Wotumidwa monga mtumiki wa Mulungu

Wotumidwa monga mtumiki wa Mulungu

Pamene Mulungu anatuma mwana wake ku dziko lapansi kudzakhala Mpulumutsi wathu, Iye anamutuma ngati mtumiki.

10/21/2026—2 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

Wotumidwa monga mtumiki wa Mulungu

Mneneri Yesaya akulemba kuti: “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, amene ndinamusankha, amenenso ndimakondwera naye,” Yesaya 42:1

Potumikira Atate Ake, Yesu nayenso anakhala mtumiki wathu. Ukhoza kuganiza kuti Iye amene Mulungu adamutuma kukhala Mpulumutsi wathu ndi Mfumu yathu akanakhoza kufika mu ulemero waukulu kuti dziko lapansi liwone kuti iye ndi ndani ndipo wabwera kudzakwaniritsa chiyani. Koma Baibulo likuti, “Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.” Afilipi 2:7.   

 Umunthu wathu womwe tinabadwa nawo ndi wodzikonda, ndipo anthu amaganiza kuti ngati ena awatumikira ndi kuwasamalira bwino, ndiye kuti adzakhala okondwera. Koma chisangalalo chenicheni chili ndi thanthauzo lake lakuya kuposa ili.  Yesu anati, “Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.” Luka 22:27.  Iye anaonetsa ichi muchitsanzo cha Iye mwini.  Ndipo Iye akunenanso za Iye mwini, “Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”Mateyu 20:28

Yesu sanatumikire ena ndi cholinga choti iwo amupatse ulemu, koma ndi chifukwa chakuti Iye anawakonda onse.  Iye anasankha kutumikira iwo amene analibe kalikonse koti akanatha kumubwezera, monga ana aang’ono, olumala ndi akhungu, akhate ndi osalidwa. Onse anatha kubwera pamodzi kwa Iye kudzatonthozedwa ndi kuchiritsidwa.  Yesu anatumikira chifukwa anawakonda anthu, osati chifukwa anali oyenera.  

 Sibwino kutumikira ndi kuchitira ena zabwino  omwe tikuganiza kuti akuyenera.  Yesu anakonda kuchita zolungama, koma anadana nacho chosalungama, ndi chifukwa chake Mulungu anamudzodza Iye “wakukwezani kuposa anzanu pokudzodzani mafuta osonyeza chimwemwe,” monga Baibulo linena ku Ahebri 1:9.  Mwanjira ina, Iye anali munthu wosangalala kwambiri kuposa anthu onse apa dziko!

 Tsopano ndi nthawi yathu, tili ndi mwayi wotsatira Yesu mu mapazi ake ndi kutumikira ena mwa chikondi. (1 Petro 2:21; Agalatiya 5:13-14). Ngati ife tikonda ndi kutumukira Mulungu, Iye adzatiwonetsera momwe tikhoza kutumikira anthu anzathu.

Positi iyi ikupezekanso ku

This article is based on an article by Helen Simons originally published on https://activechristianity.org/ and has been adapted with permission for use on this website. Nkhani iyi ikuchokera pa nkhani ya Helen Simons yomwe inatsindikizidwa koyamba pa https://activechristianity.org/ ndipo ikugwiritsidwa ntchito  ndi chilolezo pa website iyi.