Kupikisana kungakhale chinthu chachikulu kwa achinyamata (ndipo mwina kwa achikulire nawonso). Kukhala “wabwino kwambiri.” Kukhala ndi nthabwala zoseketsa kwambiri, kugoletsa zigoli zambiri kwambiri, kukhala ndi maphunziro abwino kwambiri, ndi zina zotero. Amafuna kukhala abwino kwambiri pa chilichonse chimene akuchita. Kodi njira yoyenera yowonera zimenezi ndi iti monga Mkhristu amene akufuna kukhala moyo ndi mtima wonse kwa Mulungu?
Mukupikisana pa chiyani?
Si chinthu choipa kukhala ndi mpikisano. Ndi bwino kudzipangira zolinga, kuchita zonse zimene mungathe, kapena kukhala ndi mipikisano yaubwenzi kuti mudziyese nokha.
Koma dziyeseni nokha. N’chifukwa chiyani mukuchita zimenezi? Chifukwa cha kunyada, kapena nsanje, kapena umbombo, kapena kudzikonda? Chifukwa chakuti mumasamala kwambiri za zimene anthu amakuganizirani? Onetsetsani kuti zochita zanu sizikulamulidwa ndi zilakolako zauchimo! Pamene tikugwira ntchito mwakhama kuti tikhale abwino kwambiri, kodi tiyenera kupondaponda ena kuti tichite zimenezo? Monga mmene zilili ndi zina zonse, tiyenera kufufuza ngati pali tchimo kumbuyo kwa zochita zathu, ndipo ngati lilipo, tiyenera kuliyeretsa.
“Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira” Akolose 3:12.
N’chifukwa chiyani chilichonse chiyenera kukhala mpikisano?
Nthawi zambiri, kufuna kupikisana kumachokera pa kudziona ngati sitili abwino mokwanira. Timafuna kutsimikizira, ngakhale kwa ife eni, kuti ndife abwino kwambiri pa chinthu china kuti timve ngati tili ndi phindu. Chifukwa china chingakhale kudzikuza.
Chowonadi ndi chakuti pali chinthu chimodzi chokha chimene tiyenera kutsimikizira m’moyo, ndipo ndicho chakuti timakonda Khristu ndi mtima wathu wonse. “Koma zonse zimene ndinkaziyesa za phindu, tsopano ndikuziona n'zosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjezera pamenepo, ndikuziona zonse kuti n'zopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. N'chifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu.” Afilipi 3:7-8.
Kodi tingaphunzire kuona zinthu zonse — kuphatikizapo dzina lathu labwino, mmene anthu amationera, ndi kudzikonda kwathu — ngati zopanda pake ndi zinyalala poyerekeza ndi ukulu wa kumudziwa Khristu? Kodi ndi chiyani chimene chingakhale ndi mtengo woposa umenewo?
Usalole tchimo kukukakamiza. Sikuti uyenera “kukhala” munthu winawake. Sizofunika zimene anthu amaganiza za iwe potengera mmene ulili wabwino ndi zimene wakwaniritsa. Chofunika n’chakuti titha kuima pamaso pa Mulungu ndi kudziwa kuti tilibe tchimo pa chikumbumtima chathu. Kuti ndife oyera ndi opanda cholakwa. Zimenezi zidzatipatsa mtengo weniweni mu ufumu wakumwamba.
“Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.” Mateyu 23:12.
Kodi njira ina ndi iti?
Nayi njira ya m’Baibulo imene ndi yoyenera kwambiri kupikisana nayo:
“Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamnga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho. Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota.” 1 Akorinto 9:24-25.
Kodi mumaona korona wosatha ngati chinthu choyenera kupezedwa zivute zitani? Chitani zinthu zonse kuchokera mumtima mwanu monga kwa Ambuye, m’njira yosalola kunyada, kudzikonda, ndi zina zotero kukhala ndi moyo! Pezani pamene mwadzazidwa ndi kufunafuna zofuna zanu ndi kunyada, ndipo gonjetsani zimenezo; m’malo mwake funirani ena zabwino. Funafunani kukhala opambana pa zinthu zofunika kwenikweni. Funafunani kukhala “opambana” pakukhala odzichepetsa mumtima. Chitani zonse zimene mumachita kuti Mulungu alemekezedwe ndipo uchimo ugonjetsedwe.
Kodi sizingakhale zodabwitsa ngati titapikisana kukhala ndi chipatso cha Mzimu Woyera chochuluka kwambiri? Kukhala odzichepetsa kwambiri, osadzikonda kwambiri, ndi zina zotero? Dziko limenelo likanakhala lodabwitsa bwanji, aliyense akupikisana kuti akhale wofanana kwambiri ndi Khristu!
“Musachite kalikonse ndi mtima wodzikonda chabe kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma aliyense azifuna zokomeranso ena.” Afilipi 2:3-4.
Kodi mudzatha bwanji kukhala moyo wotere?
Mudzafika ku moyo woterewu pokhapokha popempha Mulungu kuti akusonyezeni kumene mukukhala moyo wodzikondera nokha, kumene kuli uchimo kumbuyo kwa zimene mumachita. Mukamawerenga Mawu a Mulungu, Iye angakusonyezeni njira yoyenera yochitira zinthu, kuti mumvetse chifuniro Chake ndi kukhala molingana nacho. Mwa kukhala woona mtima pa zolinga zanu, kuvomereza choonadi chokhudza inu nokha, kuweruza uchimo monga mmene ulili kwenikweni, kudana ndi kusalungama ndi kukugonjetsa. Mwa kuchita mwachidwi mavesi amenewo a ku Afilipi m’moyo wanu.
Kodi zotsatira zake ndi zotani?
Kumene zochita zanu kale zinkakhudzidwa ndi kunyada ndi kudzikonda, tsopano mungathe kutumikira ndi kudalitsa ena. Chuma chanu chili kumwamba m’malo mokhala mu zinthu za padziko lapansi; ndipo kusowa kwanu chidaliro, ndi malingaliro onse oipawo sizilinso kanthu mukaziyerekeza ndi chimene mukukhala: mukukhala mwana wa Mulungu, wokonzekera mokwanira ntchito zabwino. (2 Timoteo 3:17).
Pamenepo anthu adzaona ubwino wa Khristu kuchokera m'moyo wanu. Mumakhala kuwala m'dziko lino. Mungathe kuchita zonse zimene mumachita, opanda kunyada ndi kudzikonda! Umunthu wanu umayeretsedwa ku uchimo, ndipo mungathe kuchita chilichonse mumzimu wabwino, ndi zotsatira zabwino zimene zimamanga chiyanjano ndi kupanga ubale wodala, woyera ndi ena popanda zofuna zanu zokha kulowa pakati panu.