chikulalikidwa. Kudzera mwa Iye aliyense amene akhulupirira, alungamitsidwa kuchoka ku tchimo lililonse limene silingachoke ndi Malamulo a Mose. Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu: ‘Onani, inu anthu onyoza, dabwani ndipo wonongekani, chifukwa ine ndidzachita china chake m'masiku anu, inu simudzakhulupirira ngakhale wina atakufotokozerani.’” Machitidwe 13:36-41
Mmene mungamasulidwire ku uchimo
Chikhululukiro chokha sichimatimasula ku uchimo. Zotsatira za ntchito imene Mulungu amachita mwa ophunzira Ake n’zakuti okhulupirira angathe kugawana nawo mu moyo Wake wa Mulungu. “Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero Wake ndi ubwino Wake. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili m'dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.” 2 Petro 1:3-4.
Mulungu adzakulimbitsani kwambiri ngati mukuona kuti akukuitanani kuti mukhale wophunzira wodzipereka ndi mtima wonse. Palibe malire pa zimene uthenga wabwino ungachite m’moyo wanu. Tangoganizani kuti mungathe kugawana nawo moyo wa Mulungu mwini—chifundo chake, chikondi chake, chilungamo chake ndi ubwino wake! Umenewo ndi ufulu!
Moyo waulemerero uwu ndi wa ophunzira Ake. Ngati mumva Mulungu akukuitanani, musaumitse mtima wanu, koma tembenukirani kwa Iye ndi kusiya moyo wanu wa m’dziko lino. Pamenepo mudzapeza chiyanjano ndi ena amene akulakalaka moyo womwewo ndi kukula mmenemo!
“Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa.” Mateyu 5:6.