Mu chipangano chakale, anthu amapereka nsembe zomwezomwezo kawirikawiri koma nsembezo sizinathe kuchotsa machimo awo. (Ahebri 10:11) Mwaichi panalibe kukula kapena kupita chitsogolo mmoyo wauzimu mu chipangano cha chakale; koma mu chipangano cha tsopano ndizosiyana kotheratu.
Paulo akuti ku 1 Akorinto 3:16: “Ndinu Nyumba ya Mulungu!” ndipo Petro akulemba: “Pamene mukubwera kwa Iye, amene ali mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, inunso, mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu…” 1 Petro 2:4-5.
Chitani chifuniro cha Mulungu
Yesu ndiye mwala wapangodya, mwala wa maziko. Pakuchita chifuniro cha Mulungu Iye anapangidwa kukhala mwala wa pangodya. Iye atabwera pa dziko lapansi anati, “Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa m’Malemba.” Ahebri 10:7. Timalowa mu pangano latsopano munjira ngati yomweyi. Tsopano ndi pakuchita chifuniro cha Mulungu pamene timaumbudwa kukhala ofanana ndi Khristu. Mu Baibulo zalembedwanso za ife. Timaumbidwa ndi Mau a Mulungu. Yesu anali Mau oululidwa mthupi (1 Timoteo 3:16). Kalelo anamva Mau a Mulungu, koma tsopano anawaona oululidwa mu thupi la Yesu. Iyi ndi ntchito imene Mzimu akugwira ndi wina aliyense wa ife amene walowa mu pangano la tsopano.
“Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsedwa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu m’choonadi.” 2Atesalonika 2:13
Kuyeretsedwa zimatanthauza kuti mkhalidwe wathu ukusandulizidwa kotheratu kuchokera ku umunthu wathu kukhala wa umulungu. Izi sitingathe kupanga patokha, monga momwe mwala sungathe kudzisema kukhala chifanizo. Koma manja a Osema Miyala akhoza kupanga chifanizo kuchokera ku mwala. Izi zili chimodzimodzi ndi Ife. Timawerenga kuti tikuyenera kuyeretsedwa ndi Mzimu. Mwa chikhulupiriro mwa Khristu tinalandira Mzimu amene analonjezedwa. Ndiye tsopano lino “miyala” yonse yomwe yakhala ikusautsika kuti iziseme yokha kukhala “mafanizo”, ikhoza kusinthidwa ndi manja a Mmisili wosema miyala.
Khala ofanana ndi Yesu
Yesu ndiye chifanizo chenicheni chosasinthika, ndipo ndi thandizo la Mzimu tikusinthidwa kuti tikhale monga Iye- kukhala miyala yamoyo. Mzimu amagwira nafe ntchito malinga ndi Mau a Mulungu kuti tikhoza kukhala ofanana ndi mavesi awa: “Musagonjetsedwe ndi choipa, koma mugonjetse choipa pakuchita chabwino.” “Adalitseni, ndipo osawatemberera.” “Asapezeke wina ongofuna zomukomera yekha, komanso zokomera mnansi wake,” kapena “Iye amene ali wamkulu pakati panu adzakhala wotumikira ndi kapolo wa onse,”
Ife ndife nyumba ya Mulungu; ndipo ngati tikufuna kumangidwa mooneka bwino tiyenera kubwera kwa Yesu, amene ali chifanizo chenicheni. Tisalolere kusemedwa ndi bambo kapena mayi, mbale, mlongo, kapena magazini a dziko lapansi. Komanso tisalolere kulamulidwa ndi mzimu wa dziko lapansi wa nthawi ino. Tikuyenera tibwere kwa Iye, Mwala wa Moyo, umene unakanidwa ndi anthu koma unasankhidwa ndipo ndi wa mtengowapatali pamaso pa Mulungu. (1Petro 2:4-5).
Lero lino kuli amisili ochuluka amene akusema anthu kuti akhale mchifanizo cha chipani chawo kapena gulu lawo la chipembedzo. Onse amene akufuna akhale otchuka ndi ololeredwa ndi dera lomwe amakhala.
Komatu nzosatheka kuloleredwa kumwamba komanso padziko lapansi. Ife amene talowa mu pangano latsopano kuti tipangidwe miyala ya moyo mu nyumba ya Mulungu tivomere kuti tidzakanidwa ndi anthu tikamachita chifuniro cha Mulungu.
Sunga lamulo mopanda banga ndi cholakwa
Apa tikuona momwe Paulo akuonera ndi chidwi ichi: “Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera.” 1 Timoteyo 6:12-14
Zimatanthauza chiyani kusunga lamulo mopanda cholakwa? Zikutanthauza kuti sukusintha lamulo kuti ligwirizane ndi nyengo zako; kuti kumvetsetsa kwanga kwa lamulo sikukutsogoleredwa ndi nzeru za mmabuku zatsopano. Ife tikuyenera kuumbidwa malinga ndi malamulo- malamulo amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake asanapite kumwamba. (Machitidwe a Atumwi 1:2)
Miyala ya nyumba ya Mulungu yakhala iukudulidwa ndi kusemedwa mu mibado yonse, ndipo onse adzalumikizana pamodzi kukhala kachisi pamene Yesu abweranso. Lero aliyense wa ife akuumbidwa kudzera mu nyengo zake, pakuchita chifuniro cha Mulungu. Koma tsiku likudza pamene tonse tidzalumikizana pamodzi popanda kumva hamala ikugwira ntchito, monga momwe kachisi wa Solomoni panthawi yomwe amamangidwa. (1 Mafumu 6:7).
Kodi ngati iwo amene agwira ntchito limodzi ndi Mulungu akhala akusintha lamulo malinga ndi mzimu womwe ukulamulira umene akhalamo, mukuganiza kuti miyala yosemedwayo mu zaka 2000 zimenezi ikanatha kugwira ntchito moyenera? Yesu sanasinthe, ndipo Mzimu wakhala chimodzimodzi mu zaka 2000 zonsezi; ngati lamulo likanasungidwa mopanda cholakwa, miyalayi ikanatha kugwiritsidwa ntchito mwangwiro.
Mwala oyenera mu nyumba ya Mulungu
Apa tikutha kumvetsetsa chifukwa chimene Paulo alimbikitsa Timoteyo kwambiri za kusunga lamulo popanda cholakwa kufikira Yesu atabweranso. Akumulimbikitsa kotheratu pamaso pa Mulungu, amene amapereka moyo ku zinthu zonse, ndi pamaso pa Yesu Khristu, amene anachitira umboni wabwino. Umboni wake unali wa kuti Ufumu Wake sunali wa pansi pano. Timoteyo akuyenera kubwera kwa Iye, mwala wa moyo, ndi kulowa mu pangano, ndikuyeretsedwa ndi mwazi wa Yesu Khristu.
Paulo akumukumbutsanso kuti iye wachitiranso umboni wabwino pamaso pa mboni zambiri, ndipo kuti iye anabatizidwa ndi kufunafuna zinthu za kumwamba kumene kuli Yesu, osati zinthu za padziko. Ndipo tsopano akumuza Timoteyo kuti “Menya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuitanira…”
Usadzidetse ndi mzimu umene ukulamulira nthawi ino, sunga lamulo ndi chiyero chonse. Chita chifuniro cha Mulungu. Ndipo udzakhala mwala woyenera mu nyumba ya Mulungu pamene Yesu akadzabwera.