Kubadwanso mwatsopano ndi chochitika chimene chimachitika m’moyo wa Mkristu wowona aliyense panthaŵi ina. “Mumasiya” kakhalidwe kanu kakale ndi kaganizidwe kanu, kukhala motsatira chilakolako cha uchimo m’thupi lanu. Inu mwabadwa mwatsopano mu moyo ndi Khristu; inu mumakhala cholengedwa chatsopano chomwe chiri Chauzimu ndi Chamuyaya. “Chotero ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; Zakale zapita; tawonani, zakhala zatsopano. 2 Akorinto 5:17 . Mukabadwa mwatsopano mumaona ufumu wa Mulungu ngati cholinga chanu ndipo zonse kunja kwa izo zimakhala zinyalala kwa inu. Werengani za kubadwanso kwauzimu kwa Paulo pa Afilipi 3:4-10.