Yesu atauka kwa akufa ndi kupita kumwamba, ophunzirawo anasonkhana m’nyumba yaikulu ku Yerusalemu. Mwadzidzidzi anamva phokoso lalikulu lochokera kumwamba, ngati mphepo yamphamvu, ndipo linadzaza nyumba yonse. Ophunzirawo anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo analandira mphamvu yaikulu. Tangoganizirani za Petro amene, pasanapite nthawi yaitali, anakana kuti amamudziwa Yesu. Tsopano anayima ku Yerusalemu ndipo analankhula molimba mtima za Yesu. Zimene ananena zinali zogwira mtima kwambiri moti anthu 3,000 anatembenuka tsiku lomwelo. Machitidwe a Atumwi 2.
Pa tsiku limenelo, Petro anakhala munthu watsopano. Mwadzidzidzi anakhala wolimba mtima. Analandira Mzimu Woyera ngati “injini” yamphamvu mkati mwake. Timawerenga ku Aroma 8:14-15 kuti, “Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti mudzikhala a mantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, "Abba, Atate."
Tingagwiritse ntchito chitsanzo cha galimoto. Magalimoto ali ndi injini zowayendetsa kupita patsogolo, osati m’misewu yosavuta yokha, komanso kukwera mapiri otsetsereka. Mzimu Woyera ndi chimodzimodzi—uli ngati injini yamphamvu. Mkhristu asanalandire Mzimu Woyera, mungamuyerekezere ndi galimoto yopanda injini. Zimamuvuta kukhala wolimba mtima ndi kulankhula za Yesu. Alibe mphamvu yomuyendetsa m’moyo wake wa Chikhristu. Zimaoneka ngati ena ayenera kumukankha kuti achite chilichonse.
Ngati mukufuna kukhala ndi “injini” yamphamvu mkati mwanu, tsatirani malangizo a Petro: Iye akunena kuti Mzimu Woyera amaperekedwa kwa onse amene amamvera Mulungu. (Machitidwe a Atumwi 5:32). Ngati mukufuna kukhala moyo wa Chikhristu wolimba mtima, wopambana, yesani izi! Mverani mavesi a m’Baibulo amene mukuwadziwa. Kenako mudzadzazidwa ndi Mzimu Woyera. Ngakhale mutakumana ndi “mapiri otsetsereka” m’moyo wanu, injini yamphamvu imeneyi idzayendetsa galimotoyo kukwera ndi kufika pamwamba pa phirilo. Mudzapita patsogolo ndipo simudzaletseka.