Amai mwa Khristu: Mwai wosaneneka

Amai mwa Khristu: Mwai wosaneneka

Amai onse akhoza kukhala amai mwa Khristu

1/19/20264 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Amai mwa Khristu: Mwai wosaneneka

Amai mwa Khristu

Tonse tawerenga mu Baibulo za amai omwe anali zitsanzo za zomwe tikhoza kufikira ngati tapereka miyoyo yathu kwathunthu mmanja mwa Mulungu. Amai omwe amaonetsa kuti moyo woukhala malinga ndi mau a Mulungu ndi moyo umene umakutsogolera ku kusangalala kwenikweni, chimwemwe, mtendere ndi mpumulo. Moyo wokhala wokhutitsidwa ndi wochititsa chidwi. Moyo umene wagonjetsa zovuta, wasuntha malire, wakhazikitsa maziko, walimbana ndi ululu ndi masautso, ndipo wakhala opambana nthawi zonse mwa Khristu. ( 2Akorinto 2:14). Amai amenewa anali atsogoleri a uzimu, amai, alongo, agogo, adzakhali ndi anzawo etc.

Mwa chisomo cha Mulungu pa miyoyo yathu, tonse tikhoza kukhala amai mwa Khristu.

Zilibe kanthu kuti nyengo zako ndi zotani, ngati uli kunyumba, pakati pa abale ndi alongo, kapena ku ntchito, pokhala mkhristu wa chizimayi mwai wako ndi wosaneneka mkati mwa chifuniro cha Mulungu pa iweyo. Koma tisakakamize maganizo athu pa zimene tikufuna kufikira. “Mmalo mwake, tifunefune chifuniro cha Mulungu, ndikugwiritsa ntchito mphamvu ndi nthawi yathu yonse kuti chifuniro chake chichitike pansi pano monga kulili kumwamba, kudzera mmoyo wathu.’’ (Mateyu 6:10.)

Kufunafuna nzeru yochokera kumwamba

Pali zinthu zambiri zimene timalimbana nazo ndi kutangwanika nazo, ndipo palinso nthawi zambiri pamene kusalungama kukuyenera kugonjetsedwa mmiyoyo yathu, ku ntchito, kapena kusukulu. Tikusowekera nzeru za momwe tikhoza kuchitira izi molondola. Ngati tikhoza kungonena ndi kuchita zimene ife eni tikuganiza kuti ndi zolondola, sitingathe kuchita mwachilungamo..(Yakobo 1:19-20).  Ngati tifuna thandizo, tiyeni tifunefune nzeru zimene zili zochokera kumwamba.

“Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.’’ Yakobo 3:17

Mulungu ali ndi ntchito yosiyana kwa mayi aliyense. Kaya ntchitoyo ndiyotani, tikuyenera kuichita ndi kudzichepetsa konse ndi nzeru.  Tisakhale odzimva ndi kuganiza kuti timadziwa bwino, koma muzimene timachita tichite chifukwa tikudziwa kuti izi ndi zimene Mulungu akutifunsa kuti tichite.

Nzeru zimatanthauza kuti “kuupeza moyo wako ndi kuutaya.”( Mateyu 10:39)  Izi zikutanthauza kuti mu nyengo iliyonse ndikuyenera kunena Ayi ku zochitika zochokera mu mkhalidwe wanga wokonda kuchita zoipa, ndikuchita chifuniro cha Mulungu mmalo mwake.  Pamenepo tsono tikhoza kuyamba kuona nyengo zonse monga Mulungu akuzionera, osati monga mwa kumvetsetsa kwa umunthu wanga.  Timapeza nzeru zomwe tizisowa pakufunafuna Mulungu, osati kufunafuna za ife eni.

“Nzeru ndi yabwino kupambana zida za nkhondo, koma wochimwa mmodzi amaononga zinthu zambiri zabwino.” Mlaliki 9:18

“Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu, adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka; kuopa Yehova ngati madalitso.” Yesaya 33:6

Chikhristu chokhazikika pa Mau a Mulungu

Chikhristu chomwe ndichokhazikika pa Mau a Mulungu, osati pa maganizo a anthu, chimakutsogolera ku chilungamo chenicheni ndipo sichisankha.  Chikhristu chimayenera kusonyeza ubwino wa Khristu, zipatso za Mzimu.  Chikondi, chimwemwe, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, kukhulupirika, kudekha, kudziletsa ( Agalatiya 5:22-23).  Zilibe kanthu kuti ndiwe ndani, ngati ufuna kupeza moyo umenewu umene ukhoza kukula mu zipatso za Mzimu, ndiye kuti moyo wako udzakhala chitsanzo cha Chilungamo.  

 Ngati Mkhristu ali ndi chipatso cha Mzimu ngati maziko a moyo wake, sakhalanso odana ndi ena, wozunza ndi odzikweza, ndipo sapondereza munthu aliyense.  Chikhristu chimandipatsa kulimbika mtima, monga tiwerenga ku Afilipi 4:13 komwe akunena kuti ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Khristu amene amandipatsa mphamvu; izi zimandipatsa mphamvu ndi kundithandiza ndekha kuti ndisakhale o

Palibe aliyense amene wafika pa ungwiro mu zipatso za Mzimu, koma tikhoza kulankhula limodzi ndi Paulo: “Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiitanira.” Afilipi 3:12.  Ichi ndicho cholinga cha ophunzira wa Yesu.

Dziko lapansi likadakhala kuti linazipereka ku moyo wa Chikhristu oona, ndiye kuti mavuto onse a padziko lapansi monga kuyang’anirana pansi, kuzunzana, kusankhana, kudana, etc zikadakhala zitatha.

Tsono iyi ndi ntchito ya wina aliyense.  Menya nkhondo, choyamba mu moyo wako omwe ndi nyengo zake, pa chilichonse chimene ufumu wakumwamba umapititsa patsogolo: chilungamo, chikondi, kulemekeza ena, mtendere, chimwemwe etc.  Khalani kuwala mu dziko la mdima ndi kuonetsa momwe mphamvu ya Mulungu imagwirira ntchito mwa iwo akuchita chifuniro chake. Tiyeni tonse tikhale Amai mwa Khristu.

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi inatsamira pa nkhani yolembedwa ndi Kate Kohl ndipo inatsindikizidwa mu https://activechristianity.org/ ndipo ndi chilolezo imaikidwa pa website iyi.