Mpando wa chifumu wa Chisomo

“Chotero tiyeni tifike molimbika mtima ku mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza pa nthawi yakusowa. Ahebri 4:16 . Chifukwa chakuti Yesu anayesedwa, koma sanachimwe, nkotheka kwa ife kufika kwa Iye molimbika mtima kuti tilandire chisomo. Chisomo ichi ndi choncho nafenso tisachite tchimo m’mayesero athu. Timadza pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu m’pemphero ndipo amatimva ndi kuona zokhumba za mtima wathu. Pamenepo timalumikizana ndi mphamvu zakumwamba ndipo mphamvuzo zimaperekedwa kwa ife kuti tithe kugonjetsa uchimo wonse.