Dziko lodzala ndi ziwawa ndi nkhanza. Kodi ndingatani kuti ndithandize?

Dziko lodzala ndi ziwawa ndi nkhanza. Kodi ndingatani kuti ndithandize?

Mndandanda wa zinthu zimene sindingathe kuchita ndi wosatha. Koma ndikhoza kuchita mbali yaing'ono yomwe ili patsogolo panga.

2/18/20254 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Dziko lodzala ndi ziwawa ndi nkhanza. Kodi ndingatani kuti ndithandize?

Kuntchito, mnzanga wina wogwira naye ntchito analowa mu ofesi. Zinaonekeratu mwamsanga kuti iye anali kukumana ndi nkhanza za mmbanja m'nyumba mwake. Ine ndi mnzanga wina tinamupititsa ku polisi, ndipo pambuyo pake ku khoti la Magistrate lakumaloko. Pambuyo pa maola ambiri tikudikirira m'mizere ndi kulankhula ndi akuluakulu a boma, tinachoka m'nyumbayo ndi pepala lokha lolembedwa 'chitetezo'. Ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinaona ngati nangotaya nthawi. 

Pamene tinali kuchoka m'nyumbayo, mkazi amene anamenyedwayo ananditembenukira, nkhope yake ikuwala ndi mpumulo ndi chimwemwe, ndipo anati, "poyamba ndinalibe kalikonse, koma tsopano ndili nacho china chake ." Tili m'galimoto popita kunyumba, anatithokoza kwambiri chifukwa chomuthandiza ndipo anati " ine sindili oyenera kuthandizidwa motere ndipo sindili kanthu". 

Mawu amenewa animba belu m'mutu mwanga. Kodi munthu angaganize bwanji mozichepetsa kwambiri za iye mwini mpaka kumaziona kuti sali woyenera kukhala ndi pepala la 'chitetezo'? Chiŵerengero chimene ndinaŵerenga ponena za nkhanza za m'banja mwadzidzidzi chinapatsa tanthauzo latsopano. Kuona kuvutika ndi kuzunzika kiozungulira dera lathu kunali kodabwitsa. N'zovuta kuona kuti munthu amene umamukonda ndi kusamala za iye akunzidwa, koma kwa ine kuti ndimvetse za mchitidwe umenewu mmene umakhudzira umunthu ndi wawo zinali zodabwitsa kwambiri 

Koma ndingatani tsopano? Kodi ndingathandize bwanji? 


Mndandanda wa zinthu zomwe sindingathe kuchita ndi wosatha. Sindingathe kumupatsa malo abwino okhala. Sindingathe kulipira chitetezo. Sindingathe kuthandiza ndi ndalama zachipatala kapena kupereka uphungu. Ndipo ngakhale nditathandiza munthu mmodzi mwanjira imeneyi, kodi zingapangitse kusiyana kotani pamene pali anthu aunyinji ambiri ofunikira thandizo? 

 
Ndinapita kunyumba tsiku limenelo nditataya mtima. 

Madzulo amenewo ndinapemphera kwa Mulungu wanga, ndipo ndinalandira yankho. 

 
Zalembedwa kuti, "Osati chifuniro changa, koma Chanu chichitike." Kumeneko ndiko kudzipereka kwaumwini kumene ndinapanga pamene ndinapereka moyo wanga kwa Yesu. Zimenezo zikutanthauza kuti ndi Mulungu amene ayenera kusankha zimene ndiyenera kuchita kapena zimene sindiyenera kuchita. Zalembedwa pa Aefeso 2:10 (GW): "Mulungu watipanga ife zimene tili. Iye watilenga mwa Khristu Yesu kuti tikhale ndi moyo wodzazidwa ndi ntchito zabwino zimene watikonzekeretsa kuti tichite." Pali zinthu zimene Mulungu wandikonzekeretsa kuti ndichite padziko lapansi. Izi ndi zinthu zimene ndiyenera kunena ndi kuchita. Zinthu zomwe zingathe kunenedwa ndi kuchitidwa ndi ine kwa anthu omwe ndimakumana nawo m'moyo wanga. Mwinamwake sizidzasintha m'njira imene ndikuyembekezera kapena kufuna, koma ntchito zimenezi zinasankhidwa mwangwiro ndi Mulungu kaamba ka ine mogwirizana ndi chifuniro Chake. 

Ndiyenera kuchita zomwe zili zoyenera pamaso panga 

Zonse zomwe ndiyenera kuchita ndi zomwe zili zoyenera pamaso panga, ndipo chilichonse kunja kwa izo si zaine koma za Mulungu - osati kuti ndide nazo nkhawa! 

Tsopano ndili ndi mpumulo ndi mtendere mumtima mwanga. Mulungu ananditsogolera mu mkhalidwe umenewu, ndipo ndinali wokhoza kuthandiza m'njira imene Mulungu anafuna kuti ndichite. Ndikadachita zomwe ndikufuna, tikanaloŵa ndi kutseka munthu yemwe adavulaza mnzathu wogwira naye ntchito. M'malo mwake, Mulungu ananditsogolera m'njira yosiyana kotheratu. Popanda ngakhale kuzindikira panthaŵiyo, ndinali wokhoza kusonyeza chikondi ndi chilimbikitso, mwa kungomupititsa ku polisi. Zimenezi zinam'sonyeza kuti ndi wofunika kwambiri. 

Dziko ladzala ndi ziwawa, ndipo mchitidwe wa upanduukumachitika tsiku ndi tsiku. Ndikhoza kupempherera dziko langa, ndikuti adindo oyang'anira athe kusintha zinthu bwino, kuti dongosolo loikidwa lingateteze ndi kuthandiza anthu olimba mtima kuti alankhule zovuta zomwe akukumana nazo. 

Koma nanga ndikhumudwe ndi kutaya mtima chifukwa chakuti mbali yanga ndi yaing'ono yoit sibweretsa zotsatirazimene ndikufuna? Chimenecho chikhala chipongwe kwa Mulungu ndi chochititsa manyazi ku maitanidwe anga kumwamba. 

Mulungu wandikonzera zinthu zoti ndichite. Ngati ndine wa Iye, ndiye kuti cholinga changa padziko lino lapansi ndicho kukhala maso kuti ndithandize m'njira iliyonse yaing'ono yomwe Mulungu amagwira ntchito mumtima mwanga, mu nyengo iliwonse imene ndingakumane nayo. Mwanjira imeneyi, ndine mbali ya kuthetsa ziwawa ndi nkhanza m'dzikoli. 

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhaniyi yalembedwa ndi Elizabeth Turner ku ActiveChristianity.africa