Senzani mtanda wanu tsiku ndi tsiku: Wophunzira aliyense ayenera kuchita izi
"Yesu anauza aliyense kuti: "Onse ofuna kubwera pambuyo panga ayenera kudzikaniza okha, kusenza mtanda wawo tsiku ndi tsiku, ndi kunditsatira.'" Luka 9:23.
Kodi Yesu akutanthauza chiyani pamene Iye akunena kuti muyenera kusenza mtanda wanu tsiku ndi tsiku?
"Kusenza mtanda wanu" ndi chinthu chimene mumachita m'maganizo mwanu. Pamene malingaliro omwe sali okondweretsa Mulungu abwera , muyenera "kuwapha" pa "mtanda" wamkati mwanu.
Mwinamwake lingaliro loweruza kwa bwenzi lanu limabwera, kapena mwinamwake lingaliro la kudandaula. Malingaliro amenewa akangobwera m'maganizo mwanu, mumasankha kunena kuti "ayi" kwa iwo. Maganizo anu amayang'anitsitsa pakhomo la mtima wanu, ndipo mumasankha zimene mumalola kuloŵa mumtima mwanu. Pamene lingaliro lauchimo libwera m'maganizo mwanu nthawi yoyamba, ndi chiyeso chabe - "lingaliro" kapena "choyesa" chochokera kwa Satana. Koma mukhoza kusankha kusalola lingaliro limenelo kuloŵa mumtima mwanu! Pochita zimenezo zikutanthauza kuti mwalizindikira lingalirolo ndiposimukugwirizana nalo. Simukupitiriza kuganiza za izo. Lingaliro lotere limakumana ndi "Aayi" wolimba m'maganizo mwanu. Simulola kuti lingalirolo lidutse ndi kulowa mumtima mwanu. Kunena kuti "Ayi" ku malingaliro ochimwa awa ndi momwe mumasenzera mtanda wanu tsiku ndi tsiku.
Kuvutika mu "thupi la uchimo" – kuthana ndi tchimo!
Zimakhala zowawa pamene uchitazotsutsana ndi zomwe umakonda mwachibadwa - kunena kuti "Ayi" ku malingaliro omwe mwachibadwa mungaganize. Monga momwe Munthu akhoza kumva ululu pokhomedwa pa mtanda , "mtanda wamkatiwu" umabweretsanso ululu ku "thupi la uchimo" lanu, lomwe ndi khalidwe lanu lokonda kuchita zoipa, gawo lla inu lomwe limakonda kuchimwa ndipo tsopano silingathe kuchita zomwe likufuna . Mwa ichi muli ndi chifukwa chabwino chosankhira kusachimwa, ndipo ndicho chimene chalembedwa pa 1 Petro 4:1:
"Choncho, popeza Khristu anavutika chifukwa cha ife m'thupi, dzikonzekeretseninso ndi maganizo amodzimodziwo, pakuti iye amene wavutika m'thupi waleka [kuima ndi] uchimo."
Ndimeyiikulonjeza kuti mukavutika m'thupi lanu, kutanthauza kuti mukasenza mtanda wanu ndi kunena kuti "Ayi" ku malingaliro ochimwa omwe amabwera mwa inu, mudzasiyadi tchimo limenelo! Ndipo si lonjezo chabe lomwe lidzakwaniritsidwa tsiku lina kutali mtsogolo –ayi, koma kuti mudzayamba kuona kusintha pamenemukupitirira kuchita izi.
Mwinamwake kaŵirikaŵiri mumakhala waukali ndi wosagwirizana ndi abwenzi anu. Mukamanena kuti "Ayi" nthawi iliyonse maganizo oipa okhudza anzanu abwera, mudzaona pakupita kwa nthawi kuti maganizo amenewo sabweranso nthawi zambiri. Zikatere zimakhala zosavuta kuti mukhale abwino, odekha komanso okoma mtima kwa anthu omwe akuzungulirani. Pamenepo lonjezo likukwaniritsidwa - mukukhala omasuka ku uchimo m'dera limenelo!
Kutsatira Yesu: Kodi Yesu anachita chiyani?
Izi ndi zomwe zimatanthauza kukhala wophunzira wa Yesu. Ndi za moyo umene umakhala tsiku ndi tsiku, kumtsatira Yesu. Kodi Yesu anachitanji m'moyo Wake wa tsiku ndi tsiku? Iye anali atapanga chisankho chovuta pasadakhale chochita pamene Iye anayesedwa: "Osati chifuniro Changa, koma chifuniro chanu chiyenera kuchitidwa." Luka 22:42. Iye "anasenza mtanda Wake" ndipo anati "ayi" pamene Iye anayesedwa. Mayesero ake sanathetsedwe mu uchimo - m'mawu, m'maganizo, kapena m'zochita.
Kwalembedwanso kuti Yesu "... anapemphera ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene akanam'pulumutsa ku imfa." Ahebri 5:7. Ichi ndi chimene chikufunika -kusenza mtanda wanu mokhulupirika tsiku ndi tsiku! Muyenera kufuula kwa Mulungu wanu kuti mulandire mphamvu zokuthandizani nthawi zonse kunena kuti "kayi" ndikupitiriza kunena kuti "kayi" pamene mukuyesedwa. Muyenera kudzichepetsa ndi kukhala ndi maganizo ofanana ndi amene Yesu anali nawo: "Osati chifuniro changa, koma chifuniro chanu chiyenera kuchitidwa."
Kusenza mtanda wanu tsiku ndi tsiku kumakutengera ku kusinthika kwathunthu kwa moyo. Simudzakhala nthawi zonse munthu yemweyo amene muli lero. Pamene mukuyeretsedwa ku tchimo m'chilengedwe chanu, zipatso za Mzimu zimabwera m'malo mwake. M'malo mofulumira kuweruza ndi kusuliza, kapena kukwiya ndi kumva kukhala wopanda chiyembekezo, mungakhale wodzala ndi chikondi ndi kukoma mtima. (Agalatiya 5:22-23.) Kodi zimenezo si chiyembekezo?
"Osati kuti ndapeza kale izi kapena ndili kale wangwiro, koma ndikukakamiza kuti zikhale zanga, chifukwa Khristu Yesu wandipanga ine wake." Afilipi 3:12.