Mdima wauzimu ukukulirakulira pa dziko lapansi, ndipo chimene tiyenera kuchita tichite kukadali masana. Ife sindife aku mdima kapena ausiku. Ife ndife ana a kuwala komanso a masana. (1 Atesalonika 5:5)
Ife ndife ziwalo za thupi la Khristu, ndipo Iye mwini ndiye mutu. Chilichonse chomwe Iye afuna kulankhula ndi kuchita mu nthawi zino, Iye alankhule ndi kuchita kudzera mu matupi athu, amene aperekedwa kuchita chifuniro Chake.
Tikuyenera kudziwa udindo wathu mu nkhondo yolimba ndi mphamvu za ku mdima. Tikuyenera kudziwa za maitanidwe athu akulu ndi oyera monga ana a kuwala, ndipo tisakayike konse kuti tigonjetsa choipacho. (2 Timoteo 1:9) Tikuyenera kukhala kutali ndi chilichonse cha maonekedwe a kumdima. Ndi zida za kuwala nthawi zonse tidzagonjetsa. Tikuyenera tidziveke tokha ndi Mzimu wa Khristu ndi makhalidwe a Khristu pamene tikulimba ndi Satana, mu njira iliyonse imene akudzionetsera.
Pali mphamvu zazikulu za uzimu zochokera ku ufumu wa Satana, ndipo mizimu yoipayi imagwira anthu. Chinthu chimene chili choyenera ndi chabwino chikuzilala, koma zoipa ndi zosalungama zikukulirakulira mphamvu. Chikondi chimene chimamanga anthu amene akwatirana pamodzi mukukhulupirika kwa wina ndi mnzake mpaka imfa, kwafika pozillala. M’malo mwake, kudzimva kochokera kwa Satana kwabwera kumene kukuwononga mabanja posaganizira zowawa zomwe ana akukumana nazo.
Tikuyenera kugwira ntchito moposa kale mu Mzimu wa Khristu amene amalumikizanitsa chilichonse chimene chili choyenera ndi chabwino - mu Mzimu amene ali ndi mphamvu yogonjetsa chilichonse chomwe chimabwera kuchokera ku mphamvu zoipa.
Mzimu waphamvu koposa amene abwera kuchokera ku mpando wa Mulungu ndi Mwana wa Nkhosa (Chibvumbulutso 22:1) ndi umene umapereka mtendere wamuyaya ndi chimwemwe, umenewu sungagonjetsedwe. Kuwala kumagonjetsa mdima, ndipo chikondi chimagonjetsa udani. Tikuyenera kudziwa pomwe taima ndi chomwe tikumenyera nkhondo. Kodi timayanjana ndi mphamvu za kuwala kapena ndi mphamvu za kumdima?