Pamene wina anafunsa Yesu za kuthekera kwa kuchuluka kwa omwe adzapulumutsidwe, Iye sanayankhe mwa chindunji koma anati: “Yesetsani kulowa pakhomo lopapatiza.” Luka 13:24. Kuchokera apa tikumvetsa kuti iwo amene apulumutsidwa ndi omwe adutsa pa khomo lopapatiza.
Kodi khomo lopapatiza ndi chiyani? Zikutanthauza kupereka zako zonse za pa dziko ndi kudana ndi moyo wanga womwe ( chifuniro changa) pa dziko pano. Tikhoza kuwerenga za izi ku Luka 14: 26-33 ndi Yohane 12:25.
Aneneri onyenga ndi chipata chotakata
Yesu analankhulanso za chipata chopapatiza ku Mateyu 7: 13-14. Apa analankhula za zipata ziwiri ndi njira ziwiri: Chipata chopapatiza ndi njira yovuta yopita ku moyo, komanso ndi chipata chotakata ndi njira yaikulu yopita ku chionongeko. Ambiri amakhulupirira kuti njira yotakata ndi dziko lapansi, ndipo kuti iwo amene ayenda pa njirayi ndi anthu osakhulupirira. Komatu zikuonekeratu kuti Yesu akulankhula ndi anthu amene afunafuna kulowa mu ufumu wa kumwamba: “Lowani kudzera pa chipata chopapatiza,” Iye akutero ku Mateyu 7:13. Ndipo pa ndime ya 15 Iye akutichenjeza za aneneri onyenga.
Aneneri onyenga akuyitana anthu kuti alowe kudzera pa chipata chotakata, pamene sukusowekera kupereka zako zonse kuti upulumutsidwe. Iwo akufuna kuti iweyo ukhulupirire kuti ndi zotheka kutumikira Mulungu komanso chuma (zomwe ndi ndalama, chuma), koma Yesu akunena mwa chimvekere kuti izi ndi zosatheka (Mateyu 6:24), ndipo mapeto ake ndi chionongeko.
Tikuyenera kutenga chenjezo la Yesu lokhudza aneneri onyenga ndi chidwi chachikulu pa mtima pathu, pachifukwa chakuti pakhala pali aneneri onyenga ochuluka, koma aneneri owona ndi ochepa. Pamene mfumu Yehosafati amafuna kudziwa ngati kunali koyenera kuti apite akamenye nkhondo kapena ayi, panali aneneri onyenga 400 ndipo mneneri owona analipo mmodzi (2 Mbiri 18)
Ndipo Paulo anachitira umboni, “Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira mau a Mulungu kuti tipeza phindu. M’malo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.” 2 Akorinto 2:17. Anthu awa akufunafuna phindu la iwo eni, ndiye ndikofunika kwa iwo kuti apange chipatachi kukhala chotakata kuti apeze anthu ochuluka mumipingo yawo.
Khalani opulumutsidwa pakulowa pa chipata chopapatiza
Ndikuyenera kuchita chilichonse kuti ndilowe kudzera pa chipata chopapatiza, chifukwa chakuti malinga ndi khalidwe la umunthu wanga ndimafuna kusunga moyo wanga, kuchita zofuna zanga padziko pano, koma kumafunanabe kukhala M’khristu. Ndikuyenera kuchita chilichonse kusunga malamulo ake a Yesu. Ndikamachita izi, ndimayamba kuona kuipa kwa mkhalidwe wa umunthu wanga umene umapangitsa kumvera malamulo a Yesu kukhala chinthu chovuta: ndiye ndimakayamba kudana nacho ichi, kenaka “ndimayamba kudana ndi moyo wanga womwe.”
Pamene ndalowa kudzera pa chipata chopapatiza, pali chinthu chimodzi chomwe ndifuna ndicho kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kumukondweretsa Iye. Ndikudana ndi moyo wanga ndi chifuniro changa mu dziko lino lapansi, ndipo ine ndathana nalo dziko lapansi. Lilibe kalikonse komwe likhoza kundipatsa ndipo sindikufuna kalikonse ka ilo.
Mwa ichi ndikhoza kupita chitsogolo pa njira yopapatizayi ndi kunena limodzi ndi Paulo: “Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, n’kuyiwala zam’mbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili m’tsogolo mwanga. Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.” Afilipi 3: 13-14. Pamene ndikhala ndi mtima wotere, ndikhoza kukhala otsimikizika kuti ndapulumutsidwa.