“Pita kwa nyerere, mlesi iwe; kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu.” Miyambo 6:6.
Khalani ochitachita
Nyerere zimamanga chulu chawo m’njira yabwino kwambiri kuti zizikhala motentha. Dzuwa likangotuluka, nyerere zimayamba kugwira ntchito. Njira zonse za nyerere zimapita ku chulu; nyerere iliyonse imagwira ntchito mmene ingathere. Ngati kamtengo ndi kakukulu kwambiri kwa nyerere imodzi, zina zimabwera kudzathandiza kukanyamula kupita nako ku chulu.
Kukhala wopanda kugwira ntchito kumabweretsa ulesi, ndipo ulesi umabweretsa kusowa. Yang’anani mmene nyerere zimagwirira ntchito. Choyamba zachilengedwe, kenako zauzimu. “Zilibe mfumu, zilibe woyang’anira kapena wolamulira, komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.” Miyambo 6:7-8.
Gwira ntchito molimbika
Ndi m'dalitso kugwira ntchito ndi manja anu ndi kugwira ntchito mwa mzimu. Pali chakudya chochuluka m’minda yosalimidwa ya osauka. Anamwali opusa anapempha mafuta kwa anamwali anzeru. Limenelo ndi tsogolo la anthu aulesi. Pamapeto pake amapempha. Anamwali opusa sanasonkhanitse mafuta m’zotengera zawo. Anali aulesi. Pamafunika khama kuti usonkhanitse chakudya, monga timanenera, ndipo khama lofananalo limafunikanso kuti usonkhanitse chakudya chauzimu. Kwa munthu waulesi, ntchito imamveka ngati mdani wamphamvu; imamveka ngati temberero losatheka kuligonjetsa—ndipo amenewo ndi maganizo oipa kwambiri!
Pa misonkhano yathu, palinso anthu amene, tikalankhula mwauzimu, sakhala ndi chilichonse chopereka. Amangofuna kulandira. Amangotsegula pakamwa pawo ngati ana a mbalame, kuyembekezera kuti ena awadyetse. Izi zimakhala zomvetsetseka poyamba pamene munthu akadali mwana muuzimu; koma ngati zili choncho panthawi imene munthu ayenera kukhala wokhoza kuphunzitsa ena, sizikhala zoyenera.
Chulu cha nyerere ndi kachisi
Mu mpingo, njira zonse zimatsogoleranso ku “chulu cha nyerere”—ndiko kuti, ku kachisi wauzimu amene akumangidwa; pakuti tikumangidwa pamodzi ndi ena kukhala malo okhalamo Mulungu mwa Mzimu (Aefeso 2:22). Zinthu zonse zichitike kuti zilimbikitse ndi kumanga. Khalani achangu pomanga ufumu wa Mulungu. Ngati “ndodo” ndi yolemetsa kwambiri kwa m’bale wanu, pitani mukamuthandize kuinyamula. Si aliyense amene ndi mtumiki wa Mawu, koma aliyense akhoza kukhala mtumiki wa Mulungu pamene kachisi akuyenera kumangidwa. Tilibe wolamulira, woyang’anira kapena mfumu, monga mmene nyerere zilibe, komabe ntchito imachitika mwamsanga. Onse amamanga mogwirizana ndi mphamvu ndi chilimbikitso chochokera mkati. Ndi mmene ziyenera kukhalira.
“Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti, mlesi iwe? Kodi tulo tako tidzatha liti? Kugona pang’ono, kuwodzera pang’ono, kupinda manja pang’ono kuti upumule, ndipo umphawi udzakugwera ngati mbala, ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.” Miyambo 6:9-11.