Tengani mtanda wanu

Pamene mtanda umatchulidwa m’Baibulo, nthawi zambiri sutanthauza mtanda weniweni wamtengo, kupatulapo pofotokoza za kupachikidwa kwa Yesu pa Kalvare. “Kunyamula mtanda wako” kukutanthauza mtanda wophiphiritsa umene Yesu amalankhula pa Luka 9:23. “Kusenza mtanda wako” ndiko kukana maganizo ochimwa amene amabwera mwa inu ndi kuwapha. Akolose 3:5 . Agalatiya 5:24 .