Kwa akhristu ambiri chikhulupiriro chimatanthauza kukhulupirira Mulungu, mukukhululukidwa kwa machimo, ndipo kuti adzapita kumwamba. Koma ili ndi gawo limodzi lokha la chikhulupiriro. Ngati tiwerenga ku Yakobo 2, tiona kuti chikhulupiriro chimatanthauza zambiri zoposa.
. “Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? Kodi mukuona kuti chikhulupiriro chimagwira ntchito limodzi ndi ntchito zake, ndipo pakudzera mu ntchitozo chikhulupiriro chinakhala cha ngwiro? Pakuti thupi popanda mzimu ndi lakufa, choncho chikhulupiriro chopanda ntchito ndi chakufanso.” Yakobo 2:21-22, 26.
Kunena kuti ndili ndi chikhulupiriro ndi nkhani ina, ndipo kuti ukachionetsere chikhulupirirocho ndi nkhani inanso yosiyana. Ngati chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa, tikuyenera kugwira ntchito molimbika kuti “chikhulupiriro chathu chikhale changwiro,” kuti tikhale ndi chikhulupiriro cha moyo. Nyengo iliyonse ndi mwai wathu otithandiza kuti tigwire ntchito, ngakhale tikuyesedwa kunena bodza tikhoza kunena zoona, kapena kukomera mtima munthu amene tikudzimva mkati mwathu kuti “sakuyenera”.
Kugwira ntchito ndi moyo wathu zikutanthauza kuti pamene tikuyesedwa, tidzinena kuti “Ayi” kwa Satana ndi kunena kuti “Inde” kwa Mulungu ndi kuchita zimene Mulungu atiuza kuti tichite. Ili ndi gawo lachiwiri la chikhulupiriro.
Koma tikhoza kuima bwanji mu chikhulupiriro mu zinthu zonse zomwe timakumana nazo mu moyo?
Chidwi chathu tiike mu zinthu zakumwamba
Mwina mwafika popanga chisankho chakuti chikhristu ndiye moyo wanu. Mumakhulupirira Mulungu, mumapita ku tchalitchi,mukufunitsitsa kukhala munthu wabwino. Koma pakupita pa nthawi umazindikira kuti kusunga malamulo ake a Mulungu sikophweka monga momwe umaganizira, ndipo kuchita zimene Baibulo linena sizitheka monga mwa chibadwa chathu.
”Mudzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.”Akolose 3:2
Pokhala akhristu, chiyembekezo chathu ndi chakuti tidzakwatulidwa ndi kukhala mmoyo wamuyaya pamodzi ndi Yesu. Pamene tapanga chisankho chofuna kukhala okhulupirika kwa Mulungu, cholinga chimenechi chidzikhala choyambirira pa zonse. Tikatere tidzapeza phindu lamuyaya munyengo zonse zomwe tingakumanane nazo, ndipo tidzayamba kuona chomwe tikulimbana nacho pamene tikuyesedwa kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. Kenaka sitidzanamizidwa pa kuganiza kuti china chake choposa chikhoza kutibweretsera chimwemwe koposa kuchita chifuniro cha Mulungu mu nyengo zonse.
Nchifukwa chiyani anthu amataya chikhulupiriro, kapena chiyembekezo chotere? Ndi chifukwa chakuti chidwi chawo chimachoka pa cholinga chawo cha kumwamba. Chidwi chawo chachoka ndipo chalunjika ku zinthu za pa dziko monga zolinga zawo za dziko lapansi, maloto, ndalama ndi zina zotere. Zinthu izi pa zokha sizolakwika ayi. Zimakhala zolakwika pamene zitengedwa kukhala zofunika kuposa maitanidwe athu akumwamba. Pamene afunafuna zinthu zapansi pano, anthu ambiri amaiwala kotheratu za maitanidwe awo a kumwamba. Zotsatira zake safunanso Mulungu mu moyo wawo. Maganizo awo salunjikanso ku zinthu za kumwamba.
Ngati sitionetsetsa kulunjikitsa maganizo athu ku cholinga cha kumwamba, pamakhala danga lopanda kanthu limene limakadzadzidwa ndi zinthu za padziko pano. Koma tikadzadza maganizo athu ndi zinthu za kumwamba, kukhala moyo ndi Mulungu chimakhala chinthu chofunikira kwambiri kwa ife, ndipo zotsatira zake timachita chilichonse kuti tikhale okhulupirika munyengo zonse za moyo.
Tikufunikira Mulungu
“Ife timakhala mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.”2 Akorinto 5:7
Mulungu akufuna kutiika pa muyeso mu moyo wathu umene sitingathe kukhala opanda chikhulupiriro mwa Iye. Munyengo zovuta pamene zinthu sizikuyenda mmene timayembekezera, komanso munyengo zabwino pamene zinthu zikuyenda malinga ndi mmene timafunira. Pamene tikukhala mu moyo, timayamba kuzindikira kuti sitingathe kufikira cholinga chathu cha kumwamba popanda thandizo lochokera kwa Mulungu.
Kwa anthu ena, izi zimamvetsetseka bwino atayesera ndi mphamvu zawo kufuna kugonjetsa uchimo mmoyo wawo, ndipo sizinatheke. Kwa ena, zimatengera nyengo yaikulu kuti akaone izi. Mwa njira iliyonse, aliyense wa ife akuyenera kuzindikira ichi, kuti ine ndikufunika Mulungu mu moyo wanga.
Tikafika pozindikira kuti chikhulupiriro chathu pa Mulungu ndi chinthu chokhacho cha mtengowapatali, ndipo palibe chilichonse chimene chikhoza kutilanda ichi. Tidzakumana ndi nyengo iliyonse ndi mphamvu ya Mulungu ndipo tidzakhala asilikali a Khristu omenya nkhondo molimbika ndi osagonjera ku uchimo. Tidzakhala omasulidwa ku uchimo, ndipo zotsatira zake chikhulupiriro chathu chidzakulirakulira mphamvu.
“Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.” Ahebri 10:23