Kupachikidwa ndi Khristu

Yesu anapachikidwa mwakuthupi pamtanda pa Kalvare. Ngakhale kuti anali wopanda chilema, anadzitengera chilango cha uchimo, chomwe chinali imfa, kotero kuti anakhoza kulipira mangawa athu ndi kutikhululukira machimo athu ngati tilola kukhulupirira mwa Iye ndi kumutsata Iye.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndinapachikidwa pamodzi ndi Kristu…” (Agalatiya 2:20) Kupachikidwa mophiphiritsa. Sitinapachikidwa tokha, koma timawerengera uchimo wathu kukhala wopachikidwa. M’mawu ena, ndi lakufa, choncho silingathe kulamulira zochita zathu. Munthu amene amakhala moyo wopachikidwa ndi amene amagonjetsa uchimo podziwerengera okha kuti apachikidwa pamodzi ndi Khristu.