Nthawi yoyamba mwatsopano
Kodi moyo wa m'maganizo ako ndi wofanana ndi wa “Mkhristu wabwino” amene aliyense amaona kunja?
Sizovuta kwambiri kupangitsa anthu ena kukhulupirira kuti umakhala moyo wabwino wa Chikhristu. M'moyo wakunja n’kosavuta kukhala wachifundo, owolowa manja ndi wodzichepetsa. Koma zili bwanji mu moyo wa m'maganizo ako? Kodi ndiwe wachifundo ndi wodzichepetsa kumeneko? Kodi ukhoza kuchita manyazi ngati anthu atatha kuona zimene ukuganiza?
Ndikutsimikiza kuti ungapereke zifukwa zambiri zosonyeza chifukwa chimene wakhala ukuchimwira pamene palibe amene akukuona. Koma uyenera kuyamba kukhala woona mtima kwenikweni ndi moyo wako womwe. Zimapweteka kuvomereza choonadi, koma choonadi chili ndi mphamvu yayikulu yokumasula ku mphamvu za chidetso, mkwiyo ndi machimo ena onse amene angakumange moyo wako wonse. Yakwana nthawi yolapa. Koma ndingachite bwanji zimenezo?
Vomereza kuti ukufunika thandizo
Ngati ukufuna kulapa, uyenera kudzichepetsa wekha. Khala wochepa kwambiri m’maso mwako moti udzione monga munthu amene ulili: wosauka ndi womvetsa chisoni, munthu amene akufunika thandizo.
“Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi, akutero Yehova. Ng’ambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu.” Yoweli 2:12-13.
Anthu ambiri sakhala moyo wabwino wa Chikhristu m’maganizo awo. Koma suyenera kukhalabe choncho. “Ng’amba mtima wako, osati zovala zako!” Fuulira Mulungu kuchokera pansi pa mtima wako! Ichi ndi chochitika choyamba cha kulapa, kuti uvomereze pamaso pa Mulungu momwe zinthu zilili ndi iwe. Mwina uyenera kuvomereza kuti suli woyera ndi wopatulika monga anzako amaganizira.
Vomereza tchimo lako kwa Mulungu
“Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve. Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.” Yesaya 59:1-2.
Machimo ako akulekanitsa ndi Mulungu! Kuti ukonze moyo wako, uyenera kuuza Mulungu zonse, osasiya chilichonse. Ngati pali tchimo limene ukufuna kubisa, sudzamasuka kwathunthu ku machimo ako akale. Izi ndi zofunika kwambiri!
Koma ngati utsegula mtima wako kwa Mulungu ndi kuvomereza tchimo lililonse limene likusautsa chikumbumtima chako, ndiye kuti Iye adzawakhululukira, monga momwe timawerengera mu Masalimo 32:5: “Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, ‘Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova,’ ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.”
Iye amakukhululukira! Kenako umamva mpumulo waukulu kuchokera ku kumva kutsutsika kumene kunali nawe nthawi zonse. Umamva chimwemwe chakuti Mulungu saganiziranso za machimowo. Kenako umatsimikiza kuti watengedwa kuchokera mumdima kupita ku kuunika, kuchokera ku mphamvu ya Satana kubwerera kwa Mulungu! Chinthu chokhacho chimene chingakulepheretse kulandira mphatso yaulemerero imeneyi ndi ngati sukhululukira ena. Koma ukadzawona chifundo cha Mulungu pa iwe, utaziona potsiriza kuti ndiwe wosauka ndi womvetsa chisoni, ungalephere bwanji kukhululukira ena?
Pambuyo pa chikhululukiro …
Koma chotsatira ndi chiyani? Machimo ako akhululukidwa, koma mkati mwako ukuopa kwambiri kuti mwina ungabwerere ku moyo wa “kuchimwa ndi kukhululukidwa” mobwerezabwereza. Umenewo si ufulu; pamenepo udakali kapolo wa tchimo! Koma kodi Mulungu akufuna chotsatira chotani kwa iwe? Ngati ukhala chete pamaso pa Mulungu, Iye adzakuuzadi zimene akufuna kuti uchite.
Mulungu wakukhululukira; ndipo pobwezera, akukupempha kuti usinthe moyo wako. Adzakusonyeza zinthu zimene uyenera kukonza ndi anthu ena, zizolowezi zimene uyenera kusiya, anthu ena amene uyenera kusiya kucheza nawo, ndi matsamba aintaneti, mabuku, kapena zinthu zina zimene uyenera kupewa.
“Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.” Yesaya 55:7.
Yamba kupemphera. Umuuze Yesu zonse zokhudza chikhumbo chako chofuna kumasulidwadi ku machimo amene akumanga kwa nthawi yaitali. Pempherera mphamvu yosunga mtima wako ngati kachisi wa Mulungu mwa kunena kuti “ayi” pa mayesero! Dzaza mtima ndi maganizo ako ndi zinthu zimene zimakuthandiza pa nkhondo yako yofuna kukhala woyera. Usalole aliyense kukulanda njala ndi ludzu latsopano limene uli nalo, limene zosangalatsa za dziko lino sizingakhutitse.
Ukasunga ubwenzi wako wapamtima ndi Yesu m’pemphero, adzakupatsa mphamvu kuti uzitha kukhala nthawi yonse yotsala padziko lapansi uli womasuka ku uchimo. Izi ndi zimene kulapa kumatanthauza. Izi ndi zimene kukhala wophunzira wa Yesu kumatanthauza—maitanidwe akulu kwambiri amene munthu aliyense angafune, ndi chisankho chimene sudzanong’oneza nacho bondo.