Kodi M’khristu akhoza kutaya chipulumutso chake?

Kodi M’khristu akhoza kutaya chipulumutso chake?

10/19/2026—4 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Kodi M’khristu akhoza kutaya chipulumutso chake?

M’khristu amakhala ndi chikhumbo chotumikira Mulungu.  Ichi chimakhala chiyambi cha chipulumutso chake, koma kodi chipulumutso chimenechi chikhoza kutayika?

Tikupulumutsidwa ndi chisomo chokhacho, ndipo ichi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.  Koma ndizotheka kutaya chipulumutso chako ngati M’khristu?

Kodi Chipulumutso ndi chiyani?

Pamene tafika popereka moyo wathu kotheratu kwa Mulungu ndi kukhala M’khristu, timalandira mtima watsopano, ndi kaganizidwe katsopano.  Mtima wathu wakale umangodzitumikira tokha ndi zilakolako ndi zikhumbitso zake - koma mtima watsopano ndi wakuti utumikire Mulungu ndi kuchita zomukondweretsa Iye.  Ichi ndi chiyambi chabe cha chipulumutso chathu pamene machimo athu akhululukidwa ndipo talandira mtima watsopano. Komabe tikusowekera kupulumutsidwa kwakukulu-  tikuyenera kupulumutsidwa ku zizolowezi zathu zoipa zimene zili mu umunthu wathu, kuti tikakhale ofanana ndi Khristu ( Aroma 8:29)

Paulo akulemba ku Aroma 6:6 “Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye…..”  Nkofunika kwambiri kudziwa ichi.  Ifetu sikuti tinangolandira kukhululukidwa kwa machimo kokha ayi kudzera mu imfa ya Yesu pa mtanda paja, koma kuti umunthu wathu wakale unapachikidwanso naye limodzi.  Ichi ndi chimene chimapangitsa moyo wathu kukapulumutsidwa mwakuya ndi kuyamba kukhala moyo watsopano. (Aroma 6:4)

Izi ndi zimene Paulo akulankhula ku Aefeso 4: 22-24: “…kuchotsa umunthu wanu wakale, umene ukupitirira kuonongeka ndi zilakolako za chinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano m’mitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero”.  Umunthu wanga wakale ndi mtima wanga wakale (umene umafuna kuchita zimene ine ndikufuna, ndi zilakolako ndi zikhumbitso zimene zili mu mkhalidwe wanga wokonda kuchita zoipa). Umunthu wanga watsopano ndi mtima watsopano umene ufuna kutumikira Mulungu ndi kuchita zomukondweretsa.

Mtanda - Mphamvu ya chipulumutso

Paulo akulemba ku Afilipi 3:17-19: “Abale nonsenu pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira.  Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri m’mbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu.  Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo.  Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi.”

Iwowa sanali adani a mtanda pamene amalandira chikhululukiro cha machimo awo kudzera mwa Yesu ngati nsembe, koma anakhala adani a mtanda pamene anadziwitsidwa kuti umunthu wawo wakale ukuyenera kupachikidwa ndi Khristu.  Iwowa nkutheka kuti anafika popereka moyo wawo kotheratu ndi kulandira mtima watsopano, koma zachisoni, anabwereranso ku mtima wawo wakale nayambanso kukonda za dziko lapansi.

Timawerenga ku 2 Timoteo 3:5 za anthu amene anali nawo maonekedwe a chipembedzo koma anaikana mphamvu yake.  Mphamvu ya chipembedzo imagonera mu Mtanda, chifukwa ndi Mtandawo umene uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa. (Aroma 1:16)  Ndi mtandawo umene umagwira umunthu wathu wakale kukhala opachikidwa pa mtanda kuti tikakule mu moyo watsopano - ndi kulandira mochulukira moyo wa Khristu.  Kuzizimbaitsa kuti timakonda Mulungu koma kumbali ndi kumakondabe za dziko lapansi ndi zilakolako zake, izi ndi zolakwika kwambiri pamaso pa Mulungu.  Ichi ndi chiphamaso chimene Yesu anayankhula motsutsana nacho kwambiri.  (Luka 12:1)

Ndizotheka kutaya chipulumutso chako?

Mwa ichi, chipulumutso chonse - ku mbali zonse ziwiri pa kukhululukidwa kwa machimo, komanso pakumutsata Yesu pa njira ya mtanda pamene zilakolako zathu zimakhala zopachikidwa pa mtanda- zonse zimatheka mwa chisomo chake.   Timayamba ndi mphatso yaulere ya kukhululukidwa kwa machimo- zikatha izi pali njira mu mapazi ake a Yesu, pamene amatipatsa chisomo chakuyenda munjirayi. Njira imeneyi imatsegukira kwa amene ali ophunzira ake a Yesu - iwo amene akufuna kumutsata Iye ndi kukhala ndi mtima omwe Iye anali nawo. (Afilipi 2: 5-8,  1 Petro 4:1).  Kudzera mu chisomo ndi thandizo zimene Iye amatipatsa, timagonjetsa monga Iye anagonjetsa. (Ahebri 4: 15-16)  Ichi ndicho chipulumutso chenicheni. Koma ndizotheka kutaya chipulumutso chimenechi?

Apa zikuonekeratu kuti ngati tibwerera ku mtima wathu wakale ndi kuyambanso kukonda za dziko lapansi ndi zilakolako zake, ndiye kuti tataya chipulumutso chathu.  Mtima wotere ulibe malo mu Ufumu wakumwamba.  Koma ngati tilapa moona mtima ndi kutembenukiranso kwa Mulungu, tikhoza kutenganso chipulumutso chathu kachiwiri, koma tikhala kuti tataya nthawi ya mtengo wapatali imene tikadatha kulandira mochuluka moyo wa Khristu mwa ife.  Mwa ichi tiyeni tipitirire kuyenda mumtima watsopanowu ndipo osachokamonso.

“Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Mbuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo, ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike m’chikhulupiriro…”. Akolose 2: 6-7.

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi yalembedwa kuchokera mu nkhani yomwe analemba ndi Tom Harris yomwe inatsindikizidwa pa https://activechristianity.org/ ndipo yakhazikitsidwa ndi chilolezo pa website iyi.