Ntchito za thupi

Tchimo lachodziwadziwa; zinthu zimene tikudziwa kuti ndi tchimo koma timazichitabe. Zimenezi si za "ngozi" koma uchimo wadala, ndipo ayenera kulapa ndi “kutaya” pa kutembenuka: “Tsopano ntchito za thupi zionekera, ndizo: chigololo, dama, chidetso, chiwerewere, kupembedza mafano, nyanga, udani, mikangano, nsanje, kupsa mtima; zolambana, magawano, mipatuko, kaduka, kuphana, kuledzera, maphwando, ndi zina zotere; zimene ndikuuzani kale, monganso ndinakuuzani kale, kuti iwo akucita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Agalatiya 5:19-21 . ( Akolose 3:5-9 )