Mawu a mtanda

Mawu a mtanda ndi chiphunzitso cha Chipangano Chatsopano chimene chimalalikira za kupulumutsidwa ku uchimo ponyamula mtanda wako ndi kumutsata Yesu tsiku ndi tsiku, polandira chikhululuko kudzera mu imfa ya Yesu pa mtanda ku Cavare. Mtanda umene tikuyenela kunyamula si mtanda ngati wa pa Cavare, koma ndinjira yodzikaniza zikhumbitso zako za uchimo mu thupi lako ndi "kuupachika" ndi kuugonjetsa komanso kuupanga kukhala opanda mphanvu yotilamulira ife.(1 Akorinto 1:18; Luka 9:23)