N’chifukwa chiyani kukhulupirira kumakhala kovuta?

N’chifukwa chiyani kukhulupirira kumakhala kovuta?

Unayamba waganizapo kuti, “Sindikhulupirira Mau a Mulungu; izi ndizosatheka!”

11/18/2026—3 mphindi

Ndi Moyo wa Chikirisitu Wochitachita

N’chifukwa chiyani kukhulupirira kumakhala kovuta?

Kodi aliyense akhoza kulandira chikhulupiriro?

Yesu akunena ku Mateyu 23:37, “…kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsa ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!”

Yesu amayang’ana kufunitsitsa kwawo pamene Iye amafuna kusonkhanitsa anthu a Israeli, koma ambiri samafuna, sanafune kukhulupirira.

Izi zili chimodzimodzi lero. Mwa chifundo Chake, Yesu akutiyitana kudzera ku Mau a Mulungu kuti tibwere kwa Iye, koma funso ndi lakuti tili ofuna kuwakhulupirira Mauwo?

Sikukufunikira kukhala ochenjera kuti ukakhulupirire kapena kukhala ndi chikhulupiriro; ndipo chikhulupiriro sichikungoperekedwa kwa owerengeka apadera ndi anthu auzimu.  Wina aliyense wa ife akhoza kulandira chikhulupiriro ndi kupanga chisankho kuti adzikhala mu ichi.  Chikhulupiriro ndi nkhani ya kumvera, chikhulupiriro chimatanthauza kuchita zimene Mulungu atiuza kuti tichite. (Aroma 1:5 ndi 16:26)

Koma n’chifukwa chiyani kukhulupirira kumakhala kovuta?

 Tikhoza kuwerenga zomwe Baibulo litiuza za anthu a Israeli muchipululu.  Mulungu anawalonjeza Dziko lamalonjezano, dziko loyenda mkaka ndi uchi.  Iwo anaona zodabwitsa za Mulungu ndipo Iye anawathandiza nthawi zambiri; koma iwo anatayika muchipululu kwa zaka 40. Awiri okha mwa iwo amene anachoka ku Aigupto ndi amene analowa m’dzikolo.  Aliyense amene anali ndi zaka zoposa 20 anafa osalowa mudziko lolonjezedwalo, chifukwa sanakhulupirire. (Ahebri 3:19)  Iwo sanakhulupirire kuti Mulungu akhoza kuwathandiza kugonjetsa dziko la Akanani.

N’chifukwa chiyani iwo sanakhulupirire  Mulungu kuti akhoza kukwaniritsa malonjezo Ake?

Ichi chinali kusafuna kwawo kumenya nkhondo ndi adani m’dzikolo omwe amaoneka kuti anali amphamvu kuposa iwo;  sanafune kumenya nkhondo ndi kumva zowawa kuti alandire zimene Mulungu anawalonjeza.

Ngati ndasankha kukhulupirira kuti Mau a Mulungu ndi owona, ndikuyenera kukhalanso ofuna kuchita zimene zalembedwa mu Mauwo.  Chikhulupiriro chowona chimatanthauza kuchita zimene zalembedwa m’Mau a Mulungu, ndipo apa ndikuyenera kukhala ofuna kumvera ndipo osabwerera m’mbuyo.  Izi zindilowetsa “munkhondo” pamene nditaya chifuniro changa kuti ndichite chifuniro cha Mulungu.  Koma chomwe ndilandire monga mphotho kaamba ka kukhulupirika kwanga ndi chachikulu, monga kwalembedwa ku Chibvumbulutso 3:21, “Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.”   

 Kwa anthu ambiri, chimaoneka chinthu chopusa pakukhulupirira kuti lonjezo lidzakwaniritsidwa pa iwe.  Koma zoona zake ndi zakuti pakukhala ndi chikhulupiriro choona pa vesi imeneyi ikhoza kukutsogolera ku moyo osangalala ndi wachiyembekezo cha ulemerero wamuyaya pamodzi ndiYesu.    

Funso limodzi lokha ndi lakuti ngati ndili ofuna kukhulupirira ndi ofuna kumvera!

Ndikhoza kupanga chiganizochi tsopano lino. Chikhoza kuyamba ndi pemphero lozavuta, “Ambuye Mulungu, thandizeni ine kukhulupirira mwa Inu.”

Mulungu amakhala ofunitsitsa kwa anthu amene apanga ziganizo za kukhulupirira mwa Iye ndi zimene Iye analonjeza.  Iye adzalimbikitsa chifuniro chako pa kuchita zabwino.  Pamene umvera Mau Ake mochulukira, mochulukiranso chikhulupiriro chako chimalandira mphamvu ndipo sizivutanso kukhala omvera Iye.

Positi iyi ikupezekanso ku

Nkhani iyi ikuchokera pankhani ya Karina Schytt yomwe inatsindikizidwa pa https://activechristianity.org/  ndipo ikugwira ntchito ndi chilolezo pa website iyi.