Mulungu ndiye Mlengi ndi Mtsogoleri wathu. Chifuniro chake, monga chinaululidwa kudzera mwa Yesu Khristu, sichichepa mphamvu kapena kusuluka. Malonjezano a Mulungu amene ali amuyaya ali oona ndi ofunikira lero lino monga momwe analili nthawi zonse.
“Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.”Agalatiya 6:8. Ngati uchoka pa njira ya moyo woopa Mulungu, posakhalitsa ulowa ndi kusokera mu mdima wa malingaliro ako omwe. Zikatero umayamba kukhulupirira kuti zimene umaganiza, kulankhula, ndi kuchita zinali zoyenera kuchita ndi kulankhula, koma osadziwa kuti ukulimbana ndi Mulungu ndi chifuniro chake.
Ndi kukula mtima ndi koopysa kuganiza kotere. Umadziika wekha ndi maganizo ako pamwamba pa maganizo a Mulungu. Chifukwa chochitira zotere ndi chakuti umaopa zimene anthu azakuganizira. Umagonjera ku maganizidwe ndi kachitidwe ka zinthu lero. Kachitidwe ka Umunthu kamalowa mmalo a malamulo a Mulungu. Kukula mtima kumalowa mmalo a kuzichepetsa ndiye umaganiza kuti ndiwe odziwa kwambiri kuposa Baibulo. Pamene wina akuuza kuti izi sizoyenera, umanena kuti “usaweruze!”. Koma suzindikira kuti iwenso umaweruza ndi kutsutsa iwo amene afuna kuchita mawu a Mulungu.
Ku Aroma mutu 1 ndi 3, timawerenga momwe kuipa kwathu kulili malinga ndi mkhalidwe wathu woipa wa umunthu. Izi zili chomwechi chifukwa anthu anayamba kulambira chilengedwe kuposa Wolengayo. (Aroma 1:25) Paulo anafika pomanga mkota motere: “ndipo njira ya mtendere sayidziwa. Saopa Mulungu ndi pang’ono pomwe.” Aroma 3:17-18.
Pamene anthu asowekera kuopa Mulungu, izi zimabweretsa maonekedwe a chikhistu chimene chimakhala chosamva, chokanika, chkhutitsidwa ndi zomwe akuchita koma popanda kukula mu uzimu komanso chomangolimbana ndi zoipa za ena.
Moyo woopa Mulungu weniweni nthawi zonse umakhala “otsogola,” nthawi zonse umakhala ofunikira tsopano lino. Uli ndi malonjezano amuyaya. Kwalembedwa kuti kuopa Mulungu ndiye chiyambi chanzeru (Miyambo 1:7). Ndi chinthu cha nzeru kukonda ndi kulambira Mulungu ndi kuchita chifuniro chake.
Kuopa Mulungu kumatipangitsa kukhala anthu omwe akhoza kupewa kuganiza monga dziko lapansi lichitira. Kuopa Mulungu kumatipangitsa kukhala ochitachita ndi wodzala ndi mphamvu, anthu amene amaima pa maziko a choonadi monga kwalembedwa mu Mawu a Mulungu. Kuopa Mulungu kumatipangitsa kukhala okhuzidwa ndi odzipereka nsembe omwe akugwira ntchito kuthandiza ndi kukhala abwino kwa anthu anzathu.